2 Sam. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Davide mfumu ya ku Yuda.

1Pambuyo pake, Davide adafunsa Chauta kuti, “Kodi ndipite kukakhazikika ku mzinda wina uliwonse wa ku Yuda?” Chauta adamuuza kuti, “Inde, pita.” Apo Davide adafunsa kuti, “Tsono ndipite kuti?” Chauta adati, “Pita ku Hebroni.”

21Sam. 25.42, 43 Motero Davide adapita kumeneko pamodzi ndi akazi ake aŵiri aja, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimele.

3Ndipo Davide adabwera ndi anthu ake aja amene anali nawo, aliyense ndi banja lake. Adakhala m'midzi ya ku Hebroni.

41Sam. 31.11-13 Tsono anthu a ku Yuda adafika, ndipo kumeneko adadzoza Davide kuti akhale mfumu yao.

Davide atamva kuti ndi anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene adaika Saulo m'manda,

5adatuma amithenga kwa anthuwo kukaŵauza kuti, “Chauta akudalitseni, poti mudaonetsa kukhulupirika kwanu pomuika Saulo mbuyanu.

6Tsopano Chauta akuwonetseni chikondi chake chosasinthika, ndiponso kukhulupirika kwake kwa inu. Ndipotu inenso ndidzakuchitirani zabwino chifukwa cha zimene mwachitazi.

7Nchifukwa chake tsono mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna. Paja mbuyanu Saulo adamwalira, ndipo anthu a mtundu wa Yuda andidzoza ine kuti ndikhale mfumu yao.”

Isiboseti amdzoza mfumu ya ku Israele.

8Abinere mwana wa Nere, amene ankalamula ankhondo a Saulo, anali atatenga Isiboseti mwana wa Saulo, kupita naye kutsidya, ku Mahanaimu.

9Tsono adamlonga ufumu kuti akhale mfumu ya Giliyadi, Asere, Yezireele, Efuremu ndi Benjamini, kungoti Israele yense.

10Isiboseti, mwana wa Saulo, anali wa zaka 40 pamene adayamba kulamulira Israele, ndipo ufumu wake udakhala zaka ziŵiri. Koma fuko la Yuda lidatsata Davide.

11Ndipo Davide adakhala mfumu ya fuko la Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziŵiri ndi theka.

Nkhondo pakati pa Israele ndi Yuda.

12Tsono Abinere mwana wa Nere pamodzi ndi ankhondo a Isiboseti mwana wa Saulo adapita ku Gibiyoni kuchokera ku Mahanaimu.

13Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide adapita kukakumana nawo ku dziŵe la Gibiyoni. Adakhala pansi, ena tsidya lina la dziŵelo, enanso tsidya lina.

14Abinere adauza Yowabu kuti, “Anyamata anu ndi athu abwere, amenyane tiwone.” Yowabu adati, “Chabwino, namenyane.”

15Anyamatawo adabweradi naŵaŵerenga. A fuko la Benjamini, anyamata a Isiboseti, mwana wa Saulo, analipo khumi ndi aŵiri, anyamata a Davide analinso khumi ndi aŵiri.

16Tsono aliyense adagwira mutu wa mnzake nabaya mnzakeyo m'nthitimu ndi lupanga. Choncho onse 24 adafera limodzi. Nchifukwa chake malo amenewo adaŵatchula kuti Helikati-Hazurimu, ndipo ali ku Gibiyoni.

17Tsono panali nkhondo yoopsa tsiku limenelo. Abinere pamodzi ndi anthu a ku Israele adagonjetsedwa ndi ankhondo a Davide.

18Yowabu, Abisai ndi Asahele, ana atatu aja a Zeruya, anali komweko. Asahele anali waliŵiro ngati insa.

19Iyeyo adathamangitsa Abinere. Pothamangapo sankayang'ana uku ndi uku, maso anali pa Abinere basi.

20Tsono Abinere adacheuka nati, “Kodi ndiwe, Asahele?” Iye adayankha kuti, “Ndine amene.”

21Abinere adamuuza kuti, “Patukira mbali ina iliyonse, ukagwire mmodzi mwa ankhondowo, umlande zake.” Koma Asahele sadafune kuti aleke kuthamangitsa Abinere.

22Tsono Abinere adauzanso Asahele kuti, “Iwe leke, usandithamangitse, bwanji ukundikakamiza kuti ndikuphe? Nanga ndikakupha, mbale wako Yowabu ndikaonana naye bwanji?”

23Koma Asahele sadafune kumleka. Choncho Abinere adabaya Asaheleyo m'mimba ndi luti la mkondo wake, mkondowo nkutulukira kumsana. Asahele adagwa pansi, kufa nkukhala komweko. Anthu onse amene adafika pamalo pomwe padafera Asahele, adangoima kungoti kakasi.

24Koma Yowabu ndi Abisai adayamba kuthamangitsa Abinere. Ndipo pamene dzuŵa linkaloŵa, adakafika ku phiri la Ama limene lili cha kuno kwa Giya, pa njira yopita ku chipululu cha Gibiyoni.

25Abenjamini adasonkhana pamodzi kuthandiza Abinere, ndipo adapanga gulu limodzi lankhondo, nakaima pamwamba pa phiri.

26Tsono Abinere adafuulira Yowabu namufunsa kuti, “Kodi tipitirirebe kumenyana mpakampaka? Monga sukudziŵa kuti mathero ake adzakhala oŵaŵa? Kodi udzaŵaletsa liti anthu ako kutithamangitsa ife abale ao?”

27Yowabu adayankha kuti, “Ndithudi, ndikulumbira, pali Mulungu wamoyo, ukadapanda kulankhula, ankhondo angaŵa sakadaleka kuŵathamangitsa abale aowo mpaka maŵa m'maŵa.”

28Choncho Yowabu adaliza lipenga, ndipo anthu onse adaleka, osathamangitsanso Aisraele, ndipo sadamenyane nawonso.

29Choncho Abinere ndi anthu ake adayenda usiku wonse, nabzola chidikha cha Araba. Adaoloka mtsinje wa Yordani, ndipo adayenda m'maŵa monse, nakafika ku Mahanaimu.

30Yowabu adabwerako kumene adaakathamangitsa Abinere kuja. Atasonkhanitsa anthu onse pamodzi, kudapezeka kuti padasoŵa ankhondo a Davide okwanira 19, pamodzi ndi Asahele.

31Koma ankhondo a Davidewo anali atapha anthu 360 a Abinere, a fuko la Benjamini.

32Tsono adatenga mtembo wa Asahele, nakauika m'manda a bambo wake, amene anali ku Betelehemu. Yowabu ndi anthu ake adayenda usiku wonse, ndipo kudaŵachera ali ku Hebroni.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help