Yer. 51 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kupitirira ndithu kwa chilango cha Babiloni

1Chauta akunena kuti,

“Ndidzautsa mphepo yoti idzaononge Babiloni

pamodzi ndi onse okhala m'dziko la Babiloni.

2Ndidzatuma alendo ku Babiloni,

kuti adzampepete ndi kuseseratu zonse

zokhala m'dziko lake.

Iwowo adzamuukira pa mbali zonse nthaŵi ya zoopsayo.

3Okoka uta musaŵalekerere,

kapena onyadira chovala chao chankhondo.

Anyamata ake musasiyeko ndi mmodzi yemwe.

Ankhondo ake onse muŵaononge.

4Adzavulazidwa ndi kufera m'dziko lonse

ndi m'miseu ya mzinda wao womwe.

5Israele ndi Yuda sadasiyidwe ndi Mulungu wao,

Chauta Wamphamvuzonse.

Koma dziko la Ababiloni nlodzaza ndi machimo,

machimo ake onyoza Woyera uja wa Israele.

6“Aliyense mwa inu athaŵe, achoke ku

Babiloni kuti apulumutse moyo wake.

Musaphedwe naye pamodzi

pamene adzalandira chilango chake.

Limeneli ndilodi tsiku limene Chauta adzaŵalanga,

ndipo adzaŵalipsira kwathunthu.

7 Chiv. 17.2-4; 18.3 Pajatu Babiloni anali ngati chikho

chagolide m'manja mwa Chauta,

kuti aledzeretse dziko lonse lapansi.

Mitundu yambiri ya anthu idamwako vinyo wake,

nchifukwa chake idapenga.

8Babiloni wagwa mwadzidzidzi ndipo waonongeka.

Mlireni, mfunireni mankhwala,

kuti mwina nkuchira.

9 Chiv. 18.5 Ena adati, ‘Tidayesa kumpatsa mankhwala koma sadachire.

Tiyeni tingomsiya, timchokere

ndipo aliyense apite ku dziko lakwao.

Paja mlandu wake wafika mpaka kumwamba,

wafika mpaka ku mlengalenga.’ ”

10Tsono Chauta waonetsa poyera

kuti ifeyo ndife osalakwa.

Tiyeni tilengeze ku Ziyoni

zimene Chauta, Mulungu wathu, watichitira.

11“Songolani mivi,

tengani zishango.”

Chauta wautsa mitima ya mafumu a Amedi, poti cholinga chake nchoti aononge Babiloni. Afuna kumlipsira chifukwa choononga Nyumba yake.

12Kwezani mbendera yankhondo

ndipo muwononge malinga a Babiloni.

Mulimbitse oteteza, muike alonda,

mukonzekere kulalira.

Pakuti Chauta watsimikiza,

ndipo adzachitadi zimene adanena za anthu a ku Babiloni.

13 Chiv. 17.1 Inu amene muli ndi mitsinje yambiri,

ndinu olemera kwambiri,

koma chimalizo chanu chafika,

moyo wanu watha.

14Chauta Wamphamvuzonse adalumbira pali

Iye yemwe mwini wake kuti,

“Ndidzatuma anthu osaŵerengeka ngati dzombe

kuti adzakuthireni nkhondo,

ndipo adzafuula,

kuwonetsa kuti apambana.”

Nyimbo yotamanda Mulungu

15Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi

ndi mphamvu zake.

Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake,

ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba.

16Iye akalankhula, kumamveka mkokomo wa madzi kumwamba,

ndiye amene amadzetsa mitambo

kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.

Amang'animitsa mphezi za mvula,

amakunthitsa mphepo kuchokera kumene amaisunga.

17Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru.

Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi

ndi mafano ake.

Mafano amene amapangawo ngabodza,

mwa iwo mulibe konse moyo.

18Mafanowo ngachabechabe, oyenera kuŵaseka,

ndipo pamene anthuwo adzalangidwe,

mafanowo adzaonongedwa.

19Koma Mulungu wa Yakobe sali ngati mafanowo,

Iye ndiyedi Mlengi wa zonse.

Aisraele ndi anthu ake amene Iye adaŵasankha,

dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.

20Iwe Babiloni ndiwe nyundo yanga,

chida changa chankhondo:

ndi iwe ndimaphwanyaphwanya mitundu ya anthu,

ndimaononga maufumu.

21Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya akavalo

ndi okwerapo ao.

Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya magaleta

ndi oyendetsa ake.

22Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya amuna ndi akazi ao.

Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya nkhalamba ndi achinyamata.

Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya anyamata ndi anamwali.

23Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya abusa ndi ziŵeto zao.

Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya alimi ndi ng'ombe zao.

Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya abwanamkubwa

ndi atsogoleri ankhondo.

Za chilango cha Babiloni

24“Inu mukupenya, ndidzalipsira Babiloni ndi onse okhalamo chifukwa cha zolakwa zonse zimene adachita ku Ziyoni,” akutero Chauta.

25“Ndikukuimba mlandu, iwe phiri loononga,

iwe amene umasakaza dziko lonse lapansi.

Ndidzasamula dzanja langa pofuna kukulanga,

ndi kukugubuduzira kunsi kuchokera pa mathanthwe ako.

Ndidzakusandutsa phiri lopserera.

26Palibe mwala wako ndi umodzi womwe umene

adzabwere nawo kuti augwiritse ntchito ngati

mwala wapangodya.

Iwe udzakhala chipululu mpaka muyaya,”

akutero Chauta.

27“Kwezani mbendera yankhondo pa dziko,

lizani lipenga kuti mitundu ya anthu imve.

Itanani mitundu yonse kuti imuthire nkhondo Babiloni.

Itanani maufumu a ku Ararati,

a ku Mini ndi a ku Asikenazi.

Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane

ndi Babiloniyo.

Mubweretse akavalo ochuluka ngati dzombe.

28Sonkhanitsani mitundu ya anthu kuti imuthire nkhondo.

Muitane mafumu a ku Medi, pamodzi ndi

abwanamkubwa ndi nduna zao,

ndiponso ankhondo a m'maiko onse amene amaŵalamulira.

29Dziko likunjenjemera,

likuphiriphitha chifukwa cha kupweteka,

chifukwa zimene Chauta adakonzera Babiloni

zidzachitikadi,

zakuti adzamsandutsa dziko lachipululu

lopanda anthu.

30Ankhondo a ku Babiloni aleka kuponya nkhondo,

angokhala khale m'malinga ao.

Mphamvu zao zatha,

asanduka ngati akazi.

Nyumba zake zatenthedwa,

mipiringidzo ya zipata zake yathyoka.

31Othamanga akungopezanapezana,

amithenganso akungotsatanatsatana.

Onsewo akukauza mfumu ya ku Babiloni

kuti mbali zonse za mzinda wake zalandidwa.

32Madooko onse alandidwa,

malo obisalako alonda atenthedwa,

ndipo ankhondo ake onse asokonezeka.

33Babiloni wokongola uja wangokhala ngati popunthira

tirigu pa nthaŵi yopuntha kumene.

Ndipotu posachedwa nthaŵi yake yokolola ifika,”

akutero Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele.

34A ku Yerusalemu akuti,

“Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, watiwononga,

Watitswanya ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu.

Watimeza ngati ng'ona.

Wakhuta ndi zakudya zathu zotsekemera,

kenaka nkutilavula.”

35Anthu okhala m'Ziyoni anene kuti,

“Zankhanza zimene Ababiloni

adatichita ife ndi ana athu ziŵabwerere.”

Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti,

“Magazi athu amene adamwazika

aŵagwere Ababiloniwo ngati chilango chao.”

Zakuti Chauta adzathandiza Aisraele

36Nchifukwa chake Chauta akunena kuti,

“Ndidzakumenyera nkhondo yako,

ndipo ndidzakulipsirira.

Ndidzaumitsa nyanja ya ku Babiloni,

akasupe ake onse adzaphwa.

37Motero Babiloni adzasanduka mulu wa nyumba zopasuka,

malo a nkhandwe, malo oopsa ndi onyozeka,

opanda wina wokhalamo.

38“Ababiloni adzakhuluma ngati mikango.

Adzadzuma ngati ana a mikango.

39Akachita dyera, ndidzaŵakonzera madyerero.

Tsono ndidzaŵaledzeretsa,

ndipo adzasangalala nkugona tulo tampakampaka,

osadzukanso ai.

40Ndidzapita nawo kuti akaphedwe ngati anaankhosa,

ngati nkhosa zamphongo kapena atonde,”

akutero Chauta.

Za tsoka la Babiloni

41“Ndithu Babiloni wagonjetsedwa,

mzinda umene dziko lonse lapansi

linkaunyadira walandidwa.

Ogo! Babiloni uja wasanduka chinthu

chonyansa pakati pa mitundu ya anthu!

42Nyanja yakwera mpaka kumiza Babiloni,

waphimbidwa ndi mafunde ake.

43Mizinda yake yasanduka malo onyansa,

dziko louma ndi lachipululu,

dziko lopanda anthu losayendako mwanawamunthu.

44Ndidzalanga Beli, mulungu wa Ababiloni,

ndidzamsanzitsa zimene adameza.

Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye.

Malinga a Babiloni agwa!

45Tulukani m'Babiloni, inu anthu anga!

Fulumirani, pulumutsani moyo wanu!

Thaŵani mkwiyo woopsa wa Chauta!

46Musataye mtima.

Musaope maphephe amene awanda m'dziko monse.

Chaka ndi chaka pamabuka ndithu maphephe

onena za nkhondo pa dziko lapansi,

ndiponso zakuti mfumu yakutiyakuti

ikumenyana ndi inzake.

47“Tsono ikudza nthaŵi

pamene ndidzalange mafano a Babiloni.

Dziko lonselo lidzachita manyazi.

Anthu ake onse ophedwa adzakhala ali

ngundangunda pakati pake.

48 Chiv. 18.20 Pambuyo pake dziko lakumwamba ndi dziko

lapansi ndi zonse zokhala m'menemo zidzaimba

mokondwera chifukwa cha kugwa kwa Babiloni.

Anthu oononga ochokera kumpoto adzamgonjetsa,”

akutero Chauta.

49 Chiv. 18.24 Babiloni ayeneradi kugwa chifukwa cha amene

adaphedwa ku Israele,

monga adagwera anthu a pa dziko lonse lapansi

amene adaphedwa ndi iyeyo.

Uthenga wa Chauta kwa Aisraele ku Babiloni

50“Inu amene mwapulumuka ku nkhondo ya Babiloni,

chokanipo apa, musazengereze.

Kumbukirani Chauta ngakhale muli kutali ndi kwanu,

muzimkumbukira Yerusalemu.

51Inu mukuti ‘Tikuchita manyazi

chifukwa cha manyozo amene talandira.

Nkhope zathu zagwa

chifukwa anthu achilendo aloŵa ku mabwalo

opatulika a ku Nyumba ya Chauta.’ ”

52Koma Chauta akunena kuti,

“Ikubwera nthaŵi

pamene ndidzalange mafano a ku Babiloni,

ndipo kubuula kwa anthu olasidwa

kudzamveka m'dziko lake lonse.

53Ngakhale Babiloni adzikweze mpaka ku mlengalenga,

nkulimbitsa nsanja zake,

ndidzatuma oononga kuti amgonjetse,”

akutero Chauta.

Kuwonongeka kwa Babiloni kunkirankira

54“Imvani mau olira m'Babiloni.

Imvani phokoso la kuwonongeka kwakukulu

m'dziko la Ababiloni.

55Ndithu, Chauta akuwononga Babiloni,

ndipo akuthetsa phokoso lake lalikulu.

Mfuu wa anthu ake ukumveka ngati mafunde amkokomo,

phokoso lake likukwererakwerera.

56Woononga amufikira Babiloni,

ndipo ankhondo ake onse agwidwa,

mauta ao athyoka.

Pajatu Chauta ndi Mulungu wolanga,

adzabwezeradi kwathunthu zoipa zao.

57Ndidzaledzeretsa akuluakulu ake pamodzi

ndi anzeru ake.

Ndidzaledzeretsa abwanamkubwa ake, atsogoleri

ankhondo, ndi ankhondo ake amene.

Adzagona tulo tampakampaka, tosadzuka nato,”

ikutero mfumu imene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.

58Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti,

“Malinga aakulu a Babiloni adzasalazidwa.

Zipata zake zazitali zidzatenthedwa.

Mitundu ya anthu idagwira ntchito pachabe,

anthu adangotopa nkumanga zimene tsopano

zikupsa ndi moto.”

Yeremiya atumiza uthenga ku Babiloni

59Mfumu Zedekiya anali ndi phungu wake wamkulu, dzina lake Seraya, mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseiya. Pa chaka chachinai cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, Seraya adatsagana ndi mfumuyo kupita ku Babiloni. Tsono mneneri Yeremiya adampatsirako uthenga Serayayo.

60Yeremiya anali atalemba m'buku za chiwonongeko chonse cha Babiloni, ndiponso za zina zonse zokhudza Babiloni.

61Yeremiyayo adauza Seraya kuti, “Pamene ukafike ku Babiloni, usakalephere kuŵaŵerengera anthu mau onseŵa.

62Ukanene kuti, ‘Inu Chauta, mwalengeza cholinga chanu chofuna kuwononga malo ano, osasiyapo kanthu, munthu kapena nyama. Ndipo adzakhala chipululu mpaka muyaya.’

63Chiv. 18.21 Ukakatha kuŵerenga bukulo, ukalimangire ku mwala, nkuliponya mu mtsinje wa Yufurate.

64Ndipo ukanene kuti, ‘Umu ndimo m'mene Babiloni adzamirire. Sadzadzukanso chifukwa cha zoopsa zonse zimene ndidzamgwetsere.’ ” Mau a Yeremiya athera pamenepa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help