1 2Maf. 25.25 Pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mdzukulu wa Elisama, wa m'banja la mfumu, mmodzi mwa atsogoleri akuluakulu a mfumu, adafika ndi anthu khumi ku Mizipa kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu. Pamene ankadya naye kumeneko,
2Ismaele, mwana wa Netaniya, pamodzi ndi anthu khumi aja, adadzambatuka napha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Adamupha ndi malupanga ao munthu amene mfumu ya ku Babiloni idaamuika kuti akhale bwanamkubwa wa dziko.
3Ismaele adaphanso Ayuda onse amene anali ku Mizipa ndiponso ankhondo a Ababiloni amene anali kumeneko.
4M'maŵa mwake, anthu asanadziŵe kuti Gedaliya waphedwa,
5kudafika anthu makumi asanu ndi atatu kuchokera ku Sekemu, ku Silo ndi ku Samariya. Ndevu zao adaameta, zovala zao zinali zong'ambikang'ambika, ndipo matupi ao anali otemekatemeka. Adatenga nsembe zaufa ndi lubani, kukapereka ku Nyumba ya Chauta.
6Tsono Ismaele, mwana wa Netaniya, adabwera akulira kuchokera ku Mizipa kudzakumana nawo. Atakumana nawo, adati, “Bwerani, mudzaonane ndi Gedaliya mwana wa Ahikamu.”
7Atangofika pakati pa mudzi, Ismaele mwana wa Netaniya ndi anthu ake, adaŵapha onsewo naŵataya m'chitsime.
8Koma pa gulu limenelo panali anthu khumi amene adaauza Ismaele kuti, “Ifeyo musatiphe, tili ndi tirigu, barele, mafuta, ndi uchi, zimene tidabisa m'minda.” Motero adaŵaleka osaŵaphera kumodzi ndi anzao aja.
9Chitsime chimene Ismaele adatayamo anthu amene adaŵapha aja chinali chitsime chachikulu chija chimene adaakumba ndi mfumu Asa, ataopsedwa ndi Basa mfumu ya ku Israele. Ismaele, mwana wa Netaniya adachidzaza ndi mitembo.
10Pambuyo pake Ismaele adaŵatenga ukapolo anthu onse amene adatsala ku Mizipa. Anthuwo ndi aŵa: ana aakazi a mfumu, ndi onse otsala ku Mizipa, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa nkhondo adaŵapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wao. Ndipo anthu ameneŵa adachoka nawo ndi cholinga choti akaloŵe nawo m'dziko la Aamoni.
11Pamene Yohanani, mwana wa Kareya, ndi atsogoleri a ankhondo, adamva zoipa zimene Ismaele mwana wa Netaniya adaachita,
12adasonkhanitsa anthu onse amene anali nawo, napita kukamenyana naye nkhondo. Adakampeza ku chidziŵe cha ku Gibiyoni.
13Ndipo anthu onse amene Ismaele adaaŵagwira ataona Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri a magulu ankhondo aja, adasangalala.
14Anthu onse amene Ismaele adaaŵatenga ukapolo kuchoka nawo ku Mizipa, adabwerera napita kwa Yohanani mwana wa Kareya.
15Koma Ismaele mwana wa Netaniya, pamodzi ndi anthu ake asanu ndi atatu, adathaŵa Yohanani, kuthaŵira kwa Aamoni.
16Pamenepo Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri a magulu ankhondo, adatenga otsala a ku Mizipa amene Ismaele mwana wa Netaniya, adaaŵatenga ukapolo, atapha Gedaliya mwana wa Ahikamu. Amene adaŵatengawo anali ankhondo, akazi, ana ndi otumikira bwalo la mfumu, amene Yohanani adaabwera nawo kuchokera ku Gibiyoni.
17Adanyamuka ulendo wao nakaima ku Geruti-Kimuhamu, pafupi ndi Betelehemu. Ankafuna kupita ku Ejipito,
18chifukwa choopa Ababiloni. Anali ndi manthadi chifukwa choti Ismaele mwana wa Netaniya, adaapha Gedaliya, mwana wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babiloni idaamuika kuti akhale bwanamkubwa wa dziko.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.