1Pambuyo pake ndidaona Kumwamba chizindikiro china chachikulu ndi chododometsa: angelo asanu ndi aŵiri okhala ndi miliri isanu ndi iŵiri. Miliriyo ndi yotsiriza, pakuti ukali wa Mulungu uthera pa imeneyi.
2Kenaka ndidaona ngati nyanja ya galasi losanganiza ndi moto. Ndidaonanso anthu amene adapambana chilombo chija, fano lake lija, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo adaaimirira pamphepete pa nyanja yagalasi ija, m'manjamu ali ndi azeze oŵapatsa Mulungu.
3Eks. 15.1Ankaimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa uja. Mau ake ankati,
“Ambuye, Mulungu Mphambe,
ntchito zanu nzazikulu ndi zododometsa.
Inu, Mfumu ya anthu a mitundu yonse,
njira zanu nzolungama ndi zoona.
4 Yer. 10.7; Mas. 86.9 Ambuye, ndani angapande kukuwopani
ndi kutamanda dzina lanu?
Paja ndinu nokha oyera.
Anthu a mitundu yonse adzabwera nkudzakupembedzani,
popeza kuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”
5 Eks. 38.21 Zitatha izi, ndidaona Kumwamba Malo Opatulika a m'katikati mwa Chihema cha Umboni atatsekuka.
6Tsono mudatuluka angelo asanu ndi aŵiri aja okhala ndi miliri isanu ndi iŵiri, atavala nsalu zoyera zambee, nkumangira malamba agolide pa chifuwa.
7Chimodzi mwa Zamoyo zinai zija chidapereka mikhate isanu ndi iŵiri yagolide kwa angelo asanu ndi aŵiri aja. Mikhateyo inali yodzaza ndi ukali wa Mulungu amene ali ndi moyo mpaka muyaya.
8Eks. 40.34; 1Maf. 8.10, 11; 2Mbi. 5.13, 14; Yes. 6.4M'malo Opatulika aja mudaadzaza utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu zake. Motero panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kuloŵa m'Malo Opatulikawo mpaka itatha miliri isanu ndi iŵiri ija imene anali nayo angelo asanu ndi aŵiri aja.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.