1 Ako. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kuuka kwa Khristu

1Abale, ndifuna kukukumbutsani Uthenga Wabwino umene ndidakulalikirani. Mudaulandira, ndipo mudakhazikitsapo chikhulupiriro chanu molimba.

2Mulungu adzakupulumutsani ndi Uthenga Wabwinowu, ngati musunga bwino mau ake monga ndidakulalikirani. Popanda kutero, bwenzi mutangokhulupirira pachabe.

3 chabe.

9 Ntc. 8.3 Inetu ndine wamng'onong'onodi mwa atumwi onse. Sindine woyenera konse kuti ndizitchedwa mtumwi, pakuti ndinkazunza Mpingo wa Mulungu.

10Koma chifukwa chakuti Mulungu adandikomera mtima, ndili monga ndilirimu. Ndipo kukoma mtima kwakeko sikunali kopanda phindu, popeza kuti ndidagwira ntchito koposa atumwi ena onse. Komabe si ndine ndidaigwira, koma mphamvu za Mulungu zimene zikundilimbikitsa.

11Motero kaya ndi ineyo kaya ndi iwowo, zimene timalalika ndi zomwezo, zimene mudakhulupirira ndi zomwezonso.

Za kuuka kwa anthu akufa

12Tsono popeza kuti chimene timalalika ndi chakuti Khristu adauka kwa akufa, bwanji ena mwa inu akunena kuti, “Anthu akufa sadzaukanso?”

13Ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristunso sadauke.

14Tsono ngati Khristu sadauke, kulalika kwathu nkwachabe, ndipo chikhulupiriro chanu nchachabenso.

15Ngati zili choncho, ndiye kuti ndife mboni zonama, tikuchita umboni wonama m'dzina la Mulungu, ponena kuti Mulungu adaukitsa Khristu. Ngati nzoonadi kuti akufa sauka, ndiye kuti Mulungu sadamuukitse Khristuyo.

16Pakuti ngati akufa sauka, Khristunso sadauke.

17Ndipotu ngati Khristu sadauke, chikhulupiriro chanu nchopanda pake, ndipo mukadali m'machimo anu.

18Pamenepo nawonso amene adamwalira ali okhulupirira Khristu, adatayika ndithu.

19Ngati taika chikhulupiriro chathu mwa Khristu chifukwa cha moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni koposa anthu ena onse.

20Koma ai, Khristu adauka ndithu kwa akufa. Pakati pa onse amene adafa, ndiye woyamba kuuka.

21Pakuti monga imfa idadza pansi pano kudzera mwa munthu wina, momwemonso kuuka kwa akufa kudadza kudzera mwa munthu wina.

22Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa cholumikizana ndi Khristu.

23Koma aliyense adzauka pa nthaŵi yake: woyambirira ndi Khristu, ndipo pambuyo pake, pamene Khristuyo adzabwera, nawonso amene ali ake adzauka.

24Pamenepo chimalizo chidzafika. Khristu atathetsa ufumu wonse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse, adzapereka ufumu uja kwa Mulungu Atate.

25Mas. 110.1 Paja Khristu ayenera kulamulira mpaka atagonjetsa adani ake onse.

26Mdani wotsiriza kumthetsa mphamvu, ndiye imfa.

27Mas. 8.6 Malembotu akuti, “Mulungu adamgonjetsera zinthu zonse.” Koma nchodziŵikiratu kuti pamene akuti “zinthu zonse,” sakuphatikizapo ndi Mulungu yemwe, amene adagonjetsera Khristu zinthu zonse.

28Koma pamene zonse zidzakhala zitagonjera Khristu, pamenepo Mwana wa Mulungu nayenso adzagonjera Mulungu, amene adamgonjetsera zinthu zonse. Adzachita zimenezi kuti Mulungu akhale wolamulira aliyense kwathunthu.

29 2Am. 12.44 Ngati Yesu sadauke kwa akufa, nanga amafunanji anthu amene amabatizidwa m'malo mwa amene adafa? Ngati akufa sauka konse, nanga chifukwa chiyani anthu amabatizidwa m'malo mwao?

30Nanga pamenepo ifenso timakhaliranji m'zoopsa nthaŵi zonse?

31Abale anga, imfa ndimayenda nayo tsiku ndi tsiku. Ndikunenetsa zimenezi chifukwa ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

32Yes. 22.13Nanga pamene ndidalimbana ndi zilombo ku Efeso, ndidapindulapo chiyani, ngati ndinkatsata maganizo a anthu chabe? Ndiyetu ngati akufa sauka, tizingochita monga amanenera kuti, “Tiyeni tizidya ndi kumwa, pakuti maŵa tikufa.”

33Musadzinyenge. “Paja kuyanjana ndi anthu ochimwa kumaononga khalidwe.”

34Mudzidzimuke mumtima mwanu, ndipo muleke kuchimwa. Ena mwa inu sadziŵa Mulungu konse. Ndikukuuzani zimenezi kuti muchite manyazi.

Za thupi limene munthu adzauka nalo

35Koma kapena wina nkufunsa kuti, “Kodi akufa adzauka bwanji? Kodi adzakhala ndi thupi lotani?”

36Ati kupusa ati! Mbeu imene umafesa, siingamere ndi kukhala moyo itapanda kufa.

37Ndipo chimene ufesa, si mmera umene udzatuluka ai, koma ndi njere chabe, kaya ndi ya tirigu, kapena ya mtundu wina uliwonse.

38Koma Mulungu amaisandutsa mmera monga momwe Iye akufunira, mbeu iliyonse mmera wakutiwakuti.

39Mnofu sukhala wa mtundu umodzi. Pali mnofu wina wa anthu, wina wa nyama, wina wa mbalame, ndi wina wa nsomba.

40Palinso zolengedwa zakuthambo, ndi zina zapansipano. Koma ulemerero wa zakuthambo ndi wosiyana ndi ulemerero wa zapansipano.

41Dzuŵa lili ndi kuŵala kwake, mwezi uli ndi kuŵala kwake kosiyana ndi kwa dzuŵa kuja, nyenyezinso zili ndi kuŵala kwake kosiyana ndi kwa zina zija. Ngakhale nyenyezizo zimasiyananso kuŵala kwake.

42Zidzateronso pamene akufa adzauka. Thupi loikidwa m'nthaka ngati mbeu yofesa, limaola, koma likadzauka, lidzakhala losaola.

43Thupi loikidwa m'manda, ndi lonyozeka ndi lofooka, koma likadzauka lidzakhala lokongola ndi lamphamvu.

44Thupi loikidwa m'manda, ndi lamnofu chabe, koma likadzauka, lidzakhala lauzimu.

Ngati pali thupi lamnofu, palinso thupi lauzimu.

45Gen. 2.7 Paja Malembo akuti, “Munthu woyamba uja, Adamu, adachita kusanduka chinthu chamnofu chokhala ndi moyo.” Koma Adamu wotsiriza adakhala chinthu chauzimu chopatsa moyo.

46Loyamba si thupi lauzimu ai. Loyamba ndi lamnofu, pambuyo pake lauzimu.

47Adamu woyamba uja anali wochokera ku dothi, anali wapansipano. Koma Khristu, Adamu wachiŵiri uja, anali wochokera Kumwamba.

48Anthu onse apansipano ali ngati Adamu wopangidwa ndi dothi uja. Ndipo onse amene ali a Kumwamba, ali ngati Khristu wa Kumwamba.

49Monga takhala ofanafana ndi Adamu, munthu wopangidwa ndi dothi uja, momwemonso tidzakhala ofanafana ndi Khristu, munthu wa Kumwamba.

50Abale, chimene ndikunena nchakuti munthu ndi thupi lake lamnofuli sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimaola, sizingathe kuloŵa kumene zinthu siziwola.

51 2Es. 6.23; 1Ate. 4.15-17 Mvetsetsani, ndikuuzeni chinsinsi. Sikuti tonse tidzamwalira, komabe tonse tidzasandulika.

52Zidzachitika mwadzidzidzi, pa kamphindi ngati kuphethira kwa diso, pamene lipenga lotsiriza lidzalira. Likadzaliratu lipengalo, akufa adzauka ndi matupi amene sangaole, ndipo ife tidzasandulika.

53Pakuti thupi lotha kuwolali liyenera kusanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali liyenera kusanduka losatha kufa.

54Yes. 25.8Tsono thupi lotha kuwolali likadzasanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzachitikadi zimene Malembo adanena kuti,

“Imfa yagonjetsedwa kwathunthu.”

55 Hos. 13.14 “Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti?

Iwe imfa, ululu wako uli kuti?”

56Ululu wake wa imfa ndi uchimo, ndipo chimene chimapatsa uchimo mphamvu, ndi Malamulo.

57Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

58Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help