1 ndikulemba kalatayi kwa Gayo wokondedwa, amene ndimamkonda kwenikweni.
2Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.
3Ine ndidaakondwa kwambiri pamene abale ena adafika nkumafotokoza za moyo wako m'choona, ndiponso za m'mene umayendera motsata choona.
4Palibe chondikondweretsa kwambiri koposa kumva kuti ana anga akuyenda m'choona.
Ayamika Gayo5Wokondedwa, umatsata chikhulupiriro chako pa zonse zimene umachitira abale, makamaka akakhala alendo.
6Iwo adachitira umboni chikondi chako pamaso pa mpingo. Ndi bwinodi kuti uŵathandize mokondweretsa Mulungu kupitiriza ulendo wao.
7Paja adaanyamuka ulendo wao chifukwa cha dzina la Khristu, osalandira thandizo kwa akunja.
8Tsono ife tiyenera kumaŵathandiza anthu otere, kuti tigwirizane nawo pa ntchito yofalitsa choona.
Za Diotrefe ndi Demetrio9Ndidalembera mpingo mau pang'ono, koma Diotrefe safuna kundimvera. Iye amafuna kukhala mtsogoleri.
10Choncho ndikabwera, ndidzakumbutsa ntchito zimene amachita. Iye amandilalatira ndi mau oipa. Ndipo sachita zokhazi ai, komanso iyeiyeyo amakana kulandira abale, ndipo anthu ofuna kuŵalandira, iye amaŵaletsa, nkumaŵatulutsa mu mpingo.
11Wokondedwa, usamatsanzire zoipa, koma zabwino. Aliyense wochita zabwino, ndi mwana wa Mulungu, koma wochita zoipa, sadaone Mulungu.
12Demetrio anthu onse amamchitira umboni wabwino. Ngakhale choona chomwe chimamchitira umboni. Ifenso tikumchitira umboni, ndipo iweyo ukudziŵa kuti umboni wathu ndi woona.
13Ndinali ndi zambiri zoti ndikuuze, koma sindingakonde kuzilemba m'kalata.
14Ndikuyembekeza kudzakuwona posachedwa. Pamenepo tidzakambirana pakamwa mpakamwa.
15Mtendere ukhale nawe. Abwenzi onse akuti moni. Uperekeko moni kwa abwenzi onse mmodzimmodzi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.