Amo. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mau odandaulira Israele

1Inu banja la Israele imvani mau aŵa,

amene ndikukuuzani mwadandaulo:

2“Namwali Israele wagwa chonse

osati nkudzukanso ai.

Wagwa ndi kuiŵalika pa dziko lake,

popanda wina womdzutsa.”

3Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi:

“Mzinda umene udapita ku nkhondo ndi

anthu chikwi udzatsala ndi anthu zana limodzi chabe.

Ndipo umene udapita ku nkhondo ndi anthu zana limodzi,

udzatsala ndi anthu khumi okha a m'banja la Israele.”

Chauta afuna kuti anthu atembenuke mtima

4Mau a Chauta ouza banja la Israele ndi aŵa:

“Muchite zimene Ine ndifuna,

kuti mukhalebe ndi moyo,

5koma musasonkhane ku Betele,

ndipo musakaloŵe ku Giligala,

kapena kuwolokera ku Beereseba.

Ndithu a ku Giligala adzatengedwa kupita ku ukapolo,

ndipo Betele adzaonongekeratu.”

6Muchite zimene Chauta afuna,

kuti mukhalebe ndi moyo.

Mukapanda kutero,

adzatentha banja la Yosefe ngati moto,

ndipo motowo udzapsereza a ku Betele

popanda wina wouzimitsa.

7Tsoka kwa inu amene mumasandutsa

chilungamo kuti chikhale choipa,

inu amene mumanyoza zolungama.

8 Yob. 9.9; 38.31 Iye uja ndiye amene adalenga nyenyezi

za Akamwiniatsatana ndiponso Nsangwe,

ndiye amene amasandutsa mdima

kuti ukhale m'maŵa

nasandutsa usana

kuti ukhale usiku.

Ndiye amene amaitana madzi am'nyanja

ndi kuŵathira pa dziko lapansi.

Dzina lake ndi Chauta.

9Ndiyenso amene amakantha olamulira ankhanza,

ndiye amene amagumula malinga ao.

10Inu mumadana ndi muweruzi wodzudzula zosalungama,

mumanyansidwa ndi wokamba zoona pa bwalo lamilandu.

11Mumapondereza anthu osauka

ndi kuŵabera pa msonkho.

Nchifukwa chake

ngakhale mwamanga nyumba za miyala yosema,

simudzakhalamo.

Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa,

simudzamumwa vinyo wake.

12Ine ndikudziŵa kuchuluka kwa zolakwa zanu

ndi kukula kwa machimo anu.

Inu mumazunza anthu ochita chilungamo,

mumalandira ziphuphu

ndiponso mumapotoza milandu ya anthu osauka.

13Nchifukwa chake pa nthaŵi yotere

munthu wanzeru salankhulapo kanthu,

chifukwa ndi nthaŵi yoipa.

14Muike mtima pa zabwino osati pa zoipa,

kuti mukhalebe ndi moyo.

Apo Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse,

adzakhala nanu monga mwaneneramo.

15Muzidana ndi zoipa, muzikonda zabwino.

Mukhazikitse chilungamo m'mabwalo a milandu.

Mwina mwake Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse,

adzakukomerani mtima inu anthu otsala

a m'banja la Yosefe.

16Nchifukwa chake zimene akunena Chauta, Ambuye,

Mulungu Wamphamvuzonse, ndi izi:

“M'mabwalo monse mudzakhala kulira,

ndipo m'miseu monse anthu azidzangoti,

‘Mayo! Mayo!’

Ngakhale anthu wamba adzaŵaitana kuti adzalire,

adzaitananso anthu odziŵa kubuma maliro kuti adzalire.

17M'minda yonse ya mphesa mudzakhala kulira kokhakokha,

pakuti ndidzakulanganidi nonsenu.”

Akuterotu Chauta.

18Tsoka kwa inu amene mumalilakalaka tsiku la Chauta!

Kodi tsiku limenelo lidzakupinduliraninji inuyo?

Kudzakhalatu mdima, osati kuŵala ai.

19Kudzakhala monga m'mene kumachitira

munthu akamathaŵa mkango,

ndipo akumana ndi chimbalangondo,

kapena monga munthu woti wakaloŵa m'nyumba,

atsamira chipupa ndi dzanja lake,

njoka nkumuluma.

20Kodi suja tsiku la Chauta ndi mdima wokhawokha

osati kuŵala,

kodi suja lili ngati usiku wabii

wopanda mpoti mbee pomwe!

21 Yes. 1.11-14 Chauta akuti,

“Masiku anu achikondwerero ndimadana nawo

ndipo ndimaŵanyoza.

Misonkhano yanu yachipembedzo siindikondwetsa konse.

22Ngakhale mudzapereke nsembe zanu

zopsereza ndiponso zaufa,

Ine sindidzazivomera.

Nsembe zanu zachiyanjano zophera ng'ombe zonenepa

sindidzaziyang'ana nkomwe.

23Musandisokose nazo nyimbo zanu zachipembedzo,

sindingathe kupirira kulira kwa azeze anu.

24Koma kuweruza kwanu kwangwiro

kuziyenda kosalekeza ngati madzi,

kulungama kwanu kukhale ngati mtsinje wosaphwa.

25 Ntc. 7.42, 43 “Kodi inu anthu a ku Israele,

zaka makumi anai zimene mudakhala m'chipululu,

mudanditsirirako nsembe ndi kundipatsa mitulo?

26Ndipotu muzidzanyamula Sakuti, mfumu yanu,

ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu,

mafano amene mudadzipangira.

27Pakuti ndidzakupititsani ku ukapolo,

kutali kupitirira mzinda wa Damasiko.”

Akutero Chauta,

amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help