1“Naŵa maina a mafuko: kuyambira ku malire akumpoto kuchokera ku nyanja, kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazarenoni, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyang'anana ndi Hamati, ndipo kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, nchigawo chimodzi, ndipo ncha Dani.
2Kuchitana malire ndi Dani, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Asere.
3Kuchitana malire ndi Asere kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Nafutali.
4Kuchitana malire ndi Nafutali kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Manase.
5Kuchitana malire ndi Manase kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Efuremu.
6Kuchitana malire ndi Efuremu kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Rubeni.
7Kuchitana malire ndi Rubeni kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Yuda.
8Kuchitana malire ndi Yuda kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo chapadera ndithu. Muufupi mwake chikhale makilomita 12 ndi theka. M'litali mwake chikhale ngati zigawo zina, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Ndipo malo a Nyumba ya Chauta akhale pakati pake.”
Dziko la Chauta9“Chigawo chimene muchipatule kuti chikhale cha Chauta chikhale cha makilomita 12 ndi theka m'litali mwake, muufupi mwake chikhale cha makilomita khumi.
10Chigawocho chigaŵidwe motere: chigawo cha Ansembe chikhale cha makilomita 12 ndi theka kumpoto. Kuzambwe chikhale cha makilomita khumi. Kuvuma chikhale cha makilomita asanu. Kumwera chikhale cha makilomita 12 ndi theka. Malo a Nyumba ya Chauta akhale pakatimpakati.
11Chimenechi chikhale chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene adamvera malamulo anga, osatsata Aisraele pamene adaasokera, monga m'mene adaachitira Alevi.
12Chigawo chimenechi, pakati pa zigawo zonse, chidzakhale mphatso yapadera kwa ansembewo, ndipo chikhale chopatulika kwambiri. Chichitane malire ndi dziko la Alevi.”
13“Tsono chigawo cha Alevi chikhale choyandikana ndi chigawo cha ansembe. M'litali mwake chikhale cha makilomita 12 ndi theka. Muufupi mwake chikhale cha makilomita asanu. Chigawo chonsechi m'litali mwake mukhale cha makilomita 12 ndi theka, ndipo muufupi mwake mukhale makilomita asanu.
14Asagulitse kapena kusinthitsa mbali iliyonse ya chigawo chimenechi. Ndi chigawo chapadera ndithu ndipo asachipatse ena, pakuti ndi malo opatulikira Chauta.”
15“Chigawo chotsala muufupi mwake chikhale cha makilomita aŵiri ndi hafu, m'litali mwake makilomita 12 ndi theka. Chikhale malo omangapo mzinda ndiponso busa. Mzinda ukhale pakatimpakati.
16Miyeso yake ikhale iyi: Kumpoto kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kumwera kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kuvuma kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kuzambwe kutalika kwake kukhale mamita 2,250.
17Dera la busa likhale motere: kumpoto kutalika kwake kukhale mamita 125. Kumwera kutalika kwake kukhale mamita 125. Kuvuma kutalika kwake kukhale mamita 125. Ndipo kuzambwe kutalika kwake kukhale mamita 125.
18Chigawo chotsala pafupi ndi chigawo chopatulika, kutalika kwake makilomita asanu kuvuma, makilomita asanu kuzambwe. Chikhale dziko la minda ya anthu ogwira ntchito mu mzinda.
19Anthu ogwira ntchito mu mzinda, ochokera m'fuko lililonse la Israele, ndipo azilima chigawocho.
20Tsono chigawo chathunthu chopatulikacho chikhale cha makilomita 12 ndi theka mbali zonse, ndiye kuti chigawo chopatulikacho pamodzi ndi kadziko ka mzindawo.”
Dziko la Mfumu21“Tsono chigawo chotsala pa mbali zonse ziŵiri za chigawo chopatulika ndi za kadziko ka mzinda, chikhale cha mfumu. Chidzayenda motere: kuyambira m'malire a chigawo chopatulika kukalekeza m'malire akuvuma, mbali ina kuyambiranso m'malire a chigawo chopatulika kukalekeza m'malire akuzambwe, kumapaza kufupi ndi zigawo za mafuko, dera lonselo likhale la mfumu. Chigawo chopatulika ndi malo oyera a Nyumba ya Mulungu zikhale pakatimpakati.
22Chigawo cha Alevi ndi chigawo cha mzinda zikhale pakati pa dera la mfumulo. Dera limenelo lidzakhale pakatimpakati pa dziko la Yuda ndi la Benjamini.”
Dziko la mafuko ena23“Za mafuko ena otsala zidzayenda motere: kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe padzakhala chigawo chimodzi, chimenechi ncha Benjamini.
24Kuchitana malire ndi Benjamini, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Simeoni.
25Kuchitana malire ndi Simeoni, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Isakara.
26Kuchitana malire ndi Isakara, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Zebuloni.
27Kuchitana malire ndi Zebuloni, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Gadi.
28Malire a Gadi mbali yakumwera ku Negebu achokere kumwera kuyambira ku Tamara mpaka ku Dziŵe la Meriboti-Kadesi, kenaka kuchokera ku Mtsinje wa ku Ejipito, kukafika ku Nyanja Yaikulu.
29Dziko lonselo ndilo mupatse mafuko a Israele kuti likhale choloŵa chao. Zigawo zimenezi zidzakhala zao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Zipata za Yerusalemu30 Chiv. 21.12, 13 “Aŵa ndiwo akhale makomo otulukira mu mzinda, ndipo atchulidwe maina a mafuko a Aisraele. Kumpoto, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250,
31kukhale zipata zitatu: chipata cha Rubeni, cha Yuda, ndi cha Levi.
32Kuvuma, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250, kukhale zipata zitatu: chipata cha Yosefe, cha Benjamini ndi cha Dani.
33Kumwera, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250, kukhale ndi zipata zitatu: chipata cha Simeoni, cha Isakara ndi cha Zebuloni.
34Kuzambwe, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250, kukhale zipata zitatu: chipata cha Gadi, cha Asere ndi cha Nafutali.
35Choncho kutalika kwa mzindawo kuzungulira ponse kukhale mamita 9,000, ndipo dzina la mzindawo mpaka muyaya likhale ‘Chauta-ali-pano.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.