1Ndikadakonda kuti mundilekerere pang'ono pa kupusa kwangaku. Tandilekereranipo ndithu.
2Nsanje imene ndikukuchitirani ndi yonga ya Mulungu. Pakuti ndidakupalitsani ubwenzi ndi mwamuna mmodzi yekha, ngati namwali wangwiro ndi woyera mtima, kuti mukhale akeake a Khristu.
3Gen. 3.1-5, 13 Njoka ndi kuchenjera kwake idanyenga Heva. Ndikuwopa kuti maganizo anu angaipitsidwe chimodzimodzi, ndipo mungaleke kudzipereka kwa Khristu ndi mtima wonse.
4Wina amati akabwera kudzalalika Yesu wina wosiyana ndi amene tidamlalika ife, inu mumangomulekerera. Kapena mukalandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu Woyera amene mudamlandira kale, inu nkumaloladi. Mwinanso mukalandira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene mudalandira kale, inu nkumauvomeradi msangamsanga.
5Ndikuganiza kuti atumwi anu apamwambawo sandiposa ine pa kanthu kalikonse.
6Ngakhale ndine mbuli pa luso lolankhula, koma pa nzeru ndiye ai. Zimenezi ndidakuwonetsani kaŵirikaŵiri pa zonse.
7Ndidadzitsitsa ndekha ineyo, kuti inu mukule. Ndidakulalikirani mwaulere Uthenga Wabwino wa Mulungu. Kodi ndiye kuti pakutero ndidalakwa?
8Pakulandira zondithandiza kuchokera ku mipingo ina, ndidachita ngati kuŵalanda zao kuti ndikutumikireni inu.
9Afi. 4.15-18Ndipo pamene ndinali kwanuko, nditasoŵa kanthu, sindidavute aliyense, pakuti abale ena ochokera ku Masedoniya adaandipatsa zonse zimene ndinkasoŵa. Pa zonse ndinkasamala kwambiri kuti ndisakhale ngati katundu wokulemerani, ndipo ndidzapitirirabe kutero.
10Malinga ndi choona cha Khristu chimene chili mwa ine, ndikunenetsa kuti palibe munthu amene adzandiletsa kunyadira zimenezi m'madera onse a ku Akaiya.
11Ndikutero chifukwa chiyani? Kodi monga sindikukondani? Akudziŵa ndi Mulungu kuti ndimakukondani.
12Zimene ndikuchita tsopano, ndidzazichitabe, kuti ndisaŵapatse mpata onyenga aja amene akufuna danga loti anyadire, ndi kumanena kuti iwonso akugwira ntchito molingana ndi ife.
13Anthu otereŵa si atumwi oona, koma antchito onyenga, amene amadzizimbaitsa, naoneka ngati atumwi a Khristu.
14Zimenezitu si zododometsa ai, pakuti Satana yemwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati mngelo wounikira anthu.
15Motero si chodabwitsa ngati atumiki ake omwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati otumikira chilungamo. Potsiriza adzalandira molingana ndi zimene ankachita.
Za zoŵaŵa zimene Paulo adamva chifukwa cha utumwi wake16Ndikufuna kubwerezanso kuti munthu wina aliyense asandiyese wopusa. Koma ngati inuyo mukundiyesadi wopusa, chabwino mundilandire ngati chitsiru, kuti inenso ndinyadirepo.
17Zimene ndimati ndinena panozi si zimene Ambuye afuna kuti ndinene, koma ndikungonyada, monga momwe amachitira wopusa.
18Tsono popeza kuti ambiri akunyadira zapansipano, inenso ndidzatero.
19Inu mumati ndinu anzeru kwambiri, nchifukwa chake anthu opusa mumangoŵalekerera mokondwa.
20Mumangolekerera munthu akakuyesani akapolo, kapena akadya chuma chanu, kapena akakunyengani, kapena akakunyozani, kapena akakumenyani kumaso.
21Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nkuchita zotere.
Tsopano ndilankhula ngati wopusa: zimene wina aliyense anganyadire, zomwezo inenso ndingathe kuzinyadira.
22Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso. Kodi iwo ndi Aisraele? Inenso. Kodi iwo ndi ana a Abrahamu? Inenso.
23Ntc. 16.23Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikulankhula ngati wamisala, ndine mtumiki woposa iwowo. Ndidagwira ntchito kwambiri kopambana iwo, kaŵirikaŵiri ndinali pafupi kufa.
24Deut. 25.3Kasanu Ayuda adandikwapula mikwapulo 39.
25Ntc. 16.22; Ntc. 14.19Katatu Aroma adandimenya ndi ndodo. Kamodzi anthu adandiponya miyala. Katatu pa maulendo athu apanyanja, chombo chathu chidasweka. Nthaŵi ina ndidayandama pakati pa nyanja tsiku lathunthu, usana ndi usiku.
26Ntc. 9.23; Ntc. 14.5Pa maulendo anga ochuluka ndidakumana ndi zoopsa za mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa Ayuda anzanga, ndi zina zochokera kwa akunja. Ndidapeza zoopsa m'mizinda, m'thengo, ndi pakati pa abale onyenga.
27Ndidagwira ntchito zolemetsa, ndipo kaŵirikaŵiri sindidalaŵe tulo. Ndidamva njala ndi ludzu, kaŵirikaŵiri osaona chakudya, ndipo kusoŵa zovala ndi kuzizidwa.
28Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimapsinjidwa ndi udindo wa kusamalira mipingo yonse.
29Ndani ali wofooka, ine osakhala naye pamodzi m'kufooka kwakeko? Ndani amene mnzake amchimwitsa, ine osavutika mu mtima?
30Ngati ndiyenera kunyada, ndidzanyadira kufooka kwanga.
31Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu, amene tiyenera kumtamanda nthaŵi zonse, akudziŵa kuti sindikunama.
32Ntc. 9.23-25Pamene ndinali ku Damasiko, bwanamkubwa woimirira mfumu Areta, adaaika alonda kuzinga mzinda wonsewo kuti andigwire.
33Koma anthu adandiika m'dengu nanditsitsira pa windo la m'lingalo, motero ndidamthaŵira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.