1 Sam. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kuitanidwa kwa Samuele.

1Mnyamata uja Samuele ankatumikira Chauta, ndipo Eli ankamuyang'anira. Masiku amenewo mau a Chauta sankamveka kaŵirikaŵiri, ndipo kuwona zinthu m'masomphenya sikunkachitikanso kaŵirikaŵiri.

2Tsiku lina Eli anali gone kumalo kwake. Maso ake adaali atayamba kupenya mwachimbuuzi, kotero kuti sankatha kupenya bwino.

3Samuelenso anali gone m'Nyumba ya Chauta kumene kunali Bokosi lachipangano la Chauta. Nthaŵiyo nkuti nyale ya Mulungu isanazime.

4Tsono Chauta adaitana kuti, “Samuele, Samuele!” Iye adayankha kuti, “Ŵaŵa!”

5Adathamangira kwa Eli nati, “Ndabwera, ndamva kuitana.” Koma Eli adati, “Sindidakuitane, kagone.” Motero Samuele adapita kukagona.

6Pambuyo pake Chauta adamuitananso kuti, “Samuele!” Pompo Samuele adadzuka napita kwa Eli nakamuuza kuti, “Ndabwera, ndamva ndithu kuitana.” Koma Eli adati, “Sindidakuitane mwana wanga, kagone.”

7Pamenepo nkuti Samuele asanadziŵe Chauta, ndipo mau a Chauta nkuti asanaululidwe kwa iyeyo.

8Chauta adamuitananso Samuele kachitatu. Pompo adadzukanso, napita kwa Eli, nakanena kuti, “Ndabwera, mwandiitana ndithu basi.” Pamenepo Eli adazindikira kuti Chauta ndiye amene ankaitana mnyamatayo.

9Tsono adauza Samuele kuti, “Pita, kagone. Akakuitananso, ukanene kuti, ‘Lankhulani, Inu Chauta, poti mtumiki wanune ndilikumva.’ ” Choncho Samuele adapita kukagona kumalo kwake.

10Chauta adabwera nadzaimirira pomwepo, ndipo adaitananso monga nthaŵi zina zija kuti, “Samuele, Samuele!” Samuele adayankha kuti, “Lankhulani, poti mtumiki wanune ndilikumva.”

11Tsono Chauta adauza Samuele kuti, “Tamvera, patsala pang'ono kuti ndichite chinthu mu Israele chimene chidzadabwitsa aliyense amene adzachimva.

12Tsiku limenelo ndidzachitadi zonse zimene ndidalankhula za Eli ndi banja lake, kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza.

13Ndikumdziŵitsa Eliyo kuti ndili pafupi kulanga banja lake mpaka muyaya, chifukwa cha zoipa zimene ana ake ankandichita. Eli ankazidziŵa zimenezo, koma osaŵaletsa.

14Nchifukwa chake ndikulumbira kuti mlandu wa banja la Eli sudzatha konse mpaka muyaya, ngakhale adzapereke nsembe kapena zopereka zina.”

15Samuele adagona mpaka m'maŵa. Atadzuka adatsekula zitseko za nyumba ya Chauta. Ankachita mantha kumuuza Eli zimene Chauta adaamuululirazo.

16Koma Eli adamuitana nati, “Samuele mwana wanga.” Samuele adati, “Ŵaŵa!”

17Apo Eli adafunsa kuti, “Kodi nchiyani chimene Mulungu wakuuza? Usandibisire. Mulungu akulange ndithu, ukandibisira kanthu kalikonse pa zonse zimene wakuuza.”

18Choncho Samuele adamuuza zonse osambisira kanthu kalikonse. Ndipo Eli adati, “Ameneyo ndi Chauta. Nachite zimene zikumkomera.”

19Monse Samuele ankakula, Chauta anali naye, motero zonse zimene Samueleyo ankanena zinkachitikadi.

20Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, adadziŵa kuti Chauta adamsankha Samuele kuti akhale mneneri.

21Chauta ankadziwululabe ku Silo. Kumeneko ankamveketsa mau ake kwa Samuele polankhula naye. Ndipo mau ake a Samuele ankafika kwa Aisraele onse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help