1Thokozani Chauta,
tamandani dzina lake,
lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.
2Imbirani Chauta,
muimbireni nyimbo zomtamanda,
lalikani za ntchito zake zodabwitsa.
3Munyadire dzina lake loyera.
Ikondwe mitima ya anthu
amene amapembedza Chauta.
4Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake.
Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza.
5Inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
ana a Yakobe, osankhidwa ake,
6musaiŵale ntchito zodabwitsa ndi zozizwitsa
zimene ankazichita,
ndiponso m'mene ankaweruzira anthu.
7Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu,
amalamulira dziko lonse lapansi.
8Amasunga chipangano chake nthaŵi zonse,
sangaiŵale lamulo limene adalipereka ku mibadwo yonse.
9 Gen. 12.7; 17.8; Gen. 26.3 Amasunga chipangano chimene adachita ndi Abrahamu,
lonjezo lake limene adapatsa Isaki molumbira.
10 Gen. 28.13 Lonjezolo adabwerezanso kwa Yakobe
kuti likhale chipangano chokhazikika
mu Israele mpaka muyaya.
11Adati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani
kuti likhale choloŵa chako chokhalira iweyo.”
12Pamene anali anthu oŵerengeka,
anthu osatchuka, ongokhala nawo m'dzikomo,
13omangoyendayenda kuchokera ku mtundu wina wa anthu
kupita ku mtundu wina,
kuchokera ku ufumu wina kupita ku ufumu wina,
14 Gen. 20.3-7 sadalole ndi mmodzi yemwe kuti aŵapsinje,
adalanga mafumu ena chifukwa cha anthu akewo.
15Adati,
“Musakhudze odzozedwa anga,
musaŵachite choipa aneneri anga.”
16 Gen. 41.53-57 Pamene Chauta adadzetsa njala m'dziko la Kanani
ndi kuwononga chakudya chonse,
17 Gen. 37.28; 45.5 Iye anali atatuma munthu patsogolo pa anthu ake,
Yosefe uja amene adagulitsidwa ngati kapolo.
18 Gen. 39.20—40.23 Mapazi ake adapwetekedwa ndi matangadza,
khosi lake lidavekedwa unyolo,
19mpaka zimene Yosefe adanena zija zidachitikadi.
Mau a Chauta adatsimikiza kuti iye sadalakwe.
20 Gen. 41.14 Motero mfumu idalamula kuti akammasule,
wolamulira mitundu ya anthuyo adammasuladi.
21 Gen. 41.39-41 Adamsandutsa mbuye wa nyumba yake,
ndi wolamulira chuma chake chonse,
22kuti azilangiza nduna zake monga momwe ankafunira,
ndi kuŵaphunzitsa nzeru akuluakulu.
23 Gen. 46.6; Gen. 47.11 Tsono Israele adafika ku Ejipito.
Yakobeyo adakhala nawo m'dziko la Hamu.
24 Eks. 1.7-14 Chauta adalola kuti anthu ake achuluke,
naŵasandutsa amphamvu kupambana adani ao.
25Adaumitsa mitima ya adaniwo
kuti adane ndi anthu ake
ndi kuŵapanganirana zaupandu.
26 Eks. 3.1—4.17 Kenaka adatuma Mose mtumiki wake
pamodzi ndi Aroni amene adamsankha.
27Iwo adachita zizindikiro m'dzina lake
pakati pa anthuwo,
adachita ntchito zozizwitsa m'dziko la Hamu.
28 Eks. 10.21-23 Chauta adatumiza mdima,
nasandutsa dzikolo kuti likhale lamdima.
Komabe anthuwo adakaniratu mau a Chauta.
29 Eks. 7.17-21 Iye adasandutsa madzi ao kukhala magazi,
ndipo nsomba zao zidafa.
30 Eks. 8.1-6 Dziko lao lidadzaza ndi achule,
ngakhale m'zipinda za mafumu zomwe.
31 Eks. 8.20-24; Eks. 8.16, 17 Adalankhula, ndipo kudatuluka ntchentche zochuluka,
mtundu wa udzudzu udaloŵa m'dziko mwao monse.
32 Eks. 9.22-25 Adaŵagwetsera matalala m'malo mwa mvula,
adaŵagwetsera ching'aning'ani
chimene chinkang'anima m'dziko mwao monse.
33Adagwetsa mipesa yao ndi mikuyu yao,
adathyola mitengo yonse ya m'dziko mwao.
34 Eks. 10.12-15 Adalankhula, ndipo kudafika dzombe
ndi mandowa osaŵerengeka,
35amene adaononga zomera zonse za m'dziko mwao,
nadya zipatso zonse za m'minda mwao.
36 Eks. 12.29 Iye adapha ana onse achisamba m'dziko mwao,
ana onse oyamba, oŵabala akadali abiriŵiri.
37 Eks. 12.33-36 Kenaka Chauta adaŵatulutsa Aisraele
atatenga siliva ndi golide,
pakati pa mafuko awo panalibe amene adafooka.
38Aejipito adasangalala pamene iwo adapita,
chifukwa ankachita nawo mantha anthuwo.
39 Eks. 13.21, 22 Chauta adaika mtambo kuti uziphimba anthu ake,
adaika moto kuti uziŵaunikira usiku.
40 Eks. 16.2-15 Iwo adapempha chakudya,
ndipo Chauta adatumiza zinziri,
adaŵapatsa buledi wambiri wochokera kumwamba.
41 Eks. 17.1-7; Num. 20.2-13 Adatsekula thanthwe, madzi nkutumphuka.
Madziwo adayenda m'chipululu ngati mtsinje.
42Monsemo ankakumbukira lonjezo lake loyera
limene adaachitira Abrahamu mtumiki wake.
43Motero Chauta adaŵatulutsa anthu ake,
osankhidwa akewo adatuluka ndi chimwemwe akuimba.
44 Yos. 11.16-23 Adaŵapatsa maiko a mitundu ina ya anthu,
adalanda minda ya anthu ena kuti ikhale yao.
45Potero Chauta adafuna
kuti anthu ake azisunga malangizo
ndi kumatsata malamulo ake onse.
Tamandani Chauta!
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.