Yes. 51 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mau otonthoza Ziyoni

1Chauta akunena kuti:

“Tcherani khutu inu amene mufuna kupulumuka,

inu amene mufuna kuti ndikuthandizeni.

Taganizani za thanthwe kumene mudasemedwa,

ku nkhuti ya miyala kumene adakukumbani.

2Taganizani za Abrahamu, bambo

wanu ndi Sara amene adakubalani.

Pamene ndinkamuitana Abrahamu, adaalibe mwana.

Koma ndidamudalitsa, ndidampatsa ana,

ndipo ndidachulukitsa zidzukulu zake.

3Ndidzatonthoza mtima Ziyoni,

ndidzaŵatonthoza mtima okhala ku mabwinja ake.

Ngakhale dziko lake ndi chipululu,

ndidzalisandutsa ngati Edeni.

Ngakhale dziko lake ndi thengo,

ndidzalisandutsa ngati munda wa Chauta.

Kumeneko anthu adzakondwa ndi kusangalala,

adzaimba nyimbo zondilemekeza ndi zondithokoza.

4“Mverani, inu anthu anga,

tcherani khutu, inu mtundu wanga.

Malamulo adzachokera kwa Ine,

ndipo chilungamo changa chidzaunikira anthu onse.

5Ndidzabwera mofulumira kudzaombola anthu anga,

nthaŵi yanga ya kuŵapulumutsa ili pafupi.

Ine mwiniwakene ndidzalamulira mitundu ya anthu onse.

Maiko akutali akundidikira kuti ndibwere,

akundiyembekeza ndi chikhulupiriro

kuti ndidzaŵapulumutse.

6Yang'anani mlengalenga,

yang'anani dziko lapansi.

Mlengalenga udzazimirira ngati utsi,

dziko lapansi lidzatha ngati chovala,

ndipo anthu ake onse adzafa ngati ntchentche.

Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya,

ndipo kuwombola kwanga kudzakhala kwa nthaŵi zonse.

7“Mverani, inu amene mukudziŵa chilungamo,

inu amene mukusunga malamulo anga mumtima mwanu.

Musachite mantha anthu akamakudzudzulani,

musataye mtima akamakulalatirani.

8Anthu otereŵa adzatha

ngati nsalu yodyewa ndi njenjete,

adzatha ngati thonje lodyewa ndi mbozi.

Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya,

kuwombola kwanga kudzakhala kwa nthaŵi zonse.”

9Dzambatukani, Inu Chauta,

dzambatukani! Valani dzilimbe.

Dzambatukani monga momwe munkachitira masiku amakedzana,

nthaŵi ya mibadwo yakale.

Kodi sindinu uja mudaduladula Rahabu,

chilombo cham'nyanja chija,

ndi kubaya chinjoka cham'nyanja chija?

10Kodi sindinu amene mudaumitsa nyanja yaikulu ija,

madzi ozama kwambiri?

Kodi sindinu amene mudapanga njira pa madzi,

kuti amene mudaŵapulumutsa aoloke pouma.

11Amene mudaŵaombola adzabwerera,

ndipo adzafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa.

Chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pankhope pao.

Adzakhala ndi chikondwerero ndi chisangalalo.

Chisoni ndi kubuula zidzatha.

12Chauta akunena kuti,

“Ineineyo ndine amene ndimakutonthozani mtima.

Kodi ndinu yani kuti muziwopa munthu woti adzafa,

mwanawamunthu amene angokhala nthaŵi yochepa ngati udzu?

13Kodi ndinu yani kuti muziiŵala Chauta,

Mlengi wanu, amene adayalika zakuthambo,

ndi kuika maziko a dziko lapansi?

Kodi ndinu yani kuti nthaŵi zonse

muziwopa ukali wa anthu okuzunzani,

amene angofuna kukuwonongani?

Ukali wa anthu okuzunzaniwo

tsopano uli kuti?

14Am'ndende adzaŵamasula posachedwa.

Sadzafa, sadzaloŵa m'manda,

ndipo chakudya sichidzaŵasoŵa konse.

15Ine ndine Chauta, Mulungu wanu,

amene ndimavundula nyanja,

kotero kuti mafunde ake amakokoma.

Dzina langa ndine Chauta Wamphamvuzonse.

16Ndidaika mau anga m'kamwa mwanu,

ndipo ndidakutetezani ndi dzanja langa.

Ndidayalika zakuthambo,

ndi kukhazika maziko a dziko lapansi.

Ndidauza anthu a ku Ziyoni kuti,

‘Ndinu anthu anga.’ ”

Kutha kwa mavuto a Yerusalemu

17 Chiv. 14.10; 16.19 Dzuka, dzuka, imirira, iwe Yerusalemu.

Wamwa chikho chachilango

chimene Chauta adakupatsa ali wokwiya.

Chikhocho nchochititsa chizwezwe,

ndipo iwe udachigugudiza.

18Palibe wina wokutsogolera

mwa ana amene udaŵabala.

Palibe ndi mmodzi yemwe wokugwira pa dzanja

mwa ana amene udaŵalera.

19Mavuto akugwera paŵiri:

dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka,

ndipo anthu ako apululuka ndi njala ndi nkhondo.

Ndani angakumvere chifundo?

Ndani angakutonthoze mtima?

20Ana ako akomoka,

ali ngundangunda pa miseu yonse

ngati mphoyo zokodwa mu ukonde.

Kwaŵagwera kukwiya kwa Chauta

ndi kudzudzula kwake.

21Nchifukwa chake imva iwe amene ukuvutika,

iwe amene waledzera, koma osati ndi vinyo.

22Chauta, Ambuye ako, Mulungu wako,

amene amakutchinjiriza, akunena kuti,

“Ona, ndakulanda chikho chochititsa chizwezwe chija.

Chikhocho, chimene ndidakupatsani ndili wokwiya,

sudzachimwanso.

23Chikhocho ndidzachipereka kwa okuzunza,

amene adaakuuza kuti,

‘Gona pansi, tikuyende pamsana.’

Msana wako adauyesa pansi popondapo,

adauyesa mseu woti ayendepo.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help