Lk. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kubadwa kwa Yesu(Mt. 1.18-25)

1Masiku amenewo, Augusto, Mfumu ya ku Roma, adalamula kuti pakhale kalembera wa anthu a m'maiko ake onse.

2Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo adachitika pamene Kwirinio anali bwanamkubwa wa dziko la Siriya.

3Motero anthu onse adapita kukalembedwa, aliyense ku mudzi kwao.

4Yosefe nayenso adanyamuka kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya. Adapita ku Yudeya, ku mudzi wa mfumu Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa anali wa m'banja ndi fuko la Davideyo.

5Adapita kukalembedwa pamodzi ndi Maria, mkazi wake, amene anali ndi pathupi.

6Pamene anali kumeneko, nthaŵi yake yoti Maria achire idakwana,

7ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m'nsalu namgoneka m'chodyera cha zoŵeta, chifukwa adaasoŵa malo m'nyumba ya alendo.

Angelo adziŵitsa abusa

8Ku dera lomwelo kunali abusa amene ankalonda zoŵeta zao ku dambo usiku.

9Tob. 5.4Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye adadzaimirira pakati pao, ndipo ulemerero wa Ambuye udaŵala ponse pozungulira, mwakuti abusawo adaachita mantha kwambiri.

10Koma mngeloyo adaŵauza kuti, “Musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri.

11Usiku womwe uno m'mudzi wa Davide wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

12Chitsimikizo chake ndi ichi: mukapeza mwana wakhanda, wokutidwa ndi nsalu, atagona m'chodyera cha zoŵeta.”

13Mwadzidzidzi pamodzi ndi mngeloyo padaoneka gulu lalikulu la angelo ena. Ankatamanda Mulungu ndi mau akuti,

14“Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba,

ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu

amene Iye amakondwera nawo.”

15Angelowo atachoka kubwerera Kumwamba, abusa aja adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tipite ku Betelehemu, tikaone zachitikazi, zimene Ambuye atidziŵitsa.”

16Tsono adapita mofulumira, nakapeza Maria ndi Yosefe, atagoneka mwana wakhandayo m'chodyera cha zoŵeta chija.

17Pamene adamuwona, abusawo adaŵafotokozera zimene mngelo uja adaaŵauza za mwanayo.

18Onse amene ankamva, ankadabwa ndi zimene abusawo ankaŵasimbira.

19Koma Maria adasunga zonsezo namazilingalira mumtima mwake.

20Pambuyo pake abusa aja adabwerera akuyamika ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anali atamva ndi kuziwona. Zonse zinali monga momwe mngelo uja adaaŵauzira.

Yesu aumbalidwa ndi kuperekedwa ku Nyumba ya Mulungu

21 Lev. 12.3; Lk. 1.31 Patapita masiku asanu ndi atatu, mwana uja adamuumbala namutcha dzina lake Yesu. Dzinali ndi lomwe lija limene mngelo adaatchula, Maria asanatenge pathupi.

22Kenaka idafika nthaŵi yoti Yosefe ndi Maria achite mwambo wakuyeretsedwa potsata Malamulo a Mose. Tsono mwanayo adapita naye ku Yerusalemu kuti akampereke kwa Ambuye.

23Eks. 13.2, 12 Pajatu m'Malamulo a Ambuye muli mau akuti, “Mwana aliyense wamwamuna, woyamba kubadwa, apatulidwe kuti akhale wao wa Ambuye.”

24Lev. 12.6-8 Adakaperekanso nsembe potsata Malamulo a Ambuye akuti, “Apereke njiŵa ziŵiri kapena maunda aŵiri.”

25Ku Yerusalemuko kunali munthu wina, dzina lake Simeoni. Anali munthu wolungama ndi woopa Mulungu. Ankayembekezera nthaŵi yoti Mulungu adzapulumutse Aisraele, ndipo Mzimu Woyera anali naye.

26Mzimu Woyerayo adaamuululira kuti sadzafa asanaone Mpulumutsi amene Mulungu adaalonjeza.

27Tsiku lina Mzimu Woyera adamlamula kuti apite ku Nyumba ya Mulungu. Makolo a Yesu adaloŵanso m'Nyumbamo ndi mwana waoyo kukamchitira mwambo potsata Malamulo a Mose.

28Pamenepo Simeoni adalandira mwanayo m'manja mwake, nayamba kutamanda Mulungu ndi mau akuti,

29“Ambuye, tsopano mundilole ine mtumiki wanu,

ndipite ndi mtendere,

pakuti mwachitadi zija mudaalonjezazi.

30Ndi maso angaŵa ndachiwonadi chipulumutso chija,

31chimene mudakonza kuti anthu a mitundu yonse achiwone.

32 Yes. 42.6; 49.6; 52.10 Mwapereka kuŵala kodzaunikira anthu a mitundu ina,

kodzakhala ulemerero wa anthu anu Aisraele.”

33Atate ndi amai a mwanayo ankangodabwa nazo zimene Simeoni ankanena za mwanayo.

34Kenaka Simeoniyo adaŵadalitsa, nauza Maria, mai wa mwanayo, kuti,

“Mwanayu Mulungu wamuika

kuti Aisraele ambiri adzagwe, ambirinso adzadzuke,

chifukwa cha iyeyu.

Adzakhala chizindikiro chochokera kwa Mulungu,

chimene anthu ambiri adzatsutsana nacho,

35kuti choncho maganizo amene ali m'mitima ya anthu ambiri

adzaonekere poyera.

Ndipo inunso mai, chisoni chidzabaya mtima wanu ngati lupanga.”

36 Yud. 8.4, 5 Kunalinso mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere. Anali wokalamba kwambiri. Anali atakhala pa banja zaka zisanu ndi ziŵiri zokha,

37pambuyo pake nkukhala wamasiye kufikira msinkhu wa zaka 84. Sankachokatu ku Nyumba ya Mulungu, ankakonda kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku pakupemphera ndi kusala zakudya.

38Iye adafikako nthaŵi yomweyo, nayamba kuyamika Mulungu, nkumakamba za Mwanayo ndi anthu onse amene ankayembekezera nthaŵi yoti Mulungu adzapulumutse Yerusalemu.

Abwerera ku Nazarete

39 Mt. 2.23 Yosefe ndi Maria atachita zonse potsata Malamulo a Ambuye, adabwerera ku Galileya, kumudzi kwao ku Nazarete.

40Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa.

Yesu pakati pa aphunzitsi

41 Eks. 12.1-27; Deut. 16.1-8 Makolo a Yesu ankapita ku Yerusalemu chaka ndi chaka ku chikondwerero cha Paska.

42Pamene Yesu anali ndi zaka khumi ndi ziŵiri, iwo adapita kumeneko monga adaazoloŵera.

43Masiku a chikondwererocho atatha, adanyamuka kumabwerera kwao, mnyamata uja Yesu nkutsalira ku Yerusalemu, makolo ake osadziŵa.

44Iwo ankayesa kuti ali pamodzi ndi anzao aulendo, choncho adayenda ulendo wa tsiku limodzi. Tsono adayamba kumufunafuna pakati pa abale ao ndi abwenzi ao.

45Ataona kuti sakumpeza, adabwerera ku Yerusalemu akumufunafuna ndithu.

46Patapita masiku atatu, adampeza m'Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera mau ao, ndi kumaŵafunsa mafunso.

47Onse amene ankamva mau ake, ankadabwa ndi mayankho ake anzeru.

48Pamene makolo ake adamuwona, adadabwa, ndipo mai wake adamufunsa kuti, “Mwana iwe, watisautsiranji chotere? Ine ndi bambo wako tavutika nkukufunafuna.”

49Koma Yesu adati, “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kani simumadziŵa kuti ndiyenera kupezeka m'nyumba ya Atate anga?”

50Koma iwo sadamvetse zimene adaŵayankhazo.

51Tsono Yesu adabwerera nawo pamodzi, nafika ku Nazarete, ndipo ankaŵamvera. Mai wake ankasunga zonsezi mumtima mwake.

521Sam. 2.26; Miy. 3.4Ndipo Yesu analikunka nakula m'nzeru ndi mu msinkhu, ndipo Mulungu ndi anthu omwe ankakondwera naye kwambiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help