1Pamenepo mfumu Yosiya adatumiza mau kukaitana akuluakulu onse a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti adzasonkhane.
2Ndipo mfumuyo idapita ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, nzika zonse za mu Yerusalemu, ansembe ndi aneneri, ndiponso anthu onse aakulu ndi aang'ono omwe. Tsono iye adaŵerenga pamaso pao mau onse a m'buku lija la chipangano limene lidaapezeka m'Nyumba ya Mulungu.
3Kenaka mfumuyo idaimirira pa nsanja yake, ndipo idachita chipangano pamaso pa Chauta kuti idzatsata njira za Chauta, ndipo kuti idzasunga mau, malamulo ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndiponso ndi moyo wake wonse, ndipo kuti idzagwiritsa ntchito mau a chipangano chimenechi monga momwe adalembedwera m'bukulo. Tsono anthu onse nawonso adavomera kutsata chipanganocho.
4 2Maf. 21.3; 2Mbi. 33.3 Tsono mfumu Yosiya adalamula Hilikiya, wansembe wamkulu, ndiponso ansembe othandiza ndi alonda apakhomo, kuti achotse m'Nyumba ya Mulungu zinthu zonse zopembedzera Baala, fano la Asera ndiponso mafano a zinthu zakuthambo. Zonsezo adazitenthera kunja kwa Yerusalemu, ku minda ya ku Kidroni, ndipo phulusa lake adapita nalo ku Betele.
5Yosiya adatulutsa ansembe a mafano amene mafumu a ku Yuda adaŵakhazika kuti azipereka nsembe ku akachisi ku mizinda ya m'dziko la Yuda ndi ku malo ozungulira Yerusalemu. Adatulutsanso amene ankapereka nsembe kwa Baala, kwa dzuŵa, kwa mwezi, kwa nyenyezi ndi kwa zinthu zonse zakuthambo.
6Adachotsa fano la Asera m'Nyumba ya Chauta, napita nalo kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni. Tsono adalitenthera ku mtsinje wa Kidroniko, naliperapera, nkutaya phulusa lake pa manda a anthu wamba.
7Adagwetsa tinyumba ta amuna ochitana zadama ku Nyumba ya Mulungu, ku malo amene akazi ankalukira mikanjo yovala anthu opembedza Asera.
8Yosiya adabwera nawo ansembe a ku mizinda ya ku Yuda, naononga akachisi opembedzerako mafano kumene ansembe aja ankaperekera nsembe, kuyambira ku Geba mpaka ku Beereseba. Adagwetsa akachisi onse amene anali pa chipata cha khomo la Yoswa, nduna ya mzindawo. Maloŵa anali ku dzanja lamanzere la khomo la mzindawo.
9Ansembe a ku akachisiwo sadaŵalole kufika ku guwa la Chauta ku Yerusalemu, komabe ankadya nao buledi wosatupitsa ndi ansembe anzao kumeneko.
10Yer. 7.31; 19.1-6; 32.35; Lev. 18.21 Mfumu Yosiya adaononganso ng'anjo yotchedwa Tofeti imene inali m'chigwa cha ana a Hinomu, kuti munthu aliyense asapereke mwana wake wamwamuna kapena wamkazi ngati nsembe kwa Moleki.
11Adachotsanso akavalo amene mafumu a ku Yuda adaaŵapereka ngati nsembe kwa dzuŵa. Akavalo amenewo ankaŵasunga pa bwalo la Nyumba ya Mulungu pafupi ndi chipata choloŵera m'Nyumbamo, ndiponso chipinda cha Natani Meleki, mkulu wosunga nyumbayo. Kenaka adatentha magaleta opembedzera dzuŵa.
122Maf. 21.5; 2Mbi. 33.5 Pambuyo pake mfumuyo idagwetsa ndi kuphwanyaphwanya maguwa a pa denga la chipinda chapamwamba cha Ahazi, amene adaŵamanga mafumu a ku Yuda, ndiponso maguwa amene Manase adaŵamanga pa mabwalo aŵiri a Nyumba ya Chauta. Ndipo adataya fumbi lake mu mtsinje wa Kidroni.
131Maf. 11.7 Pambuyo pake mfumuyo idaononganso akachisi opembedzerapo mafano amene anali kuvuma kwa Yerusalemu, kumwera kwa phiri lotchedwa Chiwonongeko. Maguwawo Solomoni, mfumu ya ku Israele, adaaŵamangira fano lonyansa la Asidoni lotchedwa Asitoreti, ndi la Amowabu lotchedwa Kemosi, ndiponso la Aamoni lotchedwa Milikomu.
14Adaphwanyanso zipilala zamiyala naononga mafano onse a Asera, ndipo pa malo ao adamwazapo mafupa a anthu akufa.
15 1Maf. 12.33 Yosiya adagwetsanso guwa la ku Betele, limene Yerobowamu, mwana wa Nabati, adaalimanga ku kachisi pa chitunda. Yerobowamuyo adaachimwitsa Aisraele ndi guwa limenelo. Ndipo Yosiya adagumula guwalo naphwanyanso miyala yake, nkuiperapera, naisandutsa fumbi. Adatenthanso kachisiyo, pamodzi ndi mafano a Asera.
161Maf. 13.2 Atatero, Yosiya adacheuka naona manda paphiripo. Tsono adatuma anthu kuti akatenge mafupa m'mandamo, ndipo adaŵatenthera paguwapo. Potero adalidetsa monga momwe Chauta adaanenera kudzera mwa mneneri wake amene adaaloseratu zimenezi.
171Maf. 13.30-32 Apo mfumu idafunsa kuti, “Kodi manda ena ndikuwona apowo ngayani?” Anthu amumzindamo adamuuza kuti, “Amenewo ndi manda a mneneri wa Mulungu wa ku Yuda amene adaneneratu za zimene inu mwalichita guwa la ku Betele.”
18Yosiya adati, “Mlekeni. Munthu asachotse mafupa akewo ai.” Motero mafupawo adangoŵaleka pamodzi ndi mafupa a mneneri wa ku Samariya uja.
19Yosiyayo adaononganso nyumba zonse zopembedzeramo mafano zija zimene zinali m'mizinda ya ku Samariya. Mafumu a ku Israele ndiwo amene adaamanga zimenezi, naputa mkwiyo wa Chauta potero. Yosiya uja adachita chimodzimodzi kumeneko monga momwe adaachitira ku Betele.
20Adapha ansembe onse amene ankatumikira ku nyumba zochipembedzeramo mafano kumeneko. Adaŵaphera pa maguwa ao, natentha mafupa a anthuwo pamaguwapo. Pambuyo pake adabwerera ku Yerusalemu.
Yosiya achita chikondwerero cha Paska21Tsono mfumu Yosiya adalamula anthu onse kuti, “Muchite chikondwerero cha Paska, kulemekeza Chauta, Mulungu wanu, potsata zimene zidalembedwa m'buku lachipangano.”
22Paska yotereyi inali isanachitikepo kuyambira nthaŵi ya aweruzi amene ankatsogolera Aisraele, kapena nthaŵi ya mafumu a ku Israele, kapenanso nthaŵi ya mafumu a ku Yuda.
23Koma chaka cha 18 cha ufumu wa Yosiya, Paska imeneyi adaichitira Chauta ku Yerusalemu.
24Masiku amenewo Yosiya adachotsanso anthu amaula, amatsenga, milungu ya m'nyumba ndiponso mafano ena onse, kudzanso zonyansa zonse zimene zinali ku dziko la Yuda ndi ku Yerusalemu. Adachita zimenezi kuti atsate Malamulo amene adalembedwa m'buku lomwe wansembe Hilikiya adalipeza m'Nyumba ya Chauta.
25Yosiyayo asanaloŵe ufumu, panalibenso mfumu ina yofanafana naye imene idatembenukira kwa Chauta ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse ndiponso ndi mphamvu zake zonse, potsata Malamulo a Mose. Ndipo iye atafa, sipadakhalenso wina aliyense wofanafana ndi iyeyo.
26Komabe Chauta sadaleke kukwiya kwake koopsa kumene adakwiyira Yuda, chifukwa choti Manase adaachita kuuputa mkwiyo wa Chautawo.
27Choncho Chauta adati, “Ngakhale anthu a ku Yuda omwe, ndidzaŵachotsa pamaso panga, monga momwe ndachotsera anthu a ku Israele. Ndidzagwetsa ngakhale mzinda uno wa Yerusalemu umene ndidausankha, pamodzi ndi Nyumba imene ndidati, ‘Dzina langa lidzakhala m'menemo.’ ”
Kutha kwa ufumu wa Yosiya(2 Mbi. 35.20—36.1)28Tsono ntchito zina za Yosiya pamodzi ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
29Pa masiku akewo Farao Neko, mfumu ya ku Ejipito, adapita kukathandiza mfumu ya ku Asiriya ku mtsinje wa Yufurate. Mfumu Yosiya adapita kukamenyana naye nkhondo. Koma Farao Neko adamupha Yosiyayo ku Megido pa nkhondoyo.
30Pamenepo nduna zake zidamnyamulira pa galeta kuchokera ku Medigo, nkupita naye ku Yerusalemu, ndipo zidamuika m'manda akeake. Kenaka anthu a ku Yuda adatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namdzoza, ndipo iyeyo adaloŵa ufumu m'malo mwa bambo wake.
Yehowahazi mfumu ya ku Yuda31Yehowahazi anali wa zaka 23 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Mai wake anali Hamutala, mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
32Adachita zoipa kuchimwira Chauta potsata zonse zimene makolo ake ena ankachita.
33Tsono Farao Neko adamuika m'ndende ku Ribula m'dziko la Hamati, kuti asalamulirenso ku Yerusalemu. Pambuyo pake Faraoyo adaŵakhometsa msonkho wa siliva wolemera makilogramu 3,400, ndiponso golide wolemera makilogramu 34.
34Yer. 22.11, 12 Kenaka Farao Neko wa ku Ejipito adaika Eliyakimu, mwana wa Yosiya, kuti akhale mfumu m'malo mwa bambo wake, ndipo adasintha dzina lake kuti akhale Yehoyakimu. Farao Neko adatenga Yehowahazi kupita naye ku Ejipito, ndipo adafera komweko.
Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda35Tsono Yehoyakimu nayenso ankapereka siliva ndi golide kwa Farao. Komatu ankachita kukhometsa msonkho m'dziko mwakemo kuti apereke ndalamazo kwa Farao, monga momwe Farao adamlamulira. Ankatenga siliva amene anthu am'dzikomo ankayenera kukhoma, pamodzi ndi golide yemwe, malinga ndi chuma cha munthu aliyense, ndipo ankazipereka kwa Farao Neko.
36 Yer. 22.18, 19; 26.1-6; 35.1-19 Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Zebida, mwana wa Pedaya, wa ku Ruma.
37Yehoyakimu adachita zoipa kuchimwira Chauta potsata zonse zimene makolo ake ena ankachita.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.