Mk. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu amkana Yesu ku Nazarete(Mt. 13.53-58; Lk. 4.16-30)

1Yesu adachoka kumeneko, nakafika kumudzi kwao. Ophunzira ake adatsagana naye.

2Litafika tsiku la Sabata, Iye adayamba kuphunzitsa m'nyumba yamapemphero. Anthu ambiri amene ankamvetsera adadabwa kwambiri nkumanena kuti, “Kodi Iyeyu zonsezi adazitenga kuti? Nzeru zimene adalandirazi nzotani? Akutha bwanji kuchita zinthu zamphamvu zotere?

3Kodi ameneyu si mmisiri wa matabwa uja, mwana wa Maria? Kodi abale ake si Yakobe, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Kodi suja alongo ake ali nafe pompano?” Choncho adakhumudwa naye.

4Yoh. 4.44Koma Yesu adaŵauza kuti, “Mneneri amalemekezeka kwina kulikonse, kupatula kumudzi kwao, pakati pa achibale ake, ndiponso kubanja kwao.”

5Motero sadathe kuchita zinthu zamphamvu kumeneko. Adangosanjika manja pa odwala oŵerengeka, nkuŵachiritsa.

6Ndipo adadabwa poona kuti anthu akumeneko sadamkhulupirire. Pambuyo pake Yesu adapita ku midzi yozungulira, namakaphunzitsa anthu.

Yesu atuma ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja(Mt. 10.5-15; Lk. 9.1-6)

7Yesu adaitana ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵatuma aŵiriaŵiri. Adaŵapatsa mphamvu zotulutsira mizimu yoipitsa anthu.

8Adaŵalamula kuti, “Musatenge kanthu kena kalikonse pa ulendo, koma ndodo yokha. Musatenge kamba, kapena thumba lapaulendo, kapena ndalama m'chikwama.

9Nsapato muvale inde, koma musakhale ndi mikanjo iŵiri.”

10Adaŵauzanso kuti, “Mukafika pa mudzi, muzikhala nao kunyumba kumene mudafikirako, mpaka itakwana nthaŵi yoti muchoke kumudziko.

11Ntc. 13.51

Lk. 10.4-11Ngati kumudzi kwina anthu sakulandirani, nakana kumva mau anu, pochoka musanse fumbi la kumapazi kwanu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro choti apalamula.”

12Ophunzira aja adapitadi, namakalalikira anthu kuti atembenuke mtima.

13Yak. 5.14Ankatulutsa mizimu yoipa yocholuka, ndiponso ankadzoza mafuta anthu odwala ambiri nkumaŵachiritsa.

Za imfa ya Yohane Mbatizi(Mt. 14.1-12; Lk. 9.7-9)

14 Mt. 16.14; Mk. 8.28; Lk. 9.19 Mfumu Herode adaazimva zimenezi, pakuti mbiri ya Yesu inali itamveka ponseponse. Anthu ena ankati, “Yohane Mbatizi uja adauka kwa akufa, nkuwona akuchita zamphamvu zonsezi.”

15Koma ena ankati, “Iyai, ameneyu ndi Eliya.” Enanso ankati, “Iyai, koma ndi mneneri wonga aneneri akale aja.”

16Pamene Herode adamva zimenezi, adati, “Yohane yemwe ndidamdula pakhosi uja ndiye adauka kwa akufayu.”

17Lk. 3.19, 20Pajatu Herode kale adaatuma asilikali ake kuti akagwire Yohane, akammange ndi kumponya m'ndende. Adaachita zimenezi chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo, mbale wake. Ndiye kuti Herode anali atamkwatira maiyo.

18Ndipo Yohane adaamuuza kuti, “Nkulakwira Malamulo kulanda mkazi wa mbale wanu.”

19Tsono Herodiasiyo ankadana naye Yohane, ndipo ankafuna kuti aphedwe basi. Koma ankalephera,

20chifukwa Herode ankaopa Yohane, podziŵa kuti anali munthu wolungama ndi woyera mtima. Choncho ankamusunga bwino. Ankakonda kumamvetsera mau ake, ngakhale kuti akamumva choncho, ankathedwa nzeru.

21Koma pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, Herodiasi adapezerapo mwai. Herodeyo adakonza phwando, naitana akuluakulu a Boma, ndi akulu olamulira asilikali, ndi anthu omveka a ku Galileyako.

22Tsono mwana wamkazi wa Herodiasi adaloŵa, nayamba kuvina. Kuvinako adakondweretsa nako kwambiri Herode ndi amene adaali naye paphwandopo. Pamenepo mfumuyo idauza mtsikanayo kuti, “Undipemphe chilichonse chimene ukufuna, ine ndikupatsa.”

23Ndipo adatsimikiza molumbira kuti, “Chilichonse chomwe uti undipemphe, ndikupatsa ndithu, ngakhale kukudulira dziko langa lino pakati.”

24Mtsikanayo adatuluka nakafunsa mai wake kuti, “Kodi ndikapemphe chiyani?” Mai wakeyo adati “Kapemphe mutu wa Yohane Mbatizi.”

25Mtsikana uja adabwerera msanga kwa mfumu nanena kuti, “Ndifuna kuti tsopano pompano mundipatse mutu wa Yohane Mbatizi m'mbale.”

26Pamenepo mfumu Herode adamva chisoni kwambiri. Koma chifukwa cha malumbiro ake ndiponso chifukwa cha anthu oitanidwa ku phwando aja, sadafune kuphwanya lonjezo lake kwa mtsikanayo.

27Choncho nthaŵi yomweyo adatuma mmodzi mwa asilikali ake, namulamula kuti abwere nawo mutu wa Yohanewo. Msilikaliyo adapita ku ndende, nakamdula mutu Yohaneyo.

28Adaika mutu wakewo m'mbale nkubwera nawo, naupereka kwa mtsikana uja, mtsikanayo nkukaupereka kwa mai wake.

29Ophunzira a Yohane atamva zimenezi, adabwera nadzatenga mtembo wake nkukauika m'manda.

Yesu adyetsa anthu oposa zikwi zisanu(Mt. 14.13-21; Lk. 9.10-17; Yoh. 6.1-14)

30Atumwi aja adabwerera kwa Yesu namufotokozera zonse zimene adaachita ndi kuphunzitsa.

31Yesu adaŵauza kuti, “Tiyeni tipite kwatokha kumalo kosapitapita anthu, kuti mukapumule pang'ono.” Adaatero chifukwa anthu anali piringupiringu, mwakuti iwo sankatha kupeza ndi mpata wodyera womwe.

32Tsono adaloŵa m'chombo napita kwaokha kumalo kosapitapita anthu.

33Komabe anthu ambiri adaŵaona akupita, naŵazindikira. Motero adathamanga pa mtunda kuchokera ku mizinda yonse, nakafika kumaloko, Yesu ndi ophunzira ake aja asanafike.

34Num. 27.17; 1Maf. 22.17; 2Mbi. 18.16; Ezek. 34.5; Mt. 9.36Pamene Yesu adatuluka m'chombomo, adaona chikhamu chachikulu cha anthu. Adaŵamvera chifundo anthuwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa, choncho adayamba kuŵaphunzitsa zambiri.

35Nthaŵi yamadzulo ophunzira ake adadzamuuza kuti, “Kunotu nkuthengo, ndipo ano ndi madzulo.

36Auzeni anthuŵa azipita, anke ku midzi ili pafupiyi kuti azikagula chakudya.”

37Koma Yesu adaŵauza kuti, “Inuyo apatseni chakudya.” Iwo adati, “Ndiyetu pafunika kuti tikagule buledi wa ndalama mazana aŵiri kuti tidzaŵadyetse anthu onseŵa!”

38Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Muli ndi buledi mngati? Takaonani.” Atakaona adati, “Alipo buledi msanu ndi nsomba ziŵiri.”

39Tsono Yesu adalamula kuti anthu onse aja akhale pansi m'magulumagulu pa msipu.

40Anthu aja adakhaladi pansi, m'magulu mwina anthu makumi khumi, mwina anthu makumi asanu.

41Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti akagaŵire anthuwo.

42Anthu onse aja adadya mpaka kukhuta.

43Pambuyo pake ophunzira aja adatola zotsala za buledi ndi za nsomba zija nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri.

44Mwa anthu amene adaadya bulediyo amuna okha adaalipo zikwi zisanu.

Yesu ayenda pa madzi(Mt. 14.22-33; Yoh. 6.15-21)

45Madzulo omwewo Yesu adalamula ophunzira ake kuti aloŵe m'chombo, atsogole kunka ku tsidya la ku Betsaida, pamene Iye akuuza anthu kuti azipita kwao.

46Tsono atatsazikana nawo anthu aja, Iye adakwera ku phiri kukapemphera.

47M'mene kunkayamba kuda, nkuti chombo chija chili pakati pa nyanja, Yesu ali yekha pa mtunda.

48Ndiye adaona ophunzira aja akuvutika ndi kupalasa chombo, chifukwa anali atayang'anana ndi mphepo. M'mamaŵa kukali mbuu, Yesu adadza kwa iwo, Iye akuyenda pa madzi panyanjapo, nkumafuna kuŵapitirira.

49Koma ophunzira aja, pomuwona akuyenda pa madzi, adaaganiza kuti ndi mzukwa, nayamba kukuwa.

50Onsewotu atamuwona adaaopsedwa. Koma nthaŵi yomweyo Yesu adaŵauza kuti, “Khazikani mtima pansi, ndine, musaope.”

51Pamenepo adaloŵa m'chombomo, mphepo nkuleka. Iwowo adathedwa nzeru kwabasi,

52chifukwa anali asanamvetse bwino za buledi zija. Mitu yao idaali youma.

Yesu achiritsa odwala ku Genesarete(Mt. 14.34-36)

53Yesu ndi ophunzira ake adaoloka nyanja, nakafika ku Genesarete, nkuimitsa chombo kumeneko.

54Pamene iwo adatuluka m'chombomo, nthaŵi yomweyo anthu adamzindikira Yesu.

55Adathamangira ku midzi ya kufupi ndi kumeneko, nayamba kumabwera ndi anthu odwala pa machira, kudza nawo kumene ankamva kuti Yesu ali uku.

56Kulikonse kumene Yesu ankapita, ku midzi ndi ku mizinda, anthu ankadzakhazika odwala pa mabwalo. Ankamupempha kuti aŵalole odwalawo kungokhudza ngakhale mphonje ya chovala chake. Mwakuti onse amene ankaikhudza, ankachira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help