1
2“Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwira Chauta chifukwa cha kunyenga mnzake pomakana kumubwezera mnzakeyo zimene adamsungiza, kapena kumubera, kapena kumnyenga,
3kapena kunama kuti sadatole zimene zidatayika, kapena kumalumbira zonama pa kanthu kalikonse,
4munthu akachimwa pa zimenezi ndi wopalamula ndithu, abweze zimene adalandazo, zimene adatenga monyengazo, zomsungizazo, ndi zotayika zimene adatolazo.
5Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, abweze zonsezo ndi kuwonjezapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse, tsono amubwezere mwini wakeyo.
6Ndipo nsembe yopepesera kupalamula, yopereka kwa Chauta, abwere nayo kwa wansembe. Ikhale nkhosa yamphongo yopanda chilema, mtengo wake wa nkhosayo ukhale wokwanira mtengo woikidwa wa nyama ya nsembe yopepesera kupalamula.
7Tsono wansembe achite mwambo wopepesera machimo a munthuyo pamaso pa Chauta, ndipo zonse zimene wochimwayo adachita napalamula pakutero, zidzakhululukidwa.”
Nsembe yopsereza kwathunthu8Chauta adauza Mose kuti,
9“Ulamule Aroni pamodzi ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza kwathunthu ndi ili: nsembeyo izikhala pa moto pa guwa usiku wonse mpaka m'maŵa, ndipo moto wapaguwapowo uzikhala uli chiyakire.
10Tsono wansembe avale mkanjo wake wabafuta, avalenso kabudula wabafuta, ndipo atengeko phulusa la nyama yopsereza pa guwa ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo.
11Tsono avule zovala zake, avale zina, ndipo aole phulusalo nkukaliika pa malo oyeretsedwa kunja kwa mahema.
12Moto wapaguwa uzikhala uli chiyakire, usazime. Wansembe azisonkhezera motowo ndi nkhuni m'maŵa mulimonse, ndipo aziyala nsembe yopsereza paguwapo, ndi kupserezapo mafuta a nsembe zachiyanjano.
13Moto ukhale uli chiyakire paguwapo, usazime.’ ”
Za nsembe yaufa14“Lamulo la chopereka cha chakudya ndi ili: ana a Aroni aipereke nsembeyo pamaso pa Chauta patsogolo pa guwa.
15Tsono mmodzi atapeko dzanja limodzi la ufa wosalala woperekedwa ku nsembeyo, pamodzi ndi mafuta ndi lubani yense amene ali pa chopereka cha chakudyacho. Azitenthe pa guwa, kuti zikhale chikumbutso, ndipo zitulutse fungo lokomera Chauta.
16Tsono Aroni ndi ana ake adye zimene zatsalapo. Zikhale zosafufumitsa, ndipo azidyere pa malo oyera, ndiye kuti pa bwalo la chihema chamsonkhano.
17Poziphika asathiremo chofufumitsira. Ndaŵapatsa zotsalazo kuti zikhale gawo lao la nsembe zanga zopsereza. Zonsezo nzoyera kwambiri monga nsembe yopepesera machimo, ndiponso nsembe yopepesera kupalamula.
18Ana onse aamuna a Aroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Chauta, monga kudalembedwa kuti zidzatero nthaŵi zonse pa mibadwo yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudze guwalo chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.”
19Chauta adauza Mose kuti,
20“Nsembe imene Aroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Chauta pa tsiku limene wansembe adzozedwa, izikhala yotere: apereke ufa wosalala wokwanira kilogaramu limodzi ngati chopereka cha chakudya cha nthaŵi zonse. Apereke theka limodzi m'maŵa, ndipo linalo apereke madzulo.
21Ipangidwe ndi mafuta pa chiwaya. Ubwere nacho ili yosakaniza bwino, yophikidwa mitandamitanda monga amachitira ndi chopereka cha chakudya. Ndipo aipereke kuti itulutse fungo lokomera Chauta.
22Tsono wansembe wa fuko la Aroni amene wadzozedwa kuti aloŵe m'malo mwake, aipereke kwa Chauta nthaŵi zonse monga kudalembedwera. Aipsereze nsembe yonse poti lamulo ndi lamuyaya.
23Chopereka cha chakudya chilichonse cha wansembe chikhale chopsereza kwathunthu, asachidye ai.”
Nsembe yopepesera machimo24Chauta adauza Mose kuti,
25“Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopepesera machimo ndi ili: pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza, aphereponso nsembe yopepesera machimo kwa Chauta. Imeneyo ndi nsembe yoyera kopambana.
26Wansembe amene aiperekere machimoyo, adye nyamayo. Aidyere pa malo oyera, pa bwalo la chihema chamsonkhano.
27Aliyense wokhudza nsembeyo adzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake. Tsono magazi ake akagwera pa chovala, muchape chovalacho pa malo oyera.
28Ndipo auphwanye mphika wadothi umene adaphikamo nyamayo. Koma akaphika wamkuŵa, autsuke mphikawo ndi kuutsukuluza ndi madzi.
29Munthu wamwamuna aliyense wa m'banja la ansembe angathe kudyako. Imeneyo ndiyo nsembe yoyera kopambana.
30Koma asadye nyama ya nsembe yopepesera machimo imene magazi ake amabwera nawo ku chihema chamsonkhano, kudzapepesera machimo ku malo oyera. Aitenthe pa moto imeneyo.’
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.