1Inu Mulungu, ife tidamva ndi makutu athu,
makolo athu adatiwuza za ntchito
zimene mudagwira pa masiku ao,
masiku amakedzana.
2Inu mudapirikitsa mitundu ina ya anthu,
koma makolo athu mudaŵakhazika m'dziko lao.
Inu mudasautsa mitundu ina ya anthu,
koma makolo athuwo Inu mudaŵapatsa ufulu.
3Iwo sadalande dziko ndi lupanga lao,
sadapambane pa nkhondo ndi mphamvu zao.
Koma adagonjetsa ndi mphamvu zanu,
chifukwa cha kuŵala kwa nkhope yanu,
pakuti mudakondwera nawodi.
4Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,
amene mudampambanitsa Yakobe pa nkhondo.
5Ndi thandizo lanu tidakantha adani athu.
Ndi mphamvu zanu tidapondereza ogalukira.
6Sindidalira uta wanga,
ngakhale lupanga langa silingandipulumutse.
7Koma Inu mwandilanditsa kwa adani athu,
mwaŵachititsa manyazi amene amadana nafe.
8Takhala tikunyadira mphamvu za Mulungu nthaŵi zonse,
ndipo tidzakuthokozani mpaka muyaya.
9Komabe Inu mwatitaya, ndipo mwatitsitsa,
simunapite nawo limodzi ankhondo athu.
10Mwalola kuti amaliwongo athu atipirikitse,
ndipo adani athu apeza zofunkha kwathu.
11Inu mwatisandutsa nkhosa zokaphedwa,
mwatibalalitsa pakati pa mitundu ina ya anthu.
12Inu mwagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika,
ndipo simudapindulepo kanthu ai.
13Inu mwatisandutsa anthu onyozeka
kwa anzathu oyandikana nafe,
anthu otizungulira amatiseka ndi kutinyodola.
14Inu mwatisandutsa anthu oŵanyodola
pakati pa anthu a mitundu ina,
anthu omangosekedwa pakati pa anzathu.
15Tsiku lonse ndimangodziwona
kuti ndine munthu wopandapake.
Nkhope yanga yagwa chifukwa cha manyazi,
16pakumva mau a anthu onditonza ndi onditukwana,
poona mdani wanga ndi munthu wolipsira.
17Zonsezi zatigwera,
ngakhale kuti sitidakuiŵaleni
ndipo sitidaphwanye chipangano chanu.
18Mtima wathu sudabwerere m'mbuyo,
mapazi athu sadaleke kuyenda m'njira yanu.
19Komabe Inuyo mwatitswanya
ndi kutisiya pakati pa nkhandwe ku chipululu,
kumene kuli mdima wandiweyani.
20Tikadaiŵala Mulungu wathu,
kapena kugwadira mulungu wachilendo,
21kodi Mulungu sakadazipeza zimenezi?
Paja Iye amadziŵa zinsinsi zonse zamumtima.
22 Aro. 8.36 Koma chifukwa cha Inu, adani akutipha tsiku lonse,
pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.
23Dzukani, Inu Ambuye.
Chifukwa chiyani mukukhala ngati mwagona?
Khalani maso, musatitaye kotheratu.
24Chifukwa chiyani mwatifulatira?
Mwaiŵaliranji masautso athu ndi kupsinjidwa kwathu?
25Ife tagwa pansi m'fumbi,
thupi lathu langoti thapsa pa dothi.
26Dzukani, mubwere kudzatithandiza.
Tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.