1Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
2Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
3Muziganiza za Iye amene adapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafookere ndi kutaya mtima.
4Polimbana ndi uchimo, simudafike mpaka pokhetsa magazi.
Mulungu amalanga ana ake5 Yob. 5.17; Miy. 3.11, 12 Mwaiŵala kodi mau olimbitsa mtima aja, amene Mulungu amakulankhulani ngati ana ake? Mauwo ndi aŵa:
“Mwana wanga, usanyozere malango a Ambuye,
kapena kutaya mtima pamene Iwo akudzudzula.
6Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda,
amakwapula mwana aliyense amene Iwo amamlandira.”
7Muzipirira masautso kuti muphunzirepo makhalidwe oyenera. Mulungu amakutengani ngati ana ake m'zochita zake zonse. Kodi nkale lonse analipo mwana amene bambo wake sadamlange?
8Ngati Mulungu sakulangani inuyo, monga amachitira ndi ana ake onse, ndiye kuti sindinu ana enieni, koma am'chigololo.
9Tinali nawo azibambo athu apansipano amene ankatilanga, ndipo tinkaŵalemekeza. Kwenikweni tsono tikadayenera kugonjera Mulungu, Atate a mizimu, kuti tikhale ndi moyo.
10Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake.
11Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.
12 Yes. 35.3 Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka.
13Miy. 4.26Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe.
Malangizo ndi machenjezo14Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
15Deut. 29.18Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.
16Gen. 25.29-34 Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha.
17Gen. 27.30-40 Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi.
18 Eks. 19.16-22; 20.18-21; Deut. 4.11, 12; 5.22-27 Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho;
19limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse,
20Eks. 19.12, 13 pakuti lidaaŵaopsa lamulo lija lakuti, “Ndi nyama yomwe ikangokhudza phirilo, iphedwe ndi miyala.”
21Deut. 9.19 Maonekedwe a zonsezo anali oopsa kwambiri, kotero kuti Mose yemwe adaati, “Ndikunjenjemera ndi mantha.”
22Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ndiponso ku mzinda wa Mulungu wamoyo, ndiye kuti Yerusalemu wa Kumwamba, m'mene muli angelo osaŵerengeka.
23Mwafika kuchikondwerero kumene kwasonkhana ana oyamba a Mulungu, amene maina ao adalembedwa Kumwamba. Mwafika kwa Mulungu, mweruzi wa anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama, amene Mulungu waŵasandutsa angwiro kwenikweni.
24Gen. 4.10 Mwafika kwa Yesu, Nkhoswe yokonza za chipangano chatsopano, ndiponso mwafika ku magazi okhetsedwa, amene akutilonjeza zinthu zabwino koposa m'mene magazi a Abele ankachitira.
25 Eks. 20.22 Chenjerani tsono kuti musakane kumvera amene akulankhula nanu. Anthu amene adakana kumvera iye uja amene adaaŵachenjeza pansi pano, sadapulumuke ku chilango ai. Nanji tsono ifeyo, tidzapulumuka bwanji ngati timufulatira wotilankhula kuchokera Kumwambaku?
26Hag. 2.6 Nthaŵi imeneyo mau a Mulungu adaagwedeza dziko, koma tsopano lino walonjeza ndi mau akuti, “Kamodzi kenanso ndidzagwedeza, osati dziko lokha ai, koma ndi thambo lomwe.”
27Mau akuti “Kamodzi kenanso” akuwonetsa poyera kuti zolengedwa zonse zogwedezeka zidzachotsedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zidzakhalitse.
28Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha.
29Deut. 4.24 Paja Mulungu wathu ndi moto wopsereza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.