2 Mbi. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 2Sam. 8.11; 1Mbi. 18.11 Motero Solomoni adatsiriza ntchito zonse za ku Nyumba ya Mulungu. Tsono adabwera ndi zinthu zonse zimene Davide bambo wake adaazipereka, ndipo adaika siliva, golide ndi ziŵiya zonse m'zipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Chauta.

Bokosi lachipangano abwera nalo ku Nyumba ya Chauta(1 Maf. 8.1-9)

2 2Sam. 6.12-15; 1Mbi. 15.25-28 Pambuyo pake Solomoni adasonkhanitsa akuluakulu onse a Aisraele, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraele. Onsewo adasonkhana ku Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta, kulichotsa ku Ziyoni, mzinda wa Davide.

3Aisraele onse adasonkhana pamaso pa mfumu nthaŵi ya chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiŵiri.

4Tsono atsogoleri onse a Aisraele atabwera, Alevi adanyamula Bokosi lachipangano lija.

5Adabwera nalo Bokosilo pamodzi ndi chihema chamsonkhano ndiponso ziŵiya zonse zopatulika zimene zinali m'chihemamo. Ansembe ndi Alevi ndiwo amene adabwera nazo zimenezo.

6Pamenepo mfumu Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la Aisraele amene adaasonkhana pamaso pake, ataima patsogolo pa Bokosi lachipanganolo, ankapereka nsembe za nkhosa ndi ng'ombe zosaŵerengeka.

7Tsono ansembe adafika nalo Bokosi lachipangano la Chauta lija ku malo ake a m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, ku malo opatulika kopambana naliika kunsi kwa mapiko a akerubi.

8Choncho akerubiwo ankatambasula mapiko ao pamwamba pa Bokosilo, kotero kuti ankaliphimba pamodzi ndi mphiko zake zonyamulira.

9Mphikozo zinali zazitali kwambiri, kotero kuti nsonga zake zinkaonekera kukhalira ku malo opatulika kopambana patsogolo pa malo opatulika am'kati mwenimweni. Koma kunja sizinkaonekera. Ndipo zili komweko mpaka pano.

10Deut. 10.5 M'Bokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iŵiri yokha ija imene Mose adaaikamo ku Horebu, kumene Chauta adaachita chipangano ndi Aisraele, iwowo atatuluka ku Ejipito.

111Mbi. 16.34; 2Mbi. 7.3; Eza. 3.11; Mas. 100.5; 106.1; 107.1; 118.1; 136.1; Yer. 33.11

Eks. 40.34, 35Tsono ansembe adatulukamo m'malo opatulikawo (poti ansembe onse amene analipo anali atadziyeretsa, osayang'aniranso magulu ao.)

12Pamenepo Alevi onse amene ankaimba nyimbo, Asafu, Hemani ndi Yedutuni, ana ao pamodzi ndi abale ao, ovala nsalu za bafuta wambee, ali ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe, adaimirira cha kuvuma kwa guwa, pamodzi ndi ansembe okwanira 120 amene ankaimba malipenga.

13Ndipo ntchito ya anthu oimba malipengawo ndi ya anthu oimba nyimbo aja, inali yakuti azimveketsa mau amodzi potamanda ndi kuthokoza Chauta, ndipo ankaimba nyimboyo ndi kuliza malipenga, ziwaya zamalipenga ndiponso zoimbira zina, kutamanda Chauta ndi mau akuti,

“Ndithu Chauta ndi wabwino,

pakuti chikondi chake chosasinthika

chimakhala mpaka muyaya.”

Apo Nyumbayo, Nyumba ya Chauta, idadzaza ndi mtambo,

14ndipo ansembe sankatha kuimirira kuti agwire ntchito yao yotumikira, chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Chauta unali utadzaza m'Nyumba ya Chautayo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help