Afi. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za chilungamo chenicheni

1Abale anga, potsiriza ndikuti, “Muzikondwa mwa Ambuye.” Kukulemberaninso mau omwewo sikondilemetsa, ndipo mauwo ngokuthandizani kukhala osakayika.

2Chenjera nawoni ochita zaugalu aja, ndiye kuti ochita zoipa, anthu omangodula thupi chabe.

3Paja ifeyo ndiye oumbala enieni, ife amene timapembedza Mulungu motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Timanyadira Khristu Yesu, osadalira miyambo ya thupi chabe.

4Komabetu ineyo ndikadatha kudalira miyambo yathupiyi. Ngati alipo wina woganiza kuti ali ndi chifukwa chodalira miyambo yathupi yotere, ineyo ndili ndi chifukwa choposa apo.

5Aro. 11.1; Ntc. 23.6; 26.5 Pajatu ine ndidaumbalidwa pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditabadwa. Ndine wa mtundu wa Israele, wa fuko la Benjamini, Mhebri weniweni wobadwa mwa makolo achihebri. Kunena za Malamulo achiyuda, ndinali wa gulu la Afarisi.

6Ntc. 8.3; 22.4; 26.9-11 Ndipo changu changa chinali chachikulu, kotero kuti ndinkazunza Mpingo. Kunena za chilungamo chopezeka pakutsata Malamulo, ineyo ndinali wopanda cholakwa.

7Koma chifukwa cha Khristu, zomwe kale ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziwona kuti nzosapindula.

8Zoonadi, zonse ndikuziwona kuti nzosapindulitsa poziyerekeza ndi phindu lopambana la kudziŵa Khristu Yesu, amene ndi Ambuye anga. Chifukwa cha Khristuyo ndidalolera kutaya zonse, nkumaziyesa zinyalala, kuti potero phindu langa likhale Khristu,

9Iye ndi ine tikhale amodzi. Sindiyesanso pandekha kukhala wolungama pakutsata Malamulo, koma ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu, chochilandira pakukhulupirira.

10Chimene ndikufuna nchakuti ndidziŵe Khristu, ndiponso mphamvu zimene zidamuukitsa kwa akufa. Ndikufunanso kumva zoŵaŵa pamodzi naye ndi kufanafana naye pa imfa yake.

11Ndikuyesetsa kuchita zimenezi pokhulupirira kuti inenso ndidzakhala ndi moyo wosatha podzauka kwa akufa.

Zu kuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵiro

12Sindikunena kuti ndafikapo kale pa zimenezi, kapena kuti ndine wangwiro kale. Koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuzipata pakuti ndicho chinali cholinga cha Yesu Khristu pakundikopa kuti ndikhale wake.

13Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo.

14Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.

15Tsono ife tonse amene tili okhwima pa moyo wathu wauzimu, tikhale ndi mtima womwewo. Ngati pa zinthu zina muli ndi maganizo osiyana ndi ameneŵa, pameneponso Mulungu adzakuunikirani.

16Koma ngakhale zitani, tisatayepo kanthu pa zoona zimene takhala tikuzikhulupirira mpaka tsopano.

17 1Ako. 4.16; 11.1 Abale anga, nonse pamodzi muzinditsanzira ine, ndipo muziŵapenyetsetsa amene amayenda motsata chitsanzo chimene ife timakupatsani.

18Ndakhala ndikukuuzani kaŵirikaŵiri, ndipo tsopano ndikubwerezanso molira misozi, kuti pali ambiri amene mayendedwe ao akutsimikiza kuti amadana ndi mtanda wa Khristu.

19Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha.

20Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu.

21Iyeyo adzasandutsa matupi athu achabeŵa kuti akhale ofanafana ndi thupi lake laulemerero. Adzachita zimenezi ndi mphamvu zake zomwe zija zimene angathenso kugonjetsa nazo zinthu zonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help