Mas. 30 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ndidzakutamandani, Inu Chauta,

pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa.

Simudalole kuti adani anga akondwere

poona kuti ndikuvutika.

2Chauta, Mulungu wanga, ndidalirira Inu

kuti mundithandize,

ndipo mwandichiritsa.

3Inu Chauta, mwanditulutsa m'dziko la akufa,

mwandibwezeranso moyo kuti ndingatsikire ku manda.

4Imbani nyimbo zotamanda Chauta,

inu anthu ake oyera mtima,

mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera.

5Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe,

koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse.

Misozi ingachezere kugwa usiku,

m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

6Koma ine, pamene zinthu zidaandiyendera bwino,

ndidati, “Sindidzagwedezeka konse.”

7Chifukwa cha kukoma mtima kwanu, Inu Chauta,

mudandikhazikitsa ngati phiri lolimba.

Koma pamene mudandimana madalitso anu,

ine ndidataya mtima.

8Pamenepo ndidalirira Inu Chauta,

ndipo ndidapempha chifundo chanu kuti,

9“Kodi mudzapindulanji pa imfa yanga

ngati nditsikira ku manda?

Kodi ine nditasanduka fumbi,

ndingathe kukutamandani?

Kodi pamenepo ndingathe kulalika za kukhulupirika kwanu?

10“Imvani, Inu Chauta,

ndipo mundikomere mtima.

Inu Chauta, mukhale mthandizi wanga.”

11Mwasandutsa kulira kwanga

kuti kukhale kuvina,

mwachotsa chisoni changa

ndi kundipatsa chisangalalo.

12Choncho ndisakhale chete,

koma ndikutamandeni ndi mtima wonse.

Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza,

Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help