Mas. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ulemerero wa Mulungu m'zolengedwa zakeKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la Davide.

1Zakumwamba zimalalika ulemerero wa Mulungu,

thambo limasonyeza ntchito za manja ake.

2Usana umasimbira zimenezo usana unzake,

usiku umadziŵitsa zimenezo usiku unzake.

3Palibe kulankhula, palibe kunena mau aliwonse.

Liwu lao silimveka konse.

4 Aro. 10.18 Komabe uthenga wao umafalikira

pa dziko lonse lapansi.

Mau aowo amafika mpaka ku mathero a dziko.

Mulungu adamangira dzuŵa nyumba m'thambomo.

5Dzuŵalo limatuluka ngati mkwati wokondwa

amene akutuluka m'nyumba mwake,

ndipo limayenda ndi chimwemwe

ngati ngwazi yamphamvu.

6Limatuluka kuyambira ku mathero ena a thambo,

ndi kuzungulira mpaka ku mathero enanso.

Palibe chinthu chilichonse chotha kulewa kutentha kwake.

Malamulo a Chauta

7Mau a Chauta ngangwiro,

amapatsa munthu moyo watsopano.

Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika,

umaŵapatsa nzeru amene alibe.

8Malangizo a Chauta ndi olungama,

amasangalatsa mtima.

Malamulo a Chauta ndi olungama,

amapatsa mtima womvetsa.

9Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro,

chimakhala mpaka muyaya.

Chiweruzo cha Chauta nchoona,

ncholungama nthaŵi zonse.

10Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide,

ngakhale golide wambiri wamtengowapatali,

nzotsekemera kupambana uchi,

ngakhale uchi wozuna kwambiri.

11Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu,

poŵasunga ndimalandira mphotho yaikulu.

12Nanga ndani angathe kudziŵa zolakwa zake?

Inu Chauta, mundichotsere zolakwa zanga zobisika.

13Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala,

kulakwa koteroku ndisakutsate.

Tsono ndidzakhala wangwiro

wopanda mlandu wa uchimo waukulu.

14Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu,

Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help