Esr. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Mordekai atamva zonse zimene zidachitikazo, adang'amba zovala zake chifukwa cha chisoni, ndipo adavala chiguduli, nadzola phulusa. Adakaloŵa m'kati mwenimweni mwa mzinda, akulira mokweza mau ndi moŵaŵa mtima kwambiri.

2Adakaima ku chipata cha khoma la mfumu, poti panalibe ndi mmodzi yemwe wololedwa kuloŵa pa khomo la mfumu atavala chiguduli.

3Tsono ku chigawo chilichonse kumene kudaapita malamulo a mfumu aja, kunali chiliro pakati pa Ayuda, ndipo ankasala zakudya ndi kumalira, namadandaula ndi chisoni. Ambiri mwa iwo ankagona pa ziguduli, namadzola phulusa.

Mordekai apempha Estere kuti amthandize

4Pamene adzakazi a Estere, pamodzi ndi adindo ake ofulidwa, adabwera kudzamuuza, mfumukazi uja adavutika kwambiri mu mtima. Adatumiza zovala kuti Mordekai akavale, ndi kuvula chiguduli chake, koma iyeyo sadalole zimenezo.

5Apo Estere adaitana Hataki, mmodzi mwa adindo ofulidwa a mfumu amene adaaikidwa kuti azimtumikira. Adamlamula kuti apite kwa Mordekai, kuti akamve zimene zidachitika, ndiponso kuti zidachitika chifukwa chiyani.

6Hataki adapita kwa Mordekai pa bwalo la mzinda, patsogolo pa chipata cha mfumu.

7Mordekai adamuuza zonse zimene zidaachitikazo. Adamuuzanso chiŵerengero cha ndalama chimene Hamani adaalonjeza kuti adzapereka m'matumba a chuma cha mfumu, kuperekera kuti Ayuda onse aonongedwe.

8Mordekai adampatsanso kalata yaulamuliro yochokera ku Susa yonena kuti Ayuda onse aonongedwe. Adampatsira kalatayo kuti aiwonetse Estere ndi kumufotokozera. Adampempha kuti Estereyo amuuze kuti apite kwa mfumu akaidandaulire ndi kuipemba chifukwa cha anthu ake. Adati akamuuze mau aŵa: “Kumbukira masiku amene unali munthu wamba, paja ndidakulera ndine ndi manja angaŵa. Hamani, nduna yaikulu, wapempha Amfumu kuti ifeyo tiphedwe. Ndiye iwe upemphere kwa Ambuye, ndipo utinenereko kwa Amfumu. Chonde tipulumutse tisaphedwe.”

9Hataki adapita nakamuuza Estere zimene Mordekai adaanena.

10Pamenepo Estere adalankhula ndi Hataki ndipo adampatsa uthenga wokauza Mordekai, wakuti,

11“Atumiki onse a mfumu ndi anthu onse a m'madera a dziko la mfumu amadziŵa kuti mwamuna kapena mkazi aliyense akaloŵa m'bwalo lam'kati la mfumu osaitanidwa, pali lamulo limodzi lokha. Lamulolo ndi ili: onsewo ayenera kuphedwa osasiyanitsa, kupatula yekhayo amene mfumu imloza ndi ndodo yake yaufumu yagolide, kuti akhale ndi moyo. Ndipo ine ndakhala masiku makumi atatu tsopano mfumu osandiitana kuti ndikaonane nayo.”

12Tsono iwo aja adakauza Mordekai zimene Estere adaanena.

13Apo Mordekai adaŵauza kuti abwerere kwa Estere, akamuuze mau aŵa: “Usaganize kuti kunyumba kwa mfumuko iweyo udzapulumuka kupambana Ayuda ena onse.

14Iweyotu ukakhala chete pa nthaŵi yonga imeneyi, ndiye kuti chithandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zidzachokera kwina, koma iwe pamodzi ndi banja la atate ako mudzaonongedwa. Ndipo angadziŵe ndani, mwina mwake iweyo wakwatiwa ndi mfumu chifukwa cha nyengo yonga imeneyi?”

15Pamenepo Estere adauza adindowo kuti akauze Mordekai kuti,

16“Pitani mukasonkhanitse Ayuda onse a ku Susa ndipo akasale zakudya m'malo mwanga. Asakadye kapena kumwa pa masiku atatu usana ndi usiku. Inenso pamodzi ndi anamwali anga tikasala zakudya monga inu nomwe. Pambuyo pake ndidzapita kwa mfumu, ngakhale nkuchimwira lamulo. Ngati nkufa, ndife.”

17Motero Mordekai adapita nakachita zonse monga momwe Estere adaamuuzira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help