1 Ahe. 2.18; 4.15 Zitatha izi, Mzimu Woyera adatsogolera Yesu kupita ku chipululu kuti Satana akamuyese.
2Pa masiku makumi anai Yesu adasala zakudya usana ndi usiku, ndipo pambuyo pake adamva njala.
3Tsono Woyesa uja adadza namuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, lamulani miyala ili apayi kuti isanduke chakudya.”
4Deut. 8.3Koma Yesu adati, “Malembo akuti,
“ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha,
koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ”
5Pambuyo pake Satana adatenga Yesu kupita naye ku Yerusalemu, Mzinda Wopatulika, nakamuimika pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu.
6Mas. 91.11, 12 Adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja Malembo akuti,
“ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni,
iwo adzakunyamulani m'manja mwao,
kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ”
7 Deut. 6.16 Koma Yesu adati, “Malembo akutinso, ‘Usaŵayese Ambuye, Mulungu wako.’ ”
8Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye pa phiri lalitali kwambiri, ndipo adamuwonetsa maufumu onse a pansi pano ndi ulemerero wake.
9Tsono adamuuza kuti, “Zonsezi ndidzakupatsani mukagwada pansi ndi kundipembedza.”
10Deut. 6.13 Apo Yesu adati, “Choka, Satana! Paja Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ”
11Pamenepo Satana adamsiya, angelo nkubwera kumadzamutumikira Yesuyo.
Yesu ayamba ntchito yake ku Galileya(Mk. 1.14-15; Lk. 4.14-15)12 Mt. 14.3; Mk. 6.17; Lk. 3.19, 20 Yesu atamva kuti Yohane adamponya m'ndende, adabwerera ku Galileya.
13Yoh. 2.12Adachokako ku Nazarete, nakakhala ku Kapernao, mzinda wina wa m'mbali mwa nyanja ku dera la Zebuloni ndi Nafutali.
14Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaanena kuti,
15 Yes. 9.1, 2 “Iwe dziko la Zebuloni ndi iwe dziko la Nafutali,
ku njira yakunyanja, patsidya pa Yordani,
iwe Galileya, dziko la anthu akunja!
16Anthu okhala mu mdima
aona kuŵala kwakukulu.
Anthu okhala m'dziko la mdima wabii wa imfa,
kuŵala kwaŵaonekera.”
17 Mt. 3.2 Kuyambira nthaŵi imeneyo Yesu adayamba kulalika kuti, “Tembenukani mtima, chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.”
Yesu aitana asodzi anai(Mk. 1.16-20; Lk. 5.1-11)18Yesu akuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu aŵiri pachibale pao: Simoni wotchedwa Petro, ndi mbale wake Andrea, akuponya khoka m'nyanjamo, popeza kuti anali asodzi.
19Yesu adaŵauza kuti, “Inu, munditsate, ndikakusandutseni asodzi a anthu.”
20Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi.
21Atapitirira pamenepo, Yesu adaona enanso aŵiri pachibale pao: Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwo anali m'chombo pamodzi ndi bambo waoyo, akukonza makoka ao, Yesu nkuŵaitana.
22Pomwepo iwowo adasiya chombo chao ndi bambo wao uja, namatsata Yesu.
Yesu ayamba kuphunzitsa, kulalika ndi kumachiritsa odwala(Lk. 6.17-19)23 Mt. 9.35; Mk. 1.39 Yesu adayendera dziko lonse la Galileya akuphunzitsa m'nyumba zamapemphero ndi kulalika Uthenga Wabwino wonena za ufumu wakumwamba. Ankachiritsanso nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.
24Mbiri yake idabuka m'dziko lonse la Siriya, kotero kuti anthu ankabwera kwa Iye ndi odwala onse ovutika ndi nthenda ndi zoŵaŵa zosiyanasiyana, ogwidwa ndi mizimu yoipa, akhunyu ndi opunduka, Iye nkumaŵachiritsa.
25Anthu ambirimbiri ankamutsata kuchokera ku Galileya, ku dera lotchedwa Mizinda Khumi, ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi kutsidya kwa mtsinje wa Yordani.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.