1Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza anthu onse, amoyo ndi akufa omwe, ndipo potamanda kubwera kwake ndi ufumu wake wa Khristuyo ndikukulamula ndithu kuti
2uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.
3Paja nthaŵi idzafika pamene anthu azidzakana chiphunzitso choona. M'malo mwake, chifukwa cholakalaka kumva zoŵakomera zokha, adzadzisankhira aphunzitsi ochuluka omaŵauza zimene iwo akufuna.
4Adzafulatira choona, osafunanso kuchimva, ndipo adzangotsata nthano chabe.
5Koma iwe, uzikhala maso pa zonse, pirira pa zoŵaŵa, gwira ntchito yolalika Uthenga Wabwino. Kwaniritsa udindo wako mosamala.
6Paja ine ndiye moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthaŵi yafika kuti ndinyamuke ulendo wanga wochoka m'moyo uno.
7Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro.
8Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira. Ambuye amene ali Woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphothoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso.
Mau ena9Uyesetse kubwera kuno msanga.
10Akol. 4.14; Fil. 1.24; 2Ako. 8.23; Aga. 2.3; Tit. 1.4Paja Dema adandisiya chifukwa chokonda zapansipano, adapita ku Tesalonika. Kresike adapita ku Galatiya, ndipo Tito adapita ku Dalamatiya.
11Akol. 4.14; Fil. 1.24; Ntc. 12.12, 25; 13.13; 15.37-39; Akol. 4.10; Fil. 1.24Luka yekha ndiye ali ndi ine. Ukatenge Marko udzabwere naye kuno, chifukwa amene uja angathe kundithandiza pa ntchito.
12Ntc. 20.4; Aef. 6.21, 22; Akol. 4.7, 8Ndidatuma Tikiko ku Efeso.
13Ntc. 20.6Pobwera unditengereko mwinjiro wanga umene ndidasiya kwa Karpo ku Troasi. Unditengerenso mabuku anga, makamaka aja azikopaŵa.
14 1Tim. 1.20; Mas. 62.12; Aro. 2.6 Aleksandro, mmisiri wa zosulasula uja adandichita zoipa kwambiri. Ambuye adzamlanga molingana ndi zimene adachita.
15Iwenso uchenjere naye, chifukwa iye uja adatsutsa kwamphamvu zolalika ife.
16Pamene ndinkadziteteza pa mlandu wanga poyamba paja, panalibe ndi mmodzi yemwe amene adabwera kudzandithandiza, onse adangondisiya ndekha. Mulungu aŵakhululukire.
17Koma Ambuye adakhala nane limodzi, adandilimbitsa mtima kuti ndilalike mau onse a Uthenga Wabwino, kuti anthu a mitundu yonse aŵamve. Motero ndidapulumuka m'kamwa mwa mkango.
18Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundiloŵetsa mu Ufumu wake wa Kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen.
Mau otsiriza19 Ntc. 18.2; 2Tim. 1.16, 17 Uperekeko moni kwa Prisika ndi Akwila ndiponso kwa a m'banja la Onesifore.
20Ntc. 19.22; Aro. 16.23; Ntc. 20.4; 21.29Erasito adatsalira ku Korinto, ndipo Trofimo ndidamsiya akudwala ku Mileto.
21Uyesetse ndithu kubwera isanafike nyengo yachisanu. Yubulo, Pude, Lino, Klaudia, ndi abale ena onse akuti moni.
22Ambuye akhale nawe. Mulungu akukomereni mtima nonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.