1Anthu adaloŵa nalo Bokosi lachipangano lija, nalikhazika pamalo pake m'kati mwa hema limene Davide adaamangira Bokosilo. Tsono adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Mulungu.
2Davide atamaliza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjanozo, adadalitsa anthu onse m'dzina la Chauta.
3Kenaka adagaŵira Aisraele onsewo, amuna ndi akazi, aliyense mtanda wa buledi, nthuli ya nyama ndiponso keke ya mphesa zouma.
4Ndipo adaika Alevi ena kuti azitumikira ku Bokosi lachipangano la Chauta, ndiye kuti azipemphera, azithokoza ndi kumatamanda Chauta, Mulungu wa Israele.
5Asafu ndiye amene anali mtsogoleri, ndipo omthandiza wake anali Zekariya, Yeiyele, Semiramoti, Yehiyele, Matitiya, Eliyabu, Benaya, Obededomu ndi Yeiyele. Ameneŵa ndiwo adasankhindwa kuti akhale oliza azeze ndi apangwe. Asafu ndiye amene anali woliza ziwaya zamalipenga,
6ndipo Benaya ndi Yehaziele, ansembe, ndiwo amene anali oliza malipenga nthaŵi zonse patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta.
Nyimbo yotamanda(Mas. 105.1-15; 96.1-13; 106.1, 47-48)7Tsiku limenelo ndi limene Davide adayamba kulamula Asafu ndi abale ake kuti akhale oyang'anira nyimbo zothokoza Chauta.
8Thokozani Chauta,
tamandani dzina lake,
lalikani za ntchito zake
pakati pa mitundu ya anthu.
9Imbirani Chauta, muimbireni nyimbo zomtamanda,
lalikani za ntchito zake zodabwitsa.
10Munyadire dzina lake loyera.
Ikondwe mitima ya anthu
amene amapembedza Chauta.
11Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake.
Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza.
12Muzikumbukira ntchito zodabwitsa za Chauta,
zozizwitsa zimene adachita,
ndi m'mene ankaweruzira anthu,
13inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
inu ana a Yakobe, osankhidwa a Chauta.
14Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu.
Amalamulira dziko lonse lapansi.
15Muzikumbukira chipangano chake nthaŵi zonse,
musaiŵale mpaka muyaya mau amene Iye adalamula,
16 Gen. 12.7; Gen. 26.3 Amakumbikira chipangano adachita ndi Abrahamu chija,
lonjezo lake limene adachita molumbira kwa Isaki.
17 Gen. 28.13 Lonjezolo adabwerezanso kwa Yakobe,
kuti likhale chipangano chokhazikika
mu Israele mpaka muyaya.
18Adati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani,
kuti likhale choloŵa chako chokhalira iweyo.”
19Pamene anali anthu oŵerengeka,
anthu osatchuka, ongokhala nao m'dzikomo,
20ongomayendayenda kuchokera ku mtundu wina wa anthu
kupita ku mtundu wina,
kuchokera ku ufumu wina kupita ku ufumu wina,
21 Gen. 20.3-7 sadalole ndi mmodzi yemwe aŵapsinje,
adalanga mafumu ena chifukwa cha anthu akewo.
22Adati, “Musaŵakhudze odzozedwa anga,
musaŵachite choipa aneneri anga.”
23Imbirani Chauta,
inu anthu a dziko lonse lapansi.
Lengezani tsiku ndi tsiku
za m'mene Iye adapulumutsira anthu ake.
24Lalikani za ulemerero wake
kwa anthu a mitundu yonse,
simbani za ntchito zake zodabwitsa
kwa anthu a m'maiko onse.
25Chauta ngwamkulu,
ngwoyenera kumtamanda kwambiri,
ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
26Paja milungu ya anthu a mitundu ina
ndi mafano chabe,
koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba.
27Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake,
mphamvu ndi chimwemwe zili m'Nyumba mwake.
28Tamandani Chauta, inu anthu a mitundu yonse,
vomerezani kuti ulemerero ndi mphamvu,
zonse nza Chauta.
29Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta.
Bwerani ndi zopereka,
ndipo muloŵe m'mabwalo a Nyumba yake.
Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera.
30Njenjemerani pamaso pake,
inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Ndithu dziko lapansi lakhazikika kolimba,
osatha kuligwedeza.
31Zakumwamba zisangalale,
za pansi pano zikondwere,
zonsezo zilengeze kwa anthu onse kuti,
“Chauta ndiye mfumu.”
32Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo,
minda ikondwe pamodzi ndi zonse zomera m'menemo.
33Mitengo yam'nkhalango idzaimbira Chauta mokondwa,
pamene adzabwera kudzalamulira dziko lapansi.
34 2Mbi. 5.13; 7.3; Eza. 3.11; Mas. 100.5; 106.1; 107.1; 118.1; 136.1; Yer. 33.11 Thokozani Chauta, pakuti ngwabwino,
chikondi chake chosasinthika nchamuyaya.
35Munenenso kuti, “Tipulumutseni,
Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
mutisonkhanitse ndi kutilanditsa
kwa mitundu ina ya anthu,
kuti tikuthokozeni potchula dzina lanu loyera,
ndi kuti tizinyadira pokutamandani.
36Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele,
kuyambira muyaya mpaka muyaya!”
Tsono anthu onse adati, “Inde momwemo.” Ndipo adatamanda Chauta.
37Tsono Davide adasiya Asafu pamodzi ndi abale ake kumene kunali Bokosi lachipangano la Chauta, kuti azitumikira nthaŵi zonse ku Bokosilo monga m'mene kunkafunikira tsiku lililonse.
38Obededomu pamodzi ndi abale ake 68 ankathandizana nawo pa ntchitoyo. Nthaŵi imeneyo Obededomu, mwana wa Yedutuni, ndiponso Hosa, anali ndi udindo wolonda pa makomo.
39Davide adasiyanso wansembe Zadoki pamodzi ndi abale ake ansembe ku chihema cha Chauta, ku kachisi wa ku Gibiyoni.
40Adaŵasiya kumeneko kuti azipereka nthaŵi zonse nsembe zopsereza kwa Chauta pa guwa la nsembe zopsereza, m'maŵa ndi madzulo, potsata zonse zimene zidalembedwa m'buku la Malamulo a Mose amene Chauta adalamula Aisraele.
41Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni, kudzanso onse otsala amene adasankhidwa moŵatchula maina, kuti azithokoza Chauta, chifukwa cha chikondi chake chosasinthika ndi chamuyaya.
42Hemani ndi Yedutuni ankayang'anira malipenga ndi ziwaya zamalipenga, ndiponso zipangizo zina zoimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni adaŵaika kuti azilonda pa chipata.
43 2Sam. 6.19, 20 Pambuyo pake anthu onse adachoka, aliyense kupita kunyumba kwake. Davide nayenso adapita kwao kuti akadalitse banja lake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.