Mla. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Choipa china chimene ndachiwona pansi pano, chimene chimaŵaŵa anthu zedi, ndi ichi:

2Mulungu kukulemeretsa, kukupatsa chuma ndi ulemu, osasoŵa kanthu kalikonse kamene ukukalakalaka, koma tsono osakupatsa mwai woti udyerere zinthuzo, wodyerera nkukhala munthu wachilendo. Zimenezi nzothetsa nzeru, ndipo ndi vuto lokhumudwitsa kwambiri.

3Munthu ngakhale abale ana zana limodzi, nkukhala ndi moyo zaka zambiri, ngakhale zaka zakezo zichuluke chotani, ngati sakondwerera zinthu zabwino za pa moyo wake, potsiriza osalandira maliro aulemu, ndithu ine ndikuti munthuyo ngakhale mtayo womwe umpambana kwambiri.

4Mtayo umangopita pachabe nkuloŵa mu mdima, ndipo umakaiŵalika mumdimamo.

5Ngakhale mtayowo sudaone dzuŵa kapena kudziŵa kanthu kalikonse, komabe umapumula kupambana munthu wa moyo wautali uja,

6ngakhale akadakhala ndi moyo zaka zikwi ziŵiri, koma osaona zabwino. Kodi nanga onsewo suja amapita ku malo amodzimodzi?

7Munthu amagwira ntchito zolemetsa kuti apeze chakudya, komabe satha kukhutira kotheratu.

8Nanga munthu wanzeru ali ndi chiyani chimene amapambana nacho chitsiru? Kodi mmphaŵi amene amangodziŵa kukhala bwino pamaso pa anzake, ndiye kuti wapindulapo chiyani?

9Kuli bwino kumangopenya zinthu ndi maso kupambana kumazilakalaka chamumtima. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.

10Chilichonse chimene chilipo adachitchula kale dzina. Za m'mene munthu aliri nzodziŵika, nchomveka kuti sangathe kutsutsana ndi amene ali wamphamvu kupambana iyeyo.

11Mau akachuluka, zopandapake zimachulukanso. Nanga munthu apindulapo chiyani?

12Ndani amadziŵa zomkomera munthu kwenikweni pa nthaŵi yochepa imene munthuyo ali ndi moyo? Moyo wake ndi wa masiku ochepa, ndi wopandapake, umangopitirira ngati mthunzi. Ndani angathe kumufotokozera munthuyo zimene zidzachitike pansi pano iyeyo atafa?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help