Miy. 23 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ukakhala pansi kuti udye ndi mfumu,

uyang'ane bwino zimene zili pamaso pako.

2Ngati ndiwe munthu wadyera,

udziletse kuti usachite khwinthi.

3Usasirire zakudya zake zokoma,

poti zimenezi ndi zakudya zonyenga.

4Usadzitopetse nkufuna chuma,

udziŵe kuchita zinthu mwanzeru ndi kudziletsa.

5Ukangopeza chuma, uwona chapita kale,

pakuti chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi,

nkuyamba kuuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.

6Usadye chakudya kwa munthu waunkhambo,

usamalakalaka zakudya zake zokoma.

7Paja iye amangokhalira kuganiza za mtengo wa zinthu.

Amakuuza kuti, “Kazidya, kazimwa!”

Koma mumtima mwake zimenezo sakuzifuna.

8Udzasanza nthongo wadyazo,

ndipo mau ako oshashalika adzapita pachabe.

9Usamalankhula pali munthu wopusa,

pakuti adzanyoza mau ako anzeru.

10Usasendeza malire akalekale,

kapena kukaloŵerera minda ya ana amasiye.

11Paja Momboli wao ndi wamphamvu,

adzaŵateteza pa mlandu wao kuti akutsutse iweyo.

12Mtima wako ukhale pa malangizo,

ndipo makutu ako azimvetsera mau anzeru.

13Usamaleka kumpatsa mwambo mwana,

ukamkwapula ndi tsatsa sadzafa.

14Ngati umkwapula ndi tsatsa,

udzapulumutsa moyo wake ku imfa.

15Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru,

nanenso mtima wanga udzasangalala.

16Mtima wanga udzakondwa

ndikadzakumva ukulankhula zolungama.

17Mtima wako usamachita nsanje ndi anthu ochimwa,

koma upitirire kumaopa Chauta tsiku ndi tsiku.

18Ndithu, zakutsogolo zilipo,

ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe.

19Mwana wanga, tamvera, ndipo ukhale wanzeru,

mtima wako uuyendetse m'njira yabwino.

20Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera,

kapena pakati pa anthu odya nyama mwadyera.

21Paja chidakwa ndi munthu wadyera adzasanduka amphaŵi,

ndipo munthu waulesi adzasanduka mvalansanza.

22Umvere atate ako amene adakubala,

ndipo usamanyoza amai ako atakalamba.

23Ugule choona, ndipo usachigulitse.

Ugulenso nzeru, mwambo ndiponso mtima womvetsa zinthu.

24Bambo wa mwana waulemu adzakondwa kwambiri.

Wobala mwana wanzeru adzasangalala naye.

25Atate ako ndi amai ako asangalale,

mai amene adakubala iwe akondwe.

26Mwana wanga, mtima wako ukhulupirire ine,

maso ako apenyetsetse njira zanga.

27Mkazi wadama ali ngati dzenje lakuya,

mkazi wachiwerewere ali ngati chitsime chophaphatiza.

28Amabisalira ngati mbala yachifwamba,

ndipo chifukwa cha iyeyo amuna ambiri

amasanduka osakhulupirika.

29Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni?

Ndani ali pa mkangano? Ndani akudandaula?

Ndani ali ndi zilonda zosadziŵika magwero ake?

Ndani ali wofiira maso?

30Ndi amene amakhalitsa pamene pali vinyo,

amene amamwa nawo vinyo wosanganiza ndi zina.

31Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo,

pamene akututuma m'chikho namakoma poloŵa ku m'mero.

32Potsiriza pake amaluma ngati njoka,

ndipo amanjenjedula ngati mphiri.

33Maso ako adzaona zinthu zachilendo,

maganizo ndi mau ako adzakhala okhotakhota.

34Udzakhala ngati munthu amene ali gone

pakati pa nyanja,

kapena ngati munthu wogona pa nsonga

ya mlongoti wa ngalaŵa.

35Iwe udzati, “Adanditchaya, koma sadandipweteke.

Adandimenya, koma ine osamvako.

Kodi ine ndidzatsitsimuka liti?

Ndiye ndithamangira chakumwa china.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help