2 Tim. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za makhalidwe a anthu pa masiku otsiriza

1Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta.

2Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu.

3Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino,

4opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu.

5Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.

6Ena mwa iwo amaloŵa m'nyumba za anthu nkumakanyenga akazi ofooka, olemedwa ndi katundu wa machimo. Akazi ameneŵa amatengeka ndi zilakolako zamitundumitundu,

7amangomvera za aliyense, ndipo sangathe konse kudziŵa choona.

8Eks. 7.11 Monga momwe Yane ndi Yambere adaaukira Mose, anthu amenewonso amaukira choona. Nzeru zao nzobuntha, ndipo pa za chikhulupiriro ndi anthu olephera.

9Koma sadzapitirira nazo, pakuti anthu onse adzaona kupusa kwao, monga momwe zidaachitikiranso ndi Yane uja ndi Yambere.

Malangizo otsiriza

10Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga,

11Ntc. 13.14-52; Ntc. 14.1-7; Ntc. 14.8-20mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi.

12Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,

13m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe.

14Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa.

15Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu.

16Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama.

17Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help