1Chauta, Ambuye athu,
dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.
Kumwamba amaimba nyimbo zotamanda ulemerero wanu.
2 Mt. 21.16 Nawonso ana ndi makanda omwe amauimbira.
Mwamanga linga chifukwa cha adani anu,
kuti mugonjetse onse okuukirani.
3Ndikamayang'ana ku thambo lanu
limene mudapanga ndi manja anu,
ndikamaona mwezi ndi nyenyezi
zimene mudazikhazika kumeneko,
4 Yob. 7.17, 18; Mas. 144.3; Ahe. 2.6-8 ndimadzifunsa kuti,
“Kodi munthu nchiyani
kuti muzimkumbukira,
mwana wa munthu nchiyani
kuti muzimsamalira?”
5 Lun. 2.23; Mphu. 17.1-4 Ndiyetu mudamlenga mochepera pang'ono
kwa Mulungu amene,
mudampatsa ulemerero ndi ulemu wachifumu.
6 1Ako. 15.27; Aef. 1.22; Ahe. 2.8 Mudampatsa ulamuliro pa ntchito za manja anu.
Mudamgonjetsera zolengedwa zonse,
7nkhosa, ng'ombe ndi nyama zakuthengo,
8mbalame zamumlengalenga, nsomba zam'nyanja,
ndi zonse zoyenda pansi pa nyanja.
9Chauta, Ambuye athu,
dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.