2 Sam. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tchimo la Davide.

1 1Mbi. 20.1 Pa nyengo yophukira mitengo, nthaŵi imene mafumu ankakonda kukamenya nkhondo, Davide adatuma Yowabu ndi atsogoleri ake ndi ankhondo a Aisraele onse. Adaononga Aamoni, nazinga mzinda wa Raba ndi zithando zankhondo. Koma Davide adatsalira ku Yerusalemu.

2Zidangochitika kuti tsiku lina chakumadzulo, Davide adadzuka pabedi pake, namayenda pamwamba pa denga la nyumba yake yaufumu. Ali padengapo, adaona mkazi wina akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwabasi.

3Pomwepo Davide adatuma munthu kuti akafunsitse za mkaziyo. Ndipo munthuyo adamuuza kuti, “Mkazi ujatu ndi Bateseba, mwana wa Eliyamu, mwamuna wake ndi Uriya Muhiti.”

4Apo Davide adatuma amithenga kuti akamtenge mkaziyo. Iwo adabwera naye kwa Davide, ndipo Davideyo adagona naye. Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo atangomaliza kusamba. Pambuyo pake mkazi uja adabwerera kunyumba kwake.

5Kenaka ataona kuti waima, adatumiza mau kwa Davide kukamuuza kuti, “Inetu ndi mommuja, sindili bwino!”

6Atamva zimenezi Davide adatumiza mau kwa Yowabu kuti, “Umtumize Uriya, Muhiti uja, abwere kuno.” Yowabu adatumizadi Uriya kwa Davide.

7Uriya atabwera, Davide adamufunsa m'mene analiri Yowabu kunkhondoko, ndiponso m'mene analiri anthu, ndi m'menenso nkhondo inkayendera.

8Kenaka Davide adauza Uriya kuti, “Pita kunyumba kwako, ukapumuleko.” Uriya adatuluka ku nyumba ya mfumu, ndipo mfumu idatumiza mphatso kukapereka kwa Uriya.

9Koma Uriya adagona pakhomo pa nyumba ya mfumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake, sadapite kunyumba kwake.

10Tsono anthu adamuuza Davide kuti, “Uriyatu sadapite kunyumba kwake.” Davideyo adafunsa Uriya kuti, “Kodi suja iwe wachokera ku ulendo? Nanga bwanji sudapite kunyumba kwako?”

11Uriya adauza Davide kuti, “Bokosi lachipangano likukhala m'zithando, kudzanso Aisraele ndi Ayuda. Ndipo mbuyanga Yowabu pamodzi ndi ankhondo a mfumu akugona panja pamtetete. Ndiye ine ndingapite kunyumba kwanga kuti ndizikadya ndi kumwa, ndi kumakakhala ndi mkazi wanga? Pali inu amene, ine sindingachite zimenezo.”

12Apo Davide adauza Uriya kuti, “Utandale pompano lero, maŵa ndikulola kuti uzipita.” Choncho Uriya adatandala ku Yerusalemu tsiku limenelo mpaka m'maŵa mwake.

13Davide adaitana Uriya, nadya naye ndipo adamwa kwambiri, kotero kuti Davide adamledzeretsa. Komabe madzulo Uriya adapita kukagona pogona pake, pamodzi ndi antchito a mfumu, osapita kunyumba kwake.

14M'maŵa mwake Davide adalembera Yowabu kalata, napatsira Uriya yemweyo kalatayo kuti akapereke.

15M'kalatamo adalembamo kuti, “Uriyayo umuike patsogolo penipeni pamene pakulimba nkhondo, ndipo umlekerere yekha kuti alasidwe ndi kuphedwa.”

16Choncho pamene Yowabu ankazinga mzindawo, adaika Uriya pamalo pamene ankaŵadziŵa kuti pali ankhondo amphamvu.

17Tsono ankhondo amumzindamo adatuluka nadzamenyana ndi Yowabu. Ndipo ena mwa ankhondo a Davide adaphedwa. Uriya, Muhiti uja, nayenso adaphedwa.

18Zitatero, Yowabu adatuma wamthenga kwa Davide kukamuuza zonse zimene zidachitika kunkhondoko.

19Adauza wamthengayo kuti, “Utatha kumuuza mfumu mbiri yonse ya nkhondo,

20tsono ngati mfumu ikapse mtima, nikakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mudapita kufupi ndi mzinda kuti mukamenye nkhondo? Kodi simunkadziŵa kuti adzakulasani kuchokera m'kati mwa linga?

21Owe. 9.53Kodi Abimeleki mwana wa Gideoni adamupha ndani? Kodi adamupha si mkazi, pomkunkhunizira mwalawamphero kuchokera pa linga, kotero kuti adafera ku Tebezi? Chifukwa chiyani mudakafika pafupi ndi khoma?’ Pamenepo iweyo ukanene kuti, ‘Wankhondo wanu, Uriya Muhiti uja, nayenso adaphedwa.’ ”

22Wamthenga uja adapita, nakafika kwa Davide, nakamuuza zonse zimene Yowabu adamuuza kuti akanene.

23Adauza Davide kuti, “Adani athu adaatipambana, ndipo adaatuluka kukalimbana nafe ku thengo. Koma ife tidaŵabweza mpaka ku khomo lakuchipata.

24Tsono anthu oponya mivi ankalasa ankhondo anu kuchokera m'linga. Ndipo ankhondo ena mwa ankhondo a inu mfumu adaphedwa. Wankhondo wanu uja, Uriya Muhiti, nayenso adaphedwa.”

25Apo Davide adauza wamthenga uja kuti, “Kamuuze Yowabu kuti, ‘Zimenezi usavutike nazo, poti wakufa sadziŵika. Ulimbike polimbana ndi mzindawo, ndi kuugonjetsa.’ Choncho ukamlimbitse mtima Yowabuyo.”

26Pamene mkazi wa Uriya adamva kuti mwamuna wake Uriya adaphedwa, adalira, kulira mwamuna wake.

27Mkaziyo atatha kulira malirowo, Davide adatuma munthu nakamtenga, nkubwera naye kunyumba kwa mfumu, ndipo Davide adamukwatira. Mkaziyo adambalira mwana wamwamuna. Koma zimene adachita Davidezi zidaipira Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help