1Chauta adauza Mose kuti, “Ulankhule ndi ansembe, ana a Aroni, ndipo uŵauze kuti: Pasapezeke ndi mmodzi yemwe amene adziipitse pokhudza munthu wakufa pakati pa abale ake.
2Koma angathe kukhudza mai wake, bambo wake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi,
3kapena mlongo wake wosakwatiwa amene amakhala pafupi naye, poti chikhalire alibe mwamuna.
4Wansembe asadziipitse pa imfa ya munthu amene wakwatira naye ku banja limodzi.
5Lev. 19.27, 28; Deut. 14.1 Ansembe asamete tsitsi kumutu kwao, kapena kumeta m'mphepete mwa ndevu zao, kapenanso kudzichekacheka pa thupi.
6Akhale oyera pamaso pa Ine Mulungu, ndipo asachititse manyazi dzina langa. Amapereka nsembe zotentha pa moto, chakudya cha Mulungu wao, nchifukwa chake azikhala oyera.
7Asakwatire mkazi wachiwerewere kapena mkazi amene wadziipitsa, ndiponso asakwatire mkazi amene mwamuna wake wamsudzula, pakuti wansembe ndi woyera pamaso pa Mulungu wake.
8Akhale munthu woyera kwa inu, chifukwa amapereka chakudya cha Mulungu wanu. Akhale munthu woyera kwa inu, chifukwa Ine Chauta amene ndimakuyeretsani, ndine woyera.
9Ndipo mwana wamkazi wa wansembe aliyense akadziipitsa pokhala wachiwerewere, amaipitsa bambo wake. Mwanayo ayenera kumtentha pa moto.
10“Munthu amene ali mkulu wa ansembe onse, amene adamdzoza pa mutu ndi mafuta, ndiponso amene adapatulidwa pakumuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake, kapena kung'amba zovala zake kusonyeza kuti ali pamaliro.
11Asakaloŵe kumene kuli munthu wakufa aliyense ndi kudziipitsa, ngakhale mtembo wa bambo wake kapena wa mai wake.
12Asatuluke m'malo oyera kapena kuipitsa malo oyera a Mulungu wake, pakuti mafuta odzozera a Mulungu wake amene adamdzoza nawo ali pa iye. Ine ndine Chauta.
13Ndipo akwatire mnamwali wosadziŵa mwamuna,
14asakwatire mkazi wamasiye kapena mkazi wosudzulidwa, kapenanso mkazi wachiwerewere. Koma akwatire mnamwali wosadziŵa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake, amene sanadziŵeko mwamuna,
15kuti asaloŵetse mtundu wosayera pakati pa ana ake, pakuti Ine ndine Chauta amene ndinamuyeretsa.”
16Chauta adauza Mose kuti,
17“Uza Aroni kuti munthu aliyense mwa zidzukulu zake pa mibadwo yonse, amene ali ndi chilema, asabwere kudzapereka nsembe kwa Mulungu wake.
18Munthu aliyense wachilema sayenera kusendera pafupi, monga munthu wakhungu kapena wopunduka miyendo, munthu wopunduka nkhope kapena wokhala ndi chiwalo china chachitali dziŵi,
19munthu wa phazi lopunduka kapena wa dzanja lopunduka,
20munthu wanundu kapena kafupidolo, munthu wa maso opunduka, munthu wa nthenda yonyerenyesa, kapena wamphere, kapenanso wotswanyika mavalo.
21Mwa zidzukulu za wansembe Aroni pasadzapezeke munthu ndi mmodzi yemwe wokhala ndi chilema, amene adzapereke nsembe zopsereza kwa Chauta. Popeza kuti ali ndi chilema, sayenera kusendera pafupi ndi guwa kuti akapereke zakudya za Mulungu wake.
22Koma angathe kudya chakudya choperekedwa kwa Mulungu wake, buledi wopatulika kopambana uja, pamodzi ndi zotsalira zopatulika za nsembe.
23Koma asadzabwere pafupi ndi nsalu yochinga, kapena kuyandikira guwa, chifukwa ali ndi chilema, kuwopa kuti angadzaipitse malo anga oyera. Pakuti Ine ndine Chauta amene ndidapatula malo amenewo.”
24Zimenezi ndizo zimene Mose adauza Aroni ndi ana ake aamuna ndiponso Aisraele onse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.