Deut. 29 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chipangano cha Chauta ndi Aisraele m'dziko la Amowabu

1Aŵa ndi mau a chipangano chimene Chauta adalamula Mose kuti achite ndi Aisraele m'dziko la Mowabu. Mau achipangano ameneŵa adangoonjezeka pa mau aja achipangano amene Chauta adaachita ndi iwowo ku phiri la Horebu kuja.

2Mose adaitana Aisraele onse aja, naŵauza kuti: Paja mudadziwonera nokha zimene Chauta adachita mfumu ya ku Ejipito ndi nduna zake ndi dziko lake lonse.

3Mudaonanso miliri yoopsa ija, zozizwitsa zija ndi zodabwitsa zimene adachita.

4Koma mpaka tsopano, Chauta sadakupatseni mtima womvetsa zinthu zimenezi, kapena maso openya, kapena makutu akumva.

5Pa zaka makumi anai zimene Chauta adakutsogolerani m'chipululu muja, zovala zanu sizidathe, ndipo nsapato zanu sizidang'ambike.

6Munalibe buledi woti muzidya, ngakhalenso vinyo kapena chakumwa chaukali, koma Chauta adakupatsani zonse zokusoŵani, kuti mudziŵe kuti Iye ndi Chauta, Mulungu wanu.

7Num. 21.21-30; Num. 21.31-35 Ndipo titafika pa malo ano, mfumu Sihoni wa ku Hesiboni, pamodzi ndi mfumu Ogi wa ku Basani, adadza kuti alimbane nafe, koma tidaŵagonjetsa.

8Num. 32.33 Tidalanda dziko lao ndi kuligaŵira mafuko a Rubeni, Gadi ndiponso hafu la fuko la Manase.

9Mau onse a chipangano ichi muŵamvere mokhulupirika, kuti choncho mudzakhoze pa zonse zimene mudzachite.

10Lero lino, nonse mukuimirira pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, atsogoleri anu, akuluakulu anu, akalonga anu, anthu aamuna a Aisraele,

11zidzukulu zanu, akazi anu ndiponso alendo amene amakhala m'mahema mwanu, amene amakudulirani nkhuni ndi kumakutungirani madzi.

12Muli pano lero kuti mulumbire ndi kuchita chipangano chimene Chauta, Mulungu wanu, akupangana nanu.

13Motero, mudzakhala anthu a Chauta, ndipo Iyeyo adzakhala Mulungu wanu, monga momwe adalonjezera kwa inu ndi kulumbira kwa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.

14Sindinu nokha amene Chauta akupangana nanu chipangano ichi chochita ndi malumbiro.

15Chipangano chimenechi akupangana ndi munthu aliyense amene ali pano lero pamaso pa Chauta, Mulungu wathu, ndiponso ndi ena onse amene sali nafe kuno lero.

16Mukudziŵa m'mene tidakhalira ku Ejipito kuja, ndiponso m'mene unaliri ulendo poyenda pakati pa maiko a mitundu ina.

17Mafano ao oipa amitengo, amiyala, asiliva ndiponso agolide, amene anali pakati pao, mudaona kunyansa kwake.

18Ahe. 12.15 Chonde muchenjere kuti mwamuna kapena mkazi, ngakhale banja, kaya fuko, kungoti nonsenu amene muli pano lero lino, musapotoloke kuti muchoke kwa Chauta, Mulungu wanu, ndi kumapembedza milungu ya anthu a mitundu ina. Kuteroko kungofanafana ndi muzu umene umati ukakula, umasanduka chiphe.

19Chonde muchenjere kuti pasakhale wina pano lero, womva mau ameneŵa, komabe namanena mumtima mwake kuti zinthu zidzamuyenderabe bwino, ngakhale akhale wokanika chotani nkumachita zake. Zimenezi zidzangoputira nonsenu chiwonongeko, abwino ndi oipa omwe.

20Munthu wotere Chauta sadzamkhululukira. Ndithu Chauta adzamkwiyira ndi nsanje yoyaka. Matemberero olembedwa m'buku muno adzamgwera ndipo Chauta adzamuwonongeratu ndipo adzaiŵalika pa dziko.

21Chauta adzampatula pakati pa anthu a ku Israele onse ndipo adzamlanga ndi masoka potsata matemberero a chipangano olembedwa m'buku lino la malamulo.

22Anthu a mibadwo yanu yakutsogolo, monga zidzukulu zanu ndi alendo ochokera kutali, adzaŵapenya masoka amenewo, pamodzi ndi masautso amene Chauta adzagwetse pa dziko lanu.

23Gen. 19.24, 25 Minda yanu idzakhala yoguga, yodzaza ndi sulufule ndi mchere. M'minda imeneyo simudzamera kalikonse, ngakhale ndi udzu womwe. Dziko lanu lidzakhala ngati mizinda ija ya Sodomu ndi Gomora, ndiponso ya ku Adima ndi Zoboimu, imene Chauta adaononga pa nthaŵi imene anali wokwiya koopsa ija.

24Tsono dziko lonse lapansi lidzafunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani Chauta adachita zotere m'dziko lake? Kodi chifukwa chake chinali chiyani kuti mkwiyo wake uchite kuwopsa chotere?”

25Yankho la mafunso onseŵa lidzakhala lakuti, “Chifukwa chake nchakuti anthuŵa adaphwanya chipangano chimene adachita ndi Chauta, Mulungu wa makolo ao, nthaŵi imene Iyeyo adaŵatulutsa ku Ejipito.

26Adatumikira milungu ina imene sadaipembedzepo nkale lonse, milungu imene Chauta adaŵaletsa kuipembedza.

27Motero Chauta adakwiyira anthu ake, ndipo adaŵagwetsera masoka onse olembedwa m'buku muno.

28Chauta adakwiya koopsa, ndipo ali wokwiya chotero, adaŵachotseratu m'dziko lao ndi kuŵaponya m'dziko lachilendo, kumene ali lero lino.”

29Pali zinthu zina zimene Chauta, Mulungu wathu, sanatiululire; koma watiululira ifeyo ndi zidzukulu zathu malamulo ake amene tiyenera kuwamvera nthaŵi zonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help