1Pambuyo pake Bezalele adapanga bokosi lachipangano ndi matabwa a mtengo wa kasiya. Kutalika kwake kunali masentimita 114, muufupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69.
2Tsono lonselo adalikuta ndi golide m'kati mwake ndi kunja komwe, ndipo adalemba mkombero wagolide kuzungulira bokosi lonselo.
3Adapanga mphete zinai zagolide zonyamulira, nazimangirira ku ngodya zinai za bokosilo, uku ziŵiri uku ziŵiri.
4Adapanga mphiko zinai za matabwa a mtengo wa kasiya, nazikuta ndi golide,
5ndipo mphikozo adazipisa m'mphete zija pa mbali zonse ziŵiri za bokosilo, kuti azinyamulira.
6Kenaka adapanga chivundikiro cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, muufupi wake masentimita 69.
7Pa nsonga zake ziŵiri za chivundikirocho, adazokotapo akerubi aŵiri a golide wosula ndi nyundo,
8wina uku wina uku. Adaŵapangira kumodzi ndi chivundikirocho.
9Mapiko a akerubiwo adaŵatambalitsa pamwamba, kuphimba chivundikiro chija. Adakhala choyang'anana, ndipo aliyense anali kuyang'anananso ndi chivundikirocho.
Za mapangidwe a tebulo(Eks. 25.23-30)10Bezalele adapanganso tebulo la matabwa a mtengo wa kasiya, m'litali mwake masentimita 91, muufupi mwake masentimita 46, ndipo mumsinkhu mwake masentimita 69,
11Tsono adalikuta ndi golide wabwino kwambiri, nalemba mkombelo wagolide kuzungulira tebulo lonselo.
12Adapanga fulemu lagolide pozungulira, muufupi mwake munali ngati kuyesa chikhatho, nalemba mkombero wagolide molizungulira.
13Kenaka adapanganso mphete zinai zagolide za tebulolo, naziika pa ngodya zinai ku miyendo ya tebulolo.
14Mphete zopisiramo mphiko ponyamula tebulolo, zinali pafupi ndi fulemu lija.
15Adapanga mphiko za matabwa a mtengo wa kasiya, nazikuta ndi golide.
16Adapanganso ziŵiya za golide wabwino kwambiri za pa tebulolo, monga mbale, zikho, mitsuko ndi mabeseni ogwiritsira ntchito pa zopereka zamadzi.
Apanga choikaponyale(Eks. 25.31-40)17Pambuyo pake adapanga choikaponyale cha golide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi thunthu lake zinali zagolide, ndipo zonse zinali zosula ndi nyundo. Zikho zake, ndiye kuti nkhunje ndi maluŵa ake, adazipangira kumodzi ndi choikaponyalecho.
18Pa mbali zake adapanga nthambi zisanu ndi imodzi, zitatu pa mbali iliyonse.
19Iliyonse mwa nthambizo inali ndi maluŵa atatu, opangidwa ngati maluŵa amtowo, okhala ndi nkhunje ndi maluŵa ake.
20Pa thunthu lake la choikaponyalecho panali zikho zinai zonga maluŵa amtowo okhala ndi nkhunje zake ndi maluŵa ake.
21Panali nkhunje imodzi pansi pa magulu atatu a nthambi zija, zitapatulidwa ziŵiriziŵiri.
22Nkhunjezo, pamodzi ndi nthambizo, zidapangidwira kumodzi ndi choikaponyale chija. Chonsecho chinali chinthu chimodzi chagolide, chosula ndi nyundo.
23Ndipo adapanga nyale zisanu ndi ziŵiri za pa choikaponyalecho, napanganso mbanira ndiponso zoolera phulusa za golide wabwino kwambiri.
24Popanga choikaponyalecho, pamodzi ndi zipangizo zake zonsezo, adagwiritsa ntchito makilogaramu 34 a golide wabwino kwambiri.
Apanga guwa lofukizirapo lubani(Eks. 30.1-5)25Guwa lofukizirapo lubani adalipanga ndi matabwa a mtengo wa kasiya. Linali lalibanda, muutalika mwake munali masentimita 46, muufupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 91, ndipo nyanga zake zidapangidwira kumodzi ndi guwalo.
26Adakuta guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri pamwamba pake, pa mbali zake ndi pa nyanga zake zomwe. Kuzungulira guwa lonselo, adalemba mkombero wagolide.
27Adapanga mphete ziŵiri zagolide zonyamulira guwalo, ndipo adazilumikiza ku mbali zonse ziŵiri za guwa, pansi pa mkombero uja, kuti apisemo mphiko zonyamulira.
28Mphikozo adazipanga ndi matabwa a mtengo wa kasiya, naikuta ndi golide.
Apanga mafuta odzozera ndiponso lubani(Eks. 30.22-38)29 Eks. 30.22-38 Adapanganso mafuta oyera odzozera, ndiponso zofukizira za fungo lokoma. Mapangidwe ake adachita monga momwe ankachitira mmisiri wopanga zonunkhira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.