1 Am. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Yohane adachoka ku Gazara nakadziŵitsa atate ake Simoni zimene Kendebeo ankachita.

2Tsono Simoni adaitana ana ake aŵiri oyamba, Yuda ndi Yohane, naŵauza kuti, “Ine ndi abale anga, pamodzi ndi banja la atate anga, takhala tikumenya nkhondo za Aisraele kuyambira nthaŵi ya unyamata wathu mpaka lero. Zonse zimene tidachita zidatikhalira bwino, kotero kuti kaŵirikaŵiri tidapulumutsa Aisraele.

3Koma tsopano ine ndakalamba, ndipo inu, mwa chifundo cha Mulungu, mwakula. Khalani oloŵa m'malo mwanga ndi m'malo mwa abale anga. Katsogolereni nkhondo za mtundu wanu. Thandizo lakumwamba likhale nanu.”

4Pamenepo Yohane adasankhula ankhondo oyenda pansi 20,000 ndi ena okwera pa akavalo. Onse adanyamuka kukamenyana nkhondo ndi Kendebeo. Adagona usiku ku Modini.

5Adadzuka m'mamaŵa napita ku chigwa. Adangoona gulu lalikulu la adani oyenda pansi ndi okwera pa akavalo likubwera kudzakumana nawo. Koma panali mtsinje pakati pao.

6Yohane ndi ankhondo ake adamanga zithando zao kuyang'anana ndi adaniwo. Koma ataona kuti anthu ake akuwopa kuwoloka mtsinje uja, Yohane adayambira ndiye kuwoloka. Anthu ake pomuwona, nawonso adaoloka pambuyo pake.

7Adagaŵa gulu lake lankhondo paŵiri, naika okwera pa akavalo pakati pa oyenda pansi, popeza kuti adani ao okwera pa akavalo anali ochuluka.

8Tsono adaliza malipenga ankhondo. Pamenepo Kendebeo pamodzi ndi gulu lake lankhondo adathaŵa. Ambiri adagwa naafa, otsala adathaŵira ku linga.

9Tsiku lomwelo Yudasi, mbale wake wa Yohane, adalasidwa, koma Yohane adaŵalondola adaniwo mpaka ku Kedroni, mzinda umene Kendebeo adaaumanga.

10Othaŵawo adakadzitsekera m'nsanja zankhondo zokhala m'miraga ya Azoto. Yohane adautentha mzindawo, mwakuti anthu 2,000 adaphedwa. Kenaka Yohane adabwerera ku Yudeya mwamtendere.

Ptolemeyo apha Simoni

11Ptolemeyo, mwana wa Abubusi, adasankhidwa kukhala mtsogoleri wa ankhondo ku chigwa cha Yeriko. Anali ndi golide ndi siliva wochuluka,

12chifukwa anali mkamwini wa Simoni, mkulu wa ansembe.

13Adayamba kudzitukumula. Adafuna kukhala mwini dziko, choncho adaganiza za kupha Simoni ndi ana ake mwachiwembu.

14Simoni akuyendera mizinda ya ku Yudeya, kuti aone zosoŵa zao, tsiku lina adatsikira ku Yeriko iyeyo pamodzi ndi ana ake, Matatiasi ndi Yudasi, chaka cha 177, pa mwezi wa Sebati, ndiye kuti mwezi wa khumi ndi chimodzi.

15Mwana wa Abubusi uja adaŵachenjerera, naŵalandira m'kalinga kotchedwa Doke, kamene adaamanga. Adaŵakonzera madyerero kumeneko, nabisamo anthu.

16Simoni ndi ana ake ataledzera, Ptolemeyo ndi anthu ake adadzambatuka, natenga zida zao nkulumphira Simoni pakati pa madyerero. Adamupha iyeyo ndi ana ake aŵiri aja ndi anyamata ake ena.

17Motero adachita chinyengo chachikulu, kubwezera zoipa m'malo mwa zabwino.

18Tsono Ptolemeyo adalembera mfumu mau ofotokoza zimenezo, napempha kuti mfumuyo imtumizire ankhondo odzamthandiza, ndiponso kuti ampatse dziko la Ayudalo ndi mizinda yake.

19Adatumanso anthu ena ku Gazara kuti akaphe Yohane. Adalemba makalata kwa akulu ankhondo kuti abwere adzalandire siliva ndi golide ndi mphatso zina.

20Adatumanso anthu ena kuti akalande Yerusalemu ndi phiri la ku Nyumba ya Mulungu.

21Koma munthu wina adatsogola nakadziŵitsa Yohane, amene anali ku Gazara, kuti atate ake ndi abale ake aphedwa, ndipo kuti Ptolemeyo watuma asilikali ake kuti adzamuphe.

22Atamva zimenezo, Yohane adavutika kwabasi mu mtima. Adaŵagwira anthu amene adaabwera kwa iye kuti adzamuphe, naŵapha, chifukwa adaadziŵadi kuti akufuna kumupha.

23Ntchito zina za Yohane kuyambira pamene adaloŵezera bambo wake ngati mkulu wa ansembe, monga nkhondo, ntchito zautotomoyo, kumanga malinga a mizinda ndi zochita zake zina,

24zonsezo zidalembedwa m'buku la unsembe wake, kuyambira tsiku limene adakhala mkulu wa ansembe m'malo mwa atate ake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help