1Mtsogoleri wanzeru amaphunzitsa anthu ake mwambo,
ulamuliro wa munthu wanzeru umakhala wadongosolo.
2Monga m'mene aliri mtsogoleri,
nduna zakenso zimakhala chimodzimodzi.
Monga m'mene aliri mkulu wa mzinda,
anthu akenso amakhala chimodzimodzi.
3Mfumu yopanda mwambo imaononga anthu ake,
mzinda kuti ukhale pabwino, nchifukwa cha
atsogoleri anzeru.
4Dziko lapansi ulamuliro wake uli m'manja mwa Mulungu.
Amalipatsa mtsogoleri woyenera pa nthaŵi yake.
5Kukhoza kwa munthu kuli m'manja mwa Ambuye.
Iye ndiye amene amapereka ulemerero kwa munthu
wolamulira.
Atsutsa kunyada6Usapsere mtima mnzako chifukwa cha cholakwa chilichonse,
ndipo usachite kanthu mwachipongwe.
7Kunyada kumaipira Mulungu ndi anthu omwe,
ndipo kusalungama kumaipira onsewo.
8Kusalungama, chipongwe ndi chuma zimathetsa
ulamuliro wa mtundu wa anthu,
ndiye mtundu wina umadzalamulira m'malo mwake.
9Munthu ndi fumbi chabe ndi phulusa, anganyade bwanji?
Suja m'thupi mwake mumatha kuwola iye akali moyo!
10Matenda achimgonera amathetsa nzeru asing'anga.
Munthu amati lero ndi mfumu, maŵa lino ndi mtembo.
11Tonse tikafa, zathu nzimodzimodzi:
tizilombo, nyama zokwaŵa ndi nyongolotsi.
12Kuti munthu wayamba kunyada,
mumamuwonera kusiya Ambuye,
ndiye kuti kufulatira Mlengi wake.
13Paja chiyambi cha kunyada ndi tchimo,
ndiye kuti woumirira kunyada kwake amachulukitsa zonyansa.
Nchifukwa chake anthu otero Ambuye adaŵatumizira
zilango zodabwitsa,
ndipo adaŵaononga kotheratu.
14 1Sam. 2.8; Lk. 1.52 Ambuye adachotsa mafumu amphamvu pa mipando,
m'malo mwao adaikamo anthu otsika.
15Ambuye adazula mitundu ya anthu odzitama,
ndipo m'malo mwao adaikamo anthu odzichepetsa.
16Ambuye adasakaza maiko a anthu a mitundu ina,
adaŵaononga mpaka pamaziko penipeni pa dziko.
17Ena adaŵachotseratu ndi kuŵaonongadi
mpaka kuti asakumbukikenso pa dziko lapansi.
18Mlengi sadalenge munthu kuti azinyada,
kapena wobadwa mwa mkazi kuti akhale ndi ukali woopsa.
Za anthu oyenera kulandira ulemu19Ndi mtundu wa zolengedwa ziti
umene uyenera kulandira ulemu?
Mtundu wa anthu.
Ndi anthu a mtundu wanji
amene ayenera kulandira ulemu?
Anthu oopa Ambuye.
Ndi mtundu wa zolengedwa ziti umene suyenera
kulandira ulemu?
Mtundu wa anthu.
Ndi anthu a mtundu wanji
amene ulemu suŵayenera?
Anthu ophwanya malamulo.
20Anthu apachibale mtsogoleri wao ndiye amalandira ulemu,
ndipo anthu oopa Ambuye amalandira ulemu
kwa Ambuyewo.
21Uziwopa Ambuye, ndipo adzakulandira.
Khala wokanika ndi wonyada, ndipo adzakukana.
22Olemera, otchuka ndi osauka,
onsewo ulemerero wao uli pa kuwopa Ambuye.
23Si chilungamo konse kunyoza wosauka amene ali ndi nzeru.
Nkulakwa kulemekeza munthu wochimwa.
24Mkulu, muweruzi ndi wolamulira, onsewo ngoyenera kuŵalemekeza.
Koma mwa onsewo palibe woti nkupambana munthu woopa Ambuye.
25Kapolo wanzeru mfulu zomwe zidzamtumikira.
Munthu wanzeru sadzaŵiringula nazo.
Za kulankhula zoona ndi kudzichepetsa26Pogwira ntchito zako usayerekedwe,
pamene uli m'zovuta usadzitame.
27Nkwabwino kugwira ntchito ndi kukhala ndi zinthu zambiri,
koposa kunyada ndi kukhala ndi njala.
28Mwana wanga, udzilemekeze, koma modzichepetsa,
udzipatse ulemu koma moyenera.
29Ndani angamuyese wolungama munthu wodzichimwira yekha,
kapena kumlemekeza munthu wosadzilemekeza yekha?
30Munthu wosauka amamlemekeza chifukwa cha nzeru zake,
pamene munthu wolemera amamlemekeza chifukwa
cha chuma chake.
31Ngati munthu amlemekeza ali mmphaŵi
nanji akadakhala wolemera!
Ngati munthu amnyoza ali wolemera,
nanji akadakhala wosauka!
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.