Mphu. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Munthu woopa Ambuye adzachita zimenezi.

Akasunga bwino Malamulo, adzapeza luntha.

2Lidzamchingamira ngati mai wake.

Lidzamulandira ngati mkazi wa pa unyamata wake.

3Chakudya chimene lidzampatsa chidzakhala

kumvetsa zinthu,

chakumwa chake chidzakhala nzeru.

4Adzaliyedzamira lunthalo ndipo sadzagwa.

Adzadalira lunthalo ndipo sadzachita manyazi.

5Lidzamkweza kupambana anzake,

ndipo lidzampatsa mau oti alankhule pa msonkhano.

6Choncho adzapeza chimwemwe chachikulu ndipo adzasangalala.

Dzina lake lidzatchuka mpaka muyaya.

7Zitsiru sizidzakhala nalo lunthalo,

anthu ochimwa sadzaliwona.

8Limakhala kutali ndi anthu onyada,

anthu abodza saliganizira konse.

9Nyimbo yoyamika sikhala bwino m'kamwa mwa

munthu wochimwa,

poti sichokera kwa Ambuye.

10Mayamiko ayenera kuŵatchula mwaluntha,

ndipo ndi Ambuye amene amaŵaika m'kamwa mwa munthu.

Munthu ali ndi ufulu

11 Mphu. 17.1-12 Ukalakwa usamati, “Andilakwitsa ndi Ambuye,”

poti iwo sangachititse munthu zomwe iwo omwe akudana nazo.

12Usamanena kuti, “Andisokeretsa ndi Ambuye,”

chifukwa Iwo alibe nawo ntchito anthu ochimwa.

13Ambuye amadana ndi tchimo lililonse,

nawonso anthu oŵaopa, sangakonde tchimo.

14Ambuye ndiwo amene adalenga anthu pa chiyambi,

naŵapatsa ufulu wosankha okha chochita.

15Ngati ufuna, ungathe kutsata Malamulo.

Kukhala wokhulupirika kapena ai zili kwa iwe.

16Adakuikira moto ndi madzi pamaso pako,

tambalitsa dzanja lako,

usankhepo chimene ufuna.

17Munthu amamuwonetsa moyo ndi imfa,

ndipo amalandira chimene wasankhapo.

18Nzeru za Ambuye nzambiri kwabasi,

ali ndi mphamvu zonse, ndipo amaona zonse.

19Ambuye amayang'anira onse oŵaopa,

ndipo zonse zimene anthu amachita Iwo amazidziŵa.

20Chikhalire sadalamule munthu aliyense

kuti akhale wosasamala za Mulungu,

kapena kumlola kuti azichimwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help