1Inu Mulungu, pulumutseni,
pakuti madzi ayesa m'khosi.
2Ndamira m'thope lozama
m'mene mulibe popondapo polimba.
Ndaloŵa m'madzi ozama,
ndipo mafunde andimiza.
3Ndafooka ndi kulira kwanga,
kum'mero kwanga kwauma.
M'maso mwada pamene ndikuyembekezera Mulungu wanga.
4 Mas. 35.19; Yoh. 15.25 Anthu odana nane popanda chifukwa
ndi ochuluka kupambana tsitsi la kumutu kwanga.
Ndi amphamvu anthu ongofuna kundiwononga,
ndi kundineneza ndi mabodza ao.
Kodi ndiyenera kubweza zimene sindinabe?
5Inu Mulungu, mumadziŵa kupusa kwanga,
zolakwa zanga sizili zobisika pamaso panu.
6Inu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse,
musalole kuti ndiŵachititse manyazi
anthu okhulupirira Inu.
Inu Mulungu wa Israele,
musalole kuti anthu okufunafunani
anyozeke chifukwa cha ine.
7Pakuti ndanyozedwa,
nkhope yanga yagwidwa ndi manyazi
chifukwa cha Inu.
8Kwa abale anga ndasanduka mlendo,
kwa ana a mai wanga ndili ngati wakudza.
9 Yoh. 2.17; Aro. 15.3 Changu chochitira Nyumba yanu chandiphetsa,
chipongwe cha anthu okunyozani chandigwera.
10Pamene ndidadzilanga posala zakudya,
anthu adandinyoza.
11Pamene ndidavala chiguduli kuwonetsa chisoni,
ndidasanduka chinthu choŵaseketsa.
12Anthu okhala pa chipata amandinena,
ndipo zidakwa zimandiimba nyimbo.
13Koma ine ndimapemphera kwa Inu Chauta.
Mundiyankhe pa nthaŵi yabwino, Inu Mulungu,
chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika,
ndi chithandizo chanu chokhulupirika.
14Pulumutseni kuti ndisamire m'matope,
landitseni kwa adani anga ndi ku madzi ozama.
15Musalole kuti chigumula chindikokolole,
kapena kuti nyanja yakuya indimize.
Musalole kuti manda atseke kukamwa atandimeza.
16Mundiyankhe, Inu Chauta,
pakuti chikondi chanu chosasinthika nchabwino.
Munditchere khutu
chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.
17Musandibisire ine mtumiki wanu nkhope yanu,
fulumirani kundithandiza,
pakuti ndili pa zovuta.
18Senderani pafupi, mundiwombole,
mundipulumutse kwa adani anga.
19Inu mumadziŵa m'mene anthu amandinyozera,
m'mene amandichititsira manyazi ndi kundichotsera ulemu.
Adani anga onse mumaŵadziŵa.
20Mtima wanga wasweka chifukwa cha zipongwe,
ndataya mtima kotheratu.
Ndidafunafuna ena ondichitira chifundo,
koma panalibe ndi mmodzi yemwe.
Ndidafunafunanso ena ondisangalatsa,
koma sindidampeze ndi mmodzi yemwe.
21 Mt. 27.48; Mk. 15.36; Lk. 23.26; Yoh. 19.28, 29 Adandipatsa ulembe kuti ndidye,
ndipo nditamva ludzu,
adandipatsa vinyo wosasa kuti ndimwe.
22 Aro. 11.9, 10 Zakudya zao zisanduke msampha.
Akodwe ndi maphwando a nsembe zao.
23Maso ao achite chidima kuti asathe kupenya,
ziwuno zao zizinjenjemera kosalekeza.
24Muŵagwetsere ukali wanu,
mkwiyo wanu woyaka moto uŵagwire.
25 Ntc. 1.20 Zithando zao zisanduke zopanda anthu,
m'mahema mwao musatsale munthu ndi mmodzi yemwe.
26Iwo amazunza amene Inu mwamkantha,
ndipo amene Inu mwamupweteka,
iwo amaonjezera kumuvutitsa.
27Muŵalange pa cholakwa chao chilichonse,
musagamule kuti alibe mlandu.
28 Eks. 32.32; Chiv. 3.5; 13.8; 17.8 Muŵafafanize m'buku la amoyo,
asalembedwe pamodzi ndi anthu anu.
29Koma ine ndazunzika ndipo ndikumva kuŵaŵa.
Nyamuleni Inu Mulungu, kuti ndipulumuke.
30Ndidzatamanda dzina la Mulungu pomuimbira nyimbo,
ndidzalalika ukulu wake pomuthokoza.
31Zimenezi zidzakondwetsa Chauta kupambana nsembe,
ngakhale nsembe ya ng'ombe yamphongo.
32Ozunzika aone zimenezo ndipo asangalale,
inu amene mumafunafuna Mulungu, mulimbenso mtima.
33Paja Chauta amamvera anthu osoŵa,
sanyoza anthu ake omangidwa ndi unyolo.
34Kumwamba ndi pansi pano,
nyanja ndi zonse zoyenda m'menemo zitamande Iye.
35Mulungu adzapulumutsa Ziyoni,
ndipo adzamanganso mizinda ya Yuda.
Anthu ake adzakhala kumeneko,
ndipo lidzakhala dziko lao.
36Ana a atumiki ake nawonso adzalilandira
kuti likhale lao,
ndipo okonda Mulungu adzakhala m'menemo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.