1Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
2“Lamulo limene Chauta wapereka nali: Muuze Aisraele kuti abwere ndi msoti wa ng'ombe wofiira, wosapunduka, wopanda chilema, ndiponso umene sudasenzepo goli chiyambire.
3Muupereke kwa wansembe Eleazara, kenaka anthu atuluke nawo kunja kwa mahema, ndipo auphe pamaso pake.
4Tsono wansembe Eleazara atengeko magazi a ng'ombeyo ndi chala chake, ndipo awaze magaziwo kumaso kwa chihema chamsonkhano kasanunkaŵiri.
5Ng'ombeyo aitenthe, Eleazara akupenya. Chikopa chake, nyama yake, magazi ake pamodzi ndi ndoŵe yake, azitenthe zonsezo.
6Wansembe atenge mtengo wa mkungudza, kachitsamba ka hisope ndi kansalu kamlangali, ndipo zonsezo aziponye m'moto m'mene ng'ombe ija ikunyekamo.
7Tsono wansembe achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, pambuyo pake aloŵe m'mahema. Koma wansembeyo adzakhale woipitsidwa mpaka madzulo.
8Munthu amene atentha ng'ombeyo achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma adzakhalebe woipitsidwa mpaka madzulo.
9Ahe. 9.13 Munthu amene ali wosaipa pa zachipembedzo ndiye aole phulusa la ng'ombelo, ndipo aliike kunja kwa mahema pa malo aukhondo pa zachipembedzo. Asungire mpingo wa Aisraele phulusalo, kuti aziika m'madzi oyeretsera zonyansa pa zachipembedzo. Mwambo umenewu ndi wochotsera tchimo.
10Munthu amene aola phulusa la ng'ombe achape zovala, koma iyenso adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Limeneli likhale lamulo lamuyaya kwa Aisraele ndi kwa mlendo wokhala pakati pao.
Za kukhudza mtembo11“Amene akhudza mtembo wa munthu wina aliyense, akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri.
12Asambe ndi madzi oyeretsera aja pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri kuti ayere, ndipo adzamuyeretsadi. Koma akapanda kusamba pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri kuti ayere, sadzayera.
13Munthu aliyense wokhudza munthu wakufa, ndipo sadziyeretsa, munthu ameneyo akuipitsa Chihema cha Chauta, choncho adzachotsedwa m'dziko la Aisraele. Akhale woipitsidwa chifukwa sadawazidwe madzi aja oyeretsera pa zachipembedzo, ndi woipitsidwabe ameneyo.
14“Pamene munthu afera m'hema, lamulo lake nali: munthu aliyense amene aloŵa m'hemamo, ndipo aliyense amene ali m'hema, akhale woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri.
15Ndipo chiŵiya chilichonse chopanda chivundikiro nchoipitsidwa.
16Munthu aliyense amene akhudza munthu wophedwa ndi lupanga panja, kapena mtembo, kapena fupa la munthu wakufa, kapenanso manda, akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri.
17Woipitsidwayo amtengereko m'mbiya phulusa la nsembe yopsereza yopepesera machimo, ndipo aonjezemo madzi abwino atsikulo.
18Tsono munthu wosaipitsidwa atenge kachitsamba ka hisope ndi kukaviika m'madzi aja, ndipo awaze madziwo pa hema, pa zipangizo zake zonse, pa anthu amene anali m'menemo, ndi pa munthu amene adakhudza fupa la munthu wakufa, kapena munthu wophedwa, kapena chikulu mtembo kapena manda.
19Munthu wosaipitsidwayo awaze madzi munthu woipitsidwa uja, pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Atawazidwa madzi choncho pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, achape zovala zake, asambe thupi lonse, ndipo madzulo ake adzakhala woyeretsedwa.
20“Koma munthu woipitsidwa akapanda kudziyeretsa, ameneyo achotsedwe pakati pa msonkhano, pakuti waipitsa malo opatulika a Chauta. Ameneyo ndi woipitsidwa chifukwa sadamuwaze madzi oyeretsera aja.
21Limeneli likhale lamulo lamuyaya kwa iwo. Munthu amene awaza madzi oyeretserawo, achape zovala zake. Ndipo munthu amene akhudza madzi ochapirawo, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.
22Chinthu chilichonse chimene munthu woipitsidwa akhudza, chidzakhala choipitsidwa. Ndipo munthu aliyense wokhudza chimenecho, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.