Yob. 41 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mas. 74.14; 104.26; Yes. 27.1 Kodi ungathe kuchikoka ndi

mbedza ya nsomba chilombo chija cha Leviyatani,

kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe?

2Kodi ungathe kuchimanga chingwe m'mphuno mwake,

kapena kuchiboola nsagwada ndi mbedza?

3Kodi chidzakupempha kuti uchimasule?

Kodi chidzakupemba kuti uchichitire chifundo?

4Kodi chidzachita nawe chipangano

kuti chikhale chokutumikira mpaka muyaya?

5Kodi ungaseŵere nacho ngati mbalame?

Kodi kapena nkuchimanga ndi unyolo

kuti adzakazi ako aseŵere nacho?

6Kodi asodzi nkuchitsatsa malonda?

Nanga amalondawo nkugaŵanagaŵana

nyama yake kuti akaigulitse?

7Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi ntcheto,

kapena kuboola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba?

8Ukachiputa, udziŵe kuti pali nkhondo,

ndipo iweyo sudzabwereranso.

9Ndithu, aliyense akachiwona chilombocho, amataya mtima,

ndipo amangodzigwera ndi mantha.

10Ngati palibe wina woti angalimbe mtima nkuchiputa.

Nanga ndani angalimbe mtima nkukangana ndi Ine Mulungu?

11Kodi ndani adandipatsa kanthu, kuti Ineyo ndimbwezere?

Zonse za pansi pa thambo ndi zanga.

12“Sindingaleke kulankhula

za ziwalo zake za chilombocho,

za mphamvu zake ngakhalenso za maonekedwe a thupi lake.

13Ndani angasende chikopa chake?

Ndani angachibaye chikopa chimene chija,

kulimba konse kuja ngati chovala chachitsulo?

14Ndani angatsekule kukamwa kwake?

Mano ake ndi oopsa.

15Kumsana kwake kuli mizere ya mamba

onga zishango zolumikizanalumikizana,

onse olimba ngati mwala.

16Mambawo ndi olukanalukana,

kotero kuti ndi mpweya womwe

sungathe kuloŵa pakati pake.

17Ndi olumikizanalumikizana, ndi omamatirana kwambiri,

kotero kuti sangathe kutayana.

18Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali,

maso ake amaŵala ngati kuŵala kwa mbandakucha.

19M'kamwa mwake mumatuluka nsakali za moto,

mumathetheka mbaliwali za moto.

20M'mphuno mwake mumatuluka utsi,

ngati wa m'nkhali yogaduka

ndiponso ngati wa moto wa mlulu.

21Mpweya wake umayatsa makala,

malaŵi a moto amatuluka m'kamwa mwake.

22Khosi lake ndi lamphamvu kwambiri,

aliyense wokumana nacho amangoti njenjenje ndi mantha.

23Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana,

ndi yokhwima kwambiri, ndipo ndi yolimba.

24Pachifuwa pake mpouma ngati mwala.

Pali gwa! Ngati mwala wa mphero.

25Chilombocho chikangoti vuuku,

ndi amphamvu omwe amaopa.

Akamva phokoso lake, amachita mantha.

26Ngakhale lupanga lichikanthe, silichichita kanthu.

Mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera.

27Chitsulo chimachiyesa phesi chabe,

mkuŵa chimauyesa chikuni choola.

28Muvi sungathe kuchithaŵitsa,

Miyala imene achilasa nayo, chimangoinyenyanyenya.

29Zibonga zimakhala ngati ziputu.

Akamachitchaya ndi nthungo, icho chimangoseka.

30Za kumimba kwake zili ngati mapale akuthwa.

Chimatambalala m'matope

ngati galeta lopunthira tirigu.

31Chimagadutsa madzi ozama ngati madzi am'nkhali,

chimasandutsa nyanja kuti igaduke

ngati mbiya yoyengeramo mafuta.

32Kumbuyo kwake chimasiya nthubwitubwi zambee,

kotero kuti munthu angaganize

kuti nyanja yachita imvi.

33Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho,

ncholengedwa chopanda mantha.

34Chimanyoza nyama zina zonse.

Icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.”

Mau omaliza a Yobe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help