1Naŵa mau a Mlaliki, mwana wa Davide,
mfumu ya ku Yerusalemu:
2Zonse nzopanda phindu, akutero Mlaliki.
Zonse nzachabechabe!
Ndithudi zonse nzopandapake.
3Kodi munthu amapindulanji
ndi ntchito zonse zolemetsa
zimene amazigwira pansi pano?
4 Mphu. 14.18 Mbadwo wina ukutha, wina ukudza,
koma dziko lapansi limakhalapobe losasinthika.
5Dzuŵa limatuluka, nkukaloŵa,
ndipo limapita mwamsanga kumene linatulukira.
6Mphepo imaombera chakumwera,
nkudzakhotera chakumpoto.
Imaomba mozungulirazungulira,
pozungulirapo nkudzabwereranso komwe yachokera.
7Mitsinje yonse imakathira ku nyanja,
koma nyanjayo osadzaza.
Kumene madzi adachokera
amabwereranso komweko.
8Zinthu zonse nzolemetsa,
kulemera kwake nkosasimbika.
Maso sakhuta nkupenya,
makutunso sakhuta nkumva.
9Zomwe zidaalipo kale
ndizo zidzakhaleponso.
Zomwe zidaachitika kale
ndizo zidzachitikenso.
Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano.
10Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti,
“Ichi ndiye nchatsopano?”
Iyai, chidaalipo kale,
ifenso kukadalibe nkomwe.
11Zakale sizikumbukika,
ngakhale zinthu zimene zidzachitike pambuyo pake
sizidzakumbukikanso
ndi amene adzabwere m'tsogolo mwake.
Nzeru nzodzetsa chisoni12Ine Mlalikine ndidakhalapo mfumu yolamulira Israele ku Yerusalemu.
13Ndidaaika mtima wanga pa kufunitsitsa kumvetsa bwino zonse zochitika pansi pano. Imeneyi ndi ntchito yolemetsa kwambiri imene Mulungu adatipatsa anthufe.
14Zonse zochitika pansi pano ndaziwona. Zonsezo nzopandapake, ndipo kuzifunafuna nkungodzivuta chabe.
15Chimene chidakhota sichingathe kuwongokanso,
chimene palibe sichingathe kuŵerengedwa.
16 1Maf. 4.29-31; Mphu. 47.14-18 Mumtima mwangamu ndinkati, “Ndatola nzeru zambiri, kupambana onse amene ankalamulira ku Yerusalemu kale. Ndaphunzira zambiri zaluntha ndi zanzeru.”
17Ndidaayesetsa kumvetsa kuti nzeru nchiyani, misala nchiyani, uchitsiru nchiyani. Koma ndidazindikira kuti kuterokonso kunali kungodzivuta chabe.
18Paja nzeru zambiri zimadzetsa chisoni chambiri,
munthu akamaonjezera nzeru,
ndiye kuti akuwonjezeranso chisoni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.