1Pambuyo pake Yesu adanka nayendera mizinda ndi midzi akulalika ndi kuuza anthu Uthenga Wabwino wonena za ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja anali naye.
2 limene lidapenyana ndi Galileya.
27Pamene Yesu adafika pa mtunda, munthu wina wochokera ku mudzi wakomweko, adadzakumana naye. Munthuyo adaali ndi mizimu yoipa, ndipo kuyambira kale sankavalanso zovala. Sankakhala m'nyumba, koma ku manda.
28Pamene iye adaona Yesu, adafuula nadzigwetsa ku mapazi ake, ndipo adanena mokweza mau kuti, “Kodi ndakuputani chiyani Inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wopambanazonse? Ndakupembani, musandizunze.”
29Adaatero chifukwa Yesu anali atalamula mzimu woipawo kuti utuluke mwa munthuyo. (Ndiye kuti kaŵirikaŵiri ukamugwira, anthu ankamumanga manja ndi maunyolo, nkumumanganso miyendo ndi zitsulo kuti amugwiritse bwino. Koma iyeyo ankazingomwetsula zomangirazo, ndipo mzimuwo unkamupirikitsira ku thengo.)
30Tsono Yesu adamufunsa munthuyo kuti, “Dzina lako ndani?” Iye adayankha kuti, “Dzina langa ndine Chigulu,” chifukwa mizimu yoipa yochuluka inali itamuloŵa.
31Kenaka mizimuyo idapempha Yesu kuti asailamule kuti ikaloŵe ku chiphompho chao.
32Pafupi pomwepo, pachitunda poteropo, pankadya gulu lalikulu la nkhumba. Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti ailole ikaloŵe m'nkhumbazo. Yesu adailoladi.
33Iyo idatuluka, nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo.
34Oŵeta nkhumbazo ataona zimenezi, adathaŵa, nakauza anthu ku mzinda ndi ku midzi.
35Anthuwo adatuluka kuti akaone zimene zidaachitikazo. Atafika kumene kunali Yesuko, adapeza munthu amene adaamtulutsa mizimu yoipa uja, atakhala pansi ku mapazi a Yesu, atavala, misala ija itatha. Anthuwo adagwidwa ndi mantha.
36Anzao amene adaaonerera zonse zikuchitika, adaŵasimbira m'mene munthu wamizimuyo adaamchiritsira.
37Apo anthu onse a ku malo ozungulira Geregesa adapempha Yesu kuti achoke kumeneko, chifukwa iwo anali ndi mantha aakulu. Choncho Yesu adaloŵa m'chombo, nkumabwerera ku tsidya.
38Munthu amene adaamtulutsa mizimu yoipa uja adapempha Yesu kuti apite nao. Koma Yesu adamubweza namuuza kuti,
39“Iyai, iwe bwerera kwanu, ukafotokoze zazikulu zimene Mulungu wakuchitira.” Munthuyo adapitadi kwao nkumakalengeza mumzinda monse zazikulu zimene Yesu adaamchitira.
Yesu achiza mwana wa Yairo ndi mai wina(Mt. 9.18-26; Mk. 5.21-43)40Pamene Yesu adafikanso ku tsidya, chinamtindi cha anthu chidamchingamira, popeza kuti onse ankamudikira.
41Tsono kudafika munthu wina, dzina lake Yairo, amene anali mmodzi mwa akulu a nyumba yamapemphero. Iye adadzigwetsa ku mapazi a Yesu, nayamba kumdandaulira kuti apite kunyumba kwake,
42chifukwa mwana wake wamkazi anali pafupi kufa. Anali wa zaka khumi ndi ziŵiri, ndipo mwana anali yekhayo.
Pamene Yesu ankapita kumeneko, anthu aja ankamupanikiza.
43Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Adaamwaza chuma chake chonse kulipira asing'anga, koma panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumchiza.
44Iyeyu adafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza mphonje ya chovala chake, ndipodi nthaŵi yomweyo matenda a msambowo adaleka.
45Pompo Yesu adafunsa kuti, “Ndani wandikhudza?” Poti onse ankangoti, “Kaya,” Petro adati, “Aphunzitsi, anthu onseŵa akuzungulirani ndipo akukupanikizani.”
46Koma Yesu adati, “Iyai, wina wandikhudza ndithu. Ndazindikira kuti mphamvu zina zatuluka mwa Ine.”
47Pamene mai uja adaona kuti sangathenso kudzibisa, adadza monjenjemera nadzigwetsa ku mapazi a Yesu. Adafotokoza pamaso pa anthu onse aja chifukwa chimene adaakhudzira Yesu, ndiponso m'mene adachirira nthaŵi yomweyo.
48Apo Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere.”
49Yesu akulankhulabe, kudafika munthu wina kuchokera kunyumba kwa mkulu wa nyumba yamapemphero uja. Adamuuza mkuluyo kuti, “Mwana uja watsirizika. Musaŵavutenso Aphunzitsiŵa.”
50Yesu atamva mauwo adauza Yairo kuti, “Musaope ai, inu mungokhulupira, ndipo mwanayo akhalanso bwino.”
51Pamene Yesu adafika kunyumba kuja, sadalole kuti wina aliyense aloŵe naye, koma Petro, Yohane ndi Yakobe, ndiponso bambo wake wa mwanayo ndi mai wake.
52Anthu onse ankalira ndi kubuma. Koma Yesu adati, “Musalire, mwanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.”
53Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola, chifukwa ankadziŵa kuti mwanayo wamwalira basi.
54Yesu adagwira mwanayo pa dzanja nanena mokweza mau kuti, “Mwana iwe, dzuka!”
55Pomwepo moyo wake udabwereramo, iyeyo nkudzukadi nthaŵi yomweyo. Kenaka Yesu adaŵauza kuti ampatse chakudya mtsikanayo.
56Makolo ake aja adazizwa kwambiri, koma Yesu adaŵalamula kuti asauze wina aliyense zimene zidaachitikazo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.