1 Chiv. 10.9, 10 Pamenepo Mulungu adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya chimene ndikukupatsachi. Idya mpukutuwu ndipo pita ukalankhule ndi Aisraele.”
2Motero ine ndidayasama, ndipo adandipatsa mpukutu kuti ndidye.
3Tsono adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu ndikukupatsawu, ukhute.” Choncho ndidadya, ndipo unkatsekemera ngati uchi.
4Kenaka adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, pita kwa Aisraele, ukaŵauze mau anga.
5Sindikukutuma kwa anthu olankhula chilankhulo chachilendo ndi chovuta ai, ndikukutuma kwa Aisraele.
6Sindikukutuma kwa mitundu yambiri ya anthu amene chilankhulo chao nchachilendo ndi chovuta, amenenso sungathe kumvetsa zimene akulankhula. Ndithudi, ndikadakutuma kwa anthu achilendo otero, bwenzi iwo atakumvera.
7Koma Aisraele sadzakumvera, chifukwa safuna kundimvera Ine. Onsewo ngaliwuma ndi a mtima wosamvera.
8Tsono Ine ndidzakusandutsa waliwuma ndi wolimba mtima monga iwo omwewo.
9Ndidzakulimbitsa kupambana thanthwe lina lililonse, kuti ukhale wolimba ngati mwala wa daimondi. Usachite nawo mantha anthu aupanduwo.”
10Mulungu adapitiriza nati, “Iwe mwana wa munthu, umvetsetsetu zonse zimene ndikukuuza, ndipo uzikumbukire.
11Tsopano upite kwa Aisraele anzako amene ali ku ukapolo, ukalankhule nawo. Kaya akamvera kaya akakana, uzikaŵauza kuti, ‘Zimene akunena Ambuye Chauta nzakutizakuti,’ ”
12Pamenepo Mzimu wa Mulungu udandinyamula, ndipo kumbuyo kwanga ndidamva liwu lamphamvu ngati chivomezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Chauta kumene Iye amakhala!”
13Phokoso ndidaalimvalo linali la mapiko a zilengolengo zija akukhudzana mu mlengalenga, ndiponso phokoso la mikombero ya pambali pake ija, lomveka ngati chivomezi chachikulu.
14Mzimu wa Mulungu udandikweza ndi kundinyamula, ndipo ndidachokapo ndili ndi mtima woŵaŵa ndi wonyuka. Mphamvu za Chauta zidandiloŵa dzolimba.
15Motero ndidafika kwa amene anali ku ukapolo ku Telabibu, pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Ndidakhala pansi pakati pao masiku asanu ndi aŵiri, ndili wothedwa nzeru kwabasi.
Mulungu ampatsa Ezekiele udindo wa mlonda16Masiku asanu ndi aŵiriwo atatha, Chauta adandipatsira uthenga. Adati,
17“Iwe mwana wa munthu, ndakuika kuti ukhale mlonda woyang'anira Aisraele. Uzikati ukamva mau anga, uzikaŵachenjeza.
18Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa,’ iwe nupanda kumchenjeza kuti aleke makhalidwe oipawo, kuti akhalebe ndi moyo, munthuyo adzafadi ali wochimwa, koma iweyo ndidzakuzenga mlandu chifukwa cha imfa yake.
19Koma munthu woipa ukamchenjeza kuti asiye njira zake zoipa, iye nkumapitirizabe makhalidwe ake oipawo, adzafa ali ochimwa, Koma iweyo udzapulumutsa moyo wako.
20“Ngati munthu wokhulupirira ayamba kuchita uchimo, Ine nkumuika m'zoopsa, ameneyo adzafa. Ngati iweyo sudamchenjeze, inde adzafa chifukwa cha kuchimwa kwakeko, ndipo kukhulupirika kwake sindidzakukumbukira, koma tsono mlandu wa imfa yake udzakhala pa iwe.
21Koma ukamchenjeza kuti asachimwe, iye nkulekadi kuchimwa, mosapeneka konse adzapulumutsa moyo wake, chifukwa chotsata chenjezo lako. Ndipo iwenso udzapulumutsa moyo wako.”
Ezekiele adzakhala wosatha kulankhula22Nthaŵi ina ndidamva kuti mphamvu za Chauta zandiloŵa kwambiri, ndipo Iye adandiwuza kuti “Nyamuka, upite ku chigwa. Ndidzalankhula nawe kumeneko.”
23Choncho ndidanyamuka kupita ku chigwa. Kumeneko ndidaona ulemerero wa Chauta, monga momwe ndidaauwonera ku mtsinje wa Kebara. Pomwepo ndidadzigwetsa pansi chafufumimba.
24Koma Mzimu wa Mulungu udaloŵa mwa ine, ndipo udandiimiritsa. Apo Chauta adandilankhula nandiwuza kuti, “Pita kwanu, ukadzitsekere m'nyumba mwako.
25Ndipo kumeneko, iwe mwana wa munthu, adzakumanga ndi zingwe, kotero kuti sudzatha kuyendanso pakati pa anthu.
26Ndidzakangamiza lilime lako kukhosi, kotero kuti sudzathanso kulankhula ndi kuŵachenjeza, chifukwa ndi anthu aupandu.
27Koma pamene ndidzayambe kulankhula nawe, ndidzakupatsa mphamvu zolankhulira. Ndipo udzaŵauze kuti, ‘Zimene akunena Ambuye Chauta nzakutizakuti.’ Wofuna kumva, amve. Wosafuna kumva, akhale, popeza kuti anthuwo ngaupandu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.