1Zitachitika zimenezi, atsogoleri ena adadza kwa ine, nati, “Aisraele, ansembe ndi Alevi sadadzipatule kwa anthu a mitundu iyi yoyandikana nafe: Akanani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aejipito ndi Aamori. Anthu athuwo akuchita nawo zonyansa zaozo.
2Aisraele ena ndi ana ao aamuna adayamba kukwatira ana aakazi a anthuwo. Motero mtundu wathu wopatulika wadzisokoneza ndi mitundu ya anthu a m'maikowo. Ndipo atsogoleri ndi akuluakulu ndiwo amene akupambana pa kusakhulupirika kumeneku.”
3Nditamva zimenezi, ndidang'amba zovala zanga ndi mwinjiro wanga chifukwa cha chisoni, ndipo ndidazula tsitsi la kumutu kwanga ndi kumwetsula ndevu zanga, nkukhala pansi ndili wotaya mtima.
4Ndidakhala pansi choncho kufikira nthaŵi yamadzulo. Tsono anthu onse amene ankaopa mau a Mulungu wa Israele, ataona kusakhulupirika kwa obwerako ku ukapolo aja, adayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana.
5Tsono itakwana nthaŵi ya nsembe yamadzulo, ndidadzidzimuka mumtima mwanga nkuimirira, zovala zanga zong'ambika zija zikali m'thupi. Ndidagwada nkukweza manja anga kwa Chauta, Mulungu wanga,
6Ndipo ndidati,
“Inu Mulungu wanga, manyazi ndi chisoni zikundikanikitsa kukweza nkhope yanga kwa Inu Mulungu wanga, chifukwa zoipa zathu zakwera kopambana mitu yathu. Ndithu uchimo wathu wakwera mpaka kukafika kumwamba.
7Kuyambira nthaŵi ya makolo athu mpaka pano, takhala tikuchimwa kwambiri. Chifukwa cha machimo athuwo, ifeyo pamodzi ndi mafumu athu ndi ansembe athu, atipereka kwa mafumu a m'maiko achikunja, kuti atiphe pa nkhondo, atitenge ku ukapolo, atilande zinthu ndiponso kuti atichititse manyazi kwambiri, monga momwe ziliri masiku anomu.
8Koma tsopano pa kanthaŵi kochepaka, Inu Chauta, Mulungu wathu, mwaonetsa kukoma mtima kwanu. Mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke ku ukapolo ndi kuloŵa m'malo anu oyera. Mwatilimbitsa mtima ndi kutitsitsimutsa kwa kanthaŵi mu ukapolo wathu.
9Inde ndife akapolo, komabe Inu Mulungu wathu simudatisiya mu ukapolo, mwatiwonetsa chikondi chanu chosasinthika pamaso pa mafumu a ku Persiya. Mwatitsitsimutsa kuti timange Nyumba yanu, Inu Mulungu wathu, pa mabwinja ake akale. Mwatitchinjiriza m'dziko la Yudeya ndiponso mu Yerusalemu.
10“Koma tsopano, Inu Mulungu wathu, ife tinganene chiyani titachita zoipa zonsezi? Taphwanya malamulo anu,
11amene mudatipatsa kudzera mwa aneneri atumiki anu. Mudaŵauza kuti, ‘Dziko mukuloŵamo kuti mulilandelo ndi dziko lodetsedwa ndi zonyansa za mitundu ya anthu a m'maikomo. Adzaza dziko lonselo ndi zoipa zaozo.
12Eks. 34.11-16; Deut. 7.1-5 Nchifukwa chake musakwatitse ana anu aakazi kwa ana ao aamuna, ndipo ana ao aakazi asakwatiwe ndi ana anu aamuna. Musakhale nawo mumtendere kapena kugwirizana nawo pa malonda, ngati mufuna kukhala amphamvu ndi kumadya zabwino za m'dzikomo, ndi kusiyira ana anu dziko limeneli kuti likhale choloŵa chao mpaka muyaya.’
13Inde zonsezi zatigwera kaamba ka ntchito zathu zoipa ndi uchimo wathu waukulu. Komabe Inu Mulungu wathu, mwangotilanga pang'ono, kuyerekeza ndi kukula kwa kuchimwa kwathu, ndipo mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke.
14Kodi ife nkuphwanyanso malamulo anu ndi kukwatirana ndi anthu a mitundu ina, amene amachita zonyansa zimenezi? Kodi simudzakwiya nafe ndi kutiwononga popanda wina wotsala, kapena wina aliyense wopulumuka?
15Inu Chauta, Mulungu wa Israele, ndinu achifundo pakuti ife ndife otsala amene tapulumuka, monga m'mene tiliri lero lino. Taima pano pamaso panu, tikuzindikira kuchimwa kwathu. Choncho palibe ndi mmodzi yemwe amene angaime pamaso panu chifukwa cha zochimwazi.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.