1Naŵa anthu amene adadza kwa Davide ku Zikilagi, kumene Davideyo adaathaŵira chifukwa choopa Saulo mwana wa Kisi. Anthu ameneŵa ankathandiza Davide kumenya nkhondo, pamodzi ndi anzao amphamvu.
2Iwoŵa anali anthu odziŵa kugwiritsa ntchito uta. Mivi ndi miyala ankatha kuponyera dzanja lamanja kapena lamanzere. Iwoŵa anali Abenjamini, abale ake a Saulo.
3Mtsogoleri wao anali Ahiyezere, wotsatana naye anali Yowasi. Aŵiri onsewo anali ana a Semaa wa ku Gibea. Panalinso Yeziyele ndi Peleti, ana a Azimaveti, Beraka, Yahu wa ku Anatoti,
4ndi Isimaya wa ku Gibiyoni, amene anali wamphamvu mwa anthu makumi atatu aja ndiponso mmodzi mwa atsogoleri ao. Panalinso Yeremiya, Yahaziele, Yohanani, Yozabadi wa ku Gedera,
5Eluzai, Yeremoti, Bealiya, Semariya, Sefatiya wa ku Harufi,
6Elikana, Isiya, Azarele, Yowezere, ndiponso Yasobeamu. Onsewo anali Akora.
7Panalinso Yowela ndi Zebadiya, ana a Yerohamu wa ku Gedori.
Anthu otsatira Davide a fuko la Gadi8Asilikali ena amphamvu, ochokera ku dziko la Gadi, adafika kwa Davide ku linga lake lam'chipululu. Iwoŵa anali ngwazi zodziŵa kumenya nkhondo, makamaka pogwiritsa ntchito chishango ndi mkondo, ndipo anali oopsa ngati mikango. Akamathamanga, ngati ngoma zam'mapiri liŵiro lake.
9Ezere anali mtsogoleri, wachiŵiri anali Obadiya, wachitatu Eliyabu,
10wachinai Misimana, wachisanu Yeremiya,
11wachisanu ndi chimodzi Atai, wachisanu ndi chiŵiri Eliyele,
12wachisanu ndi chitatu Yohanani, wachisanu ndi chinai Elizabadi,
13wa 10 Yeremiya, wa 11 Makibanai.
14Agadi ameneŵa ndiwo amene anali m'gulu la atsogoleri ankhondo. Ang'onoang'ono ankalamulira anthu 100, pamene akuluakulu ankalamulira anthu 1,000.
15Ameneŵa ndiwo anthu amene adaoloka Yordani mwezi woyamba, nthaŵi imene mtsinjewo unali wodzaza nkumasefukira pa zibumi zake zonse. Motero adapirikitsa anthu onse amene anali m'zigwa. Ena kuthaŵira kuvuma ena kuzambwe.
16Tsiku lina anthu ena a ku Benjamini ndi a ku Yuda adadza ku linga la Davide.
17Davide adatuluka kukakumana nawo, ndipo adaŵauza kuti, “Ngati mwadza kwa ine kuno mwaubwenzi kuti mudzandithandize, ndiye kuti mtima wanga udzagwirizana nanu. Koma ngati nkundipereka kwa adani anga, ngakhale sindidalakwe, pamenepo Mulungu wa makolo athu apenye ndipo akulangeni.”
18Pomwepo Mzimu wa Mulungu udamtsikira Amasai, mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja, ndipo adati,
“Inu Davide, ifetu ndife anu.
Tili limodzi nanu, inu mwana wa Yese.
Inu ndi anthu amene amakuthandizani,
mudzakhala opambana.
Zoonadi Mulungu wanu ali nanu.”
Tsono Davide adaŵalandira ndipo adaŵasandutsa atsogoleri a magulu ake ankhondo.
Otsata Davide a fuko la Manase19Anthu ena a fuko la Manase adabwera kwa Davide nthaŵi imene Davide adadza ndi Afilisti kudzamenyana nkhondo ndi Saulo. Komabe nthaŵiyo Davide sadaŵathandize Afilisti, poti akazembe ao adambweza namanena kuti, “Uyu akhoza kubwerera kwa mbuye wake Saulo, ndiye ife tidzaonongeka pamenepo.”
20Motero pamene Davide ankabwerera ku Zikilagi, anthu a fuko la Manase aja adapita naye limodzi. Amanasewo anali aŵa: Adina, Yozabadi, Yediyaele, Mikaele, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai, atsogoleri a magulu a ankhondo zikwi zambiri a ku Manase.
21Iwoŵa adathandiza Davide kulimbana ndi magulu a achifwamba, pakuti onseŵa anali anthu amphamvu, olimba mtima, ndipo anali atsogoleri pa nkhondo.
22Anthu ankabwera kwa Davide tsiku ndi tsiku kudzamthandiza, mpaka gulu lake lankhondo lidakula kwambiri, ngati gulu lankhondo la Mulungu.Ankhondo a Davide
23Nachi chiwerengero cha magulu a anthu ankhondo amene adadza ku Hebroni kwa Davide, kudzamlonga ufumu m'malo mwa Saulo, potsata mau a Chauta.
24Ankhondo a ku Yuda ogwira zishango ndi mikondo analipo 6,800.
25A fuko la Simeoni, anthu amphamvu olimba mtima pomenya nkhondo, 7,100.
26A fuko la Levi, 4,600.
27Mtsogoleri Yehoyada wa banja la Aroni adabwera ndi anthu 3,700.
28Zadoki mnyamata wolimba mtima adabwera ndi achibale ake 22.
29A fuko la Benjamini, abale ake a Saulo, analipo 3,000. Koma mpaka pa nthaŵi imeneyo, ambiri mwa iwowo ankaumirirabe kumatsata banja la Saulo.
30A banja la Efuremu, 20,800 anthu amphamvu ndi olimba mtima, anthu omveka ku mabanja a makolo ao.
31A fuko lahafu la Manase analipo 18,000, amene adaachita kuŵaitana kuti adzalonge nao ufumu Davide.
32A fuko la Isakara analipo atsogoleri 200 pamodzi ndi anthu ao. Atsogoleriwo ankamvetsa zinthu pa nthaŵi imeneyo, namadziŵa zimene Israele ankayenera kuchita pa nthaŵi yake.
33A fuko la Zebuloni analipo 50,000 asilikali okonzekera nkhondo, okhala ndi zida zankhondo zamitundumitundu, othandiza Davide ndi mtima umodzi.
34A fuko la Nafutali, atsogoleri 1,000 amene anali ndi asilikali 37,000 a zishango ndi mikondo.
35A fuko la Dani, anthu 28,600 okonzekera kumenya nkhondo.
36A fuko la Asere anali 40,000, ankhondo enieni, okonzekera kumenya nkhondo.
37A fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi fuko lahafu la Manase, kuchokera pa tsidya ilo la mtsinje wa Yordani, analipo 120,000 odziŵa kumenya nkhondo ndi zida zosiyanasiyana.
38Ankhondo onseŵa amene ankadziŵa kamenyedwe ka nkhondo, adadza ku Hebroni ndi mtima umodzi, kuti akamlonge ufumu Davide. Aisraele onse nawonso anali ndi mtima womwewo wofuna kumlonga ufumu Davide.
39Ndipo adakhala komweko masiku atatu pamodzi ndi Davide namadya zimene abale ao anali ataŵakonzekera.
40Nawonso anansi ao, ochokera ngakhale ku Isakara ndi Zebuloni ndi Nafutali, adadza atasenzetsa chakudya abulu ao, ngamira zao, nyulu zao ndi ng'ombe zao. Adazisenzetsa chakudya chambiri, makeke ankhuyu, ntchichi zamphesa, vinyo ndiponso mafuta. Adabweranso ndi ng'ombe ndi nkhosa zambiri, poti ku dziko la Israele kunali chisangalalo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.