1Mabanja onse a fuko la Yuda adalandira chigawo cha dzikolo motero: dziko lao lidalekeza ku malire a Edomu, mpaka ku chipululu cha Zini, kumwera kwenikweni.
2Malire ake akumwera adayambira kumwera kwenikweni kwa Nyanja Yakufa,
3napita cha kumwera kokhakokha kuyambira ku chikweza cha ku Akarabimu, nkudzera pa mpata wa mapiri a ku Zini. Kuchokera kumeneko, adabzola cha kumwera kwa Kadesi-Baranea, kupitirira Hezironi mpaka ku Adara, ndi kutembenukira ku Karaka.
4Adapitirira mpaka ku Azimoni, natsata mtsinje wa m'malire a Ejipito mpaka ku nyanja. Ameneŵa ndiwo malire akumwera.
5Malire akuvuma anali Nyanja Yakufa mpaka kumene Yordani amathira m'Nyanja Yakufa. Tsono malire akumpoto adayambira kunyanjako,
6napitirira mpaka ku Betehogila, nakafika kumpoto kwa Betaraba. Adapitirira mpaka kukafika ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni.
7Ndipo malirewo adachokeranso ku chigwa cha Mavuto mpaka ku Debiri, mpakanso kumpoto kuloŵera ku Giligala, kuyang'anana ndi chikweza cha Adumimupasi cha ku mbali yakumwera ya chigwa. Tsono adapitiriranso ku akasupe a Enisemesi, natulukira ku Enirogele.
8Ndipo adakwera kubzola chigwa cha mwana wa Hinomu cha mbali ya kumwera kwa Ayebusi, (ndiye kuti ku Yerusalemu). Malirewo adapitirira kukafika pamwamba pa phiri moyang'anana ndi chigwa cha Hinomu chakuzambwe, ku mathero akumpoto a chigwa cha Refaimu.
9Tsono adachokeranso pamwamba pa phiri, nakafika mpaka ku akasupe a Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya ku phiri la Efuroni. Kuchoka uko nkutsikira ku Baala, (ndiye kuti Kariyati-Yearimu),
10kumene adazungulira cha kuzambwe kwa Baala, kuloza ku dziko lamapiri la Seiri. Adapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu, (ndiye kuti Kesaloni), natsikira ku Betesemesi mpaka kubzola Timna.
11Tsono malirewo adatulukira ku matsitso a phiri cha kumpoto kwa Ekeroni. Adakhotera ku Sikeroni, kubzola phiri la Baala, mpaka kukafika ku Yabinele. Malire amenewo adakathera ku nyanja.
12Kuzambwe malire anali gombe la Nyanja Yaikulu yomwe. Ameneŵa ndiwo malire amene adazungulira maiko opatsidwa kwa fuko la Yuda.
Kalebe agonjetsa Hebroni ndi Debiri.13 Owe. 1.20 Monga momwe Chauta adalamulira Yoswa, gawo lina la dziko la fuko la Yuda lidapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune. Yoswa adampatsa Kiriyati-Ariba ndiye kuti Hebroni. (Araba anali bambo wa Anaki).
14Kalebe adapirikitsa mafuko atatu a Anaki m'dzikomo, maina ao ndi aŵa: Sesai, Ahimani ndi Talimai.
15Kuchokera kumeneko adapita kukalimbana ndi anthu a ku Debiri. Mzinda umenewu kale unkatchedwa Kiriyati-Sefere.
16Tsono Kalebe adati, “Mkulu wa ankhondo amene athire nkhondo mzinda wa Kiriyati-Sefere, naulanda, ndidzampatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.”
17Mbale wake wa Kalebe, Otiniyele, mwana wa Kenazi, adaulanda mzindawo. Choncho Kalebe adampatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.
18Tsiku lina, Akisayo atafika, Otiniyele adaumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe bambo wake. Tsono Akisa atatsika pa bulu wake, Kalebe adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kanthu?”
19Iye adayankha kuti, “Ndimati mundipatseko mphatso. Popeza kuti mwandikhazika m'dziko la Negebu lopanda madzi, mundipatsenso akasupe a madzi.” Choncho Kalebe adampatsa akasupe akumtunda ndi akuchigwa omwe.
Dziko lopatsidwa kwa Yuda.20Ili ndilo dziko limene mabanja a fuko la Yuda adalandira ngati choloŵa chao.
21Mizinda ya kumwera kwenikweni imene iwo adalandira yoyandikana ndi dziko la Edomu, inali iyi: Kabizeele, Edere, Yaguru,
22Kina, Dimona, Adada,
23Kedesi, Hazori, Itinani,
24Zifi, Telemu, Bealoti,
25Hazori-Hadata, Keriyoti-Hezironi, (ndiye kuti Hazori),
26Amama, Sema, Molada,
27Hazaragada, Hesimoni, Betepeleti,
28Hazara-Suwala, Beereseba, Biziyotiya,
29Baala, Iyimu, Ezemu,
30Elitoladi, Kesili, Horoma,
31Zikilagi, Madimana, Sanisana,
32Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni. Yonse inalipo mizinda 29, pamodzi ndi midzi yake yozungulira yomwe.
33Mizinda yakuchigwa inali iyi: Esitaoli, Zora, Asina,
34Zanowa, Enganimu, Tapuwa, Enamu,
35Taramuti, Adulamu, Soko, Azeka,
36Saraimu, Aditaimu, Gedera ndi Gederotaimu. Yonse inalipo mizinda 14, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
37Panalinso Zenani, Hadasa, Megidali-Gadi,
38Dileani, Mizipa, Yokotele,
39Lakisi, Bozikati, Egiloni,
40Kaboni, Lahamasi, Kitilisi,
41Gederoti, Betedagoni, Naama ndiponso Makeda. Yonse inali mizinda 16, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
42Panalinso Libina, Eteri, Asani,
43Ifuta, Asana, Nezibu,
44Keila, Akizibu ndi Maresa. Yonse inali mizinda isanu ndi inai, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
45Panalinso Ekeroni ndi midzi yake.
46Yonse imene inali m'mbali mwa Nyanja Yaikulu, kuchokera ku Ekeroni mpaka ku Asidodi.
47Adalandiranso mizinda yaikulu ya Asidodi ndi Gaza, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Malire ake adafika ku mtsinje wa ku Ejipito, ndipo mpaka ku Nyanja Yaikulu.
48Ku dziko lakumapiri kunali Samiri, Yatiri, Soko,
49Dana, Kiriyati-Sana, (ndiye kuti Debiri),
50Anabu, Esitemowa, Animu,
51Goseni, Holoni ndi Gilo. Yonse inalipo 11, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
52Panalinso Arabu, Duma, Esani,
53Yanimu, Betetapuwa, Afeka,
54Humata, Kiriyati-Ariba (ndiye kuti Hebroni), ndi Aziyori. Yonse inalipo isanu ndi inai, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
55Panalinso Maoni, Karimele, Zifi, Yuta,
56Yezireele, Yokodeamu, Zanowa,
57Kaini, Gibea ndi Timna. Yonse inalipo mizinda khumi, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
58Panalinso Halahulu, Betezuri, Gedori,
59Maarati, Betanoti ndi Elitekoni. Yonse inalipo mizinda isanu ndi umodzi, kuphatikizapo midzi yake yozungulira.
60Panalinso Kiriyati-Baala (ndiye kuti Kiriyati-Yearimu) ndi Raba. Yonse inalipo mizinda iŵiri, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
61Mizinda yam'chipululu inali Betaraba, Midini, Sekaka,
62Nibisani, mzinda wa Mchere ndi Engedi. Yonse inalipo mizinda isanu ndi umodzi, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
63 Owe. 1.21; 2Sam. 5.6; 1Mbi. 11.4 Koma anthu a fuko la Yuda sadathe kupirikitsa Ayebusi amene ankakhala ku Yerusalemu. Ndipo mpaka pano Ayebusiwo amakhalabe mu Yerusalemu, pamodzi ndi anthu a fuko la Yuda.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.