1Pa nthaŵi imeneyo Abiya, mwana wa Yerobowamu, adayamba kudwala.
2Ndiye Yerobowamu adauza mkazi wake kuti, “Tiye udzizimbaitse, munthu asakudziŵe kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu, ndipo upite ku Silo kwa mneneri Ahiya, amene adanena za ine, kuti ndidzakhala mfumu yolamulira anthu aŵa.
3Utenge mitanda khumi yabuledi, makeke ndiponso botolo la uchi, upite kwa iyeyo. Iye adzakuuza zimene zidzamuwonekere mwanayu.”
4Mkazi wa Yerobowamu adadzizimbaitsadi, ndipo adapita ku Silo, nakafika ku nyumba ya Ahiya. Ahiya sankatha kupenya bwino, ankangoona ngati nkhungu, chifukwa cha ukalamba.
5Chauta adauza Ahiya kuti, “Taona, mkazi wa Yerobowamu akubwera kudzafunsa iwe za mwana wake, pakuti akudwala. Ndiye iwe udzamuuze zakutizakuti mkaziyo. Akafika adzadzibisa, nkukhala ngati mkazi wina.”
6Tsono Ahiya atangomva mgugu wa mapazi ake akuloŵa pa khomo, adati “Loŵa, iwe mkazi wa Yerobowamu, bwanji ukudzibisa? Ndakutengera mau oŵaŵa.
7Pita, kamuuze Yerobowamu kuti Chauta, Mulungu wa Israele, akuti, ‘Ine ndidakukweza pakati pa anthu, ndipo ndidakusandutsa mtsogoleri wa anthu anga a ku Israele.
8Ndidachotsa ufumu ku banja la Davide ndi kuupereka kwa iwe. Komabe iwe sudafanefane ndi Davide mtumiki wanga, amene ankamvera malamulo anga, ndipo ankanditsata ndi mtima wake wonse, namachita zimene Ine ndimafuna.
9Koma iwe wachita zoipa kupambana onse amene analipo kale, iwe usanakhale pa mpando waufumu, pakuti wadzipangira milungu ina ndiponso mafano osungunula. Pakutero wandipsetsa mtima kwabasi. Ineyo wanditayiratu kumbuyo.
101Maf. 15.29 Nchifukwa chake ndidzagwetsa mavuto pa banja lako, iwe Yerobowamu. Ndidzaononga mwamuna aliyense wa pa banja lako, kapolo pamodzi ndi mfulu yomwe, m'dziko la Israele. Ndidzaononga kwathunthu banja la Yerobowamu monga m'mene munthu amachotsera ndoŵe pa bwalo mpaka yonse itatha.
11Aliyense m'banja la Yerobowamu, amene adzafere mu mzinda, agalu adzamudya. Aliyense amene adzafere ku thengo, mbalame zidzamudya. Ndatero Ine Chauta.’
12Nchifukwa chake tsono nyamuka, upite kunyumba kwako. Phazi lako likangoponda mumzindamo, mwanayo adzafa.
13Aisraele onse adzalira maliro ake, ndipo adzamuika, pakuti iye yekhayo mwa anthu a m'banja la Yerobowamu ndiye adzaikidwe ku manda, chifukwa Chauta, Mulungu wa Aisraele, wakondwa ndi iye yekha pa banja lonse la Yerobowamu.
14Kuwonjezera pamenepo, Chauta adzadzisankhira mfumu yolamulira a ku Israele, imene idzaonongeretu banja la Yerobowamu. Tsiku lake ndi lero, wamvatu!
15Chauta adzagwedeza Israele ngati bango lapamadzi, ndipo adzachotsa anthu a ku Israele m'dziko labwinoli, limene Iye adapatsa makolo ao. Adzaŵamwazira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, chifukwa choti iwo adadzipangira mafano a Asera, mulungu wachikazi, nakwiyitsa Chauta pakutero.
16Choncho Chauta adzaŵataya a ku Israele chifukwa cha zoipa za Yerobowamu, zimene adachita iye mwini ndi kuŵachimwitsanso Aisraelewo.”
17Tsono mkazi wa Yerobowamu adachoka napita ku Tiriza. Atangofika pa khomo la nyumba yake, mwana uja adamwalira.
18Aisraele adamuika, nalira maliro ake, monga momwe Chauta adaanenera kudzera mwa mneneri Ahiya.
Imfa ya Yerobowamu19Tsono ntchito zonse za Yerobowamu, m'mene ankamenyera nkhondo ndi m'mene ankalamulira, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a Aisraele.
20Nthaŵi imene Yerobowamu adakhala mfumu idakwana zaka makumi aŵiri. Ndipo adamwalira, naikidwa m'manda. Pambuyo pake Nadabu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Mfumu Rehobowamu wa ku Yuda(2 Mbi. 11.5—12.15)21Rehobowamu, mwana wa Solomoni, anali mfumu ya ku Yuda. Anali wa zaka 41 nthaŵi imene ankaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Chauta adaausankha pakati pa mafuko onse a Aisraele, kuti anthu azimpembedzerako. Mai wake anali Naama, wa kwa Aamoni.
22Masiku amenewo anthu a ku Yuda ankachita zoipa, ankachimwira Chauta kupambana m'mene adaachitira makolo ao onse, nakwiyitsa Mulungu.
232Maf. 17.9, 10Pakuti iwonso adadzimangira akachisi opembedzerapo mafano pa zitunda zina, ndi kuimika miyala ndi mitengo yachipembedzo pa phiri lalitali lililonse, ndiponso patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.
24Deut. 23.17 Kuwonjezera pamenepo, m'dzikomo munkapezeka anthu ena ochitana zadama potsata chipembedzo chao. Anthu ankachita zonyansa zonse zimene inkachita mitundu ya anthu amene Chauta adaaipirikitsa pofika Aisraele.
25 2Mbi. 12.2-8 Chaka chachisanu cha ufumu wa Rehobowamu, Sisake, mfumu ya ku Ejipito, adabwera kudzathira Yerusalemu nkhondo.
261Maf. 10.16, 17; 2Mbi. 9.15, 16 Adalanda chuma cha ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi chuma cha ku nyumba ya mfumu. Adatenga zonse, ngakhalenso zishango zomwe zagolide zimene Solomoni adaapanga.
27Pambuyo pake mfumu Rehobowamu adapanga zishango zamkuŵa m'malo mwake, nazipereka m'manja mwa akapitao a alonda amene ankalonda pakhomo pa nyumba ya mfumu.
28Tsono nthaŵi zonse mfumu ikamaloŵa m'Nyumba ya Chauta, alondawo ankatenga zishangozo, kenaka nkumazibwezera ku chipinda cha alonda.
29Tsono ntchito zina za Mfumu Rehobowamu, ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
30Panali nkhondo zosalekeza pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu.
31Ndipo Rehobowamu adamwalira, naikidwa mu mzinda wa Davide m'manda momwe adaikidwa makolo ake. Mai wake uja anali Naama, wa mtundu wa Aamoni. Ndipo Abiya, mwana wa Rehobowamu, adaloŵa ufumu m'malo mwa bambo wake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.