Gen. 42 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Abale ake a Yosefe afika ku Ejipito kudzagula tirigu

1Yakobe atamva kuti ku Ejipito ndiko kuli tirigu, adafunsa ana ake kuti, “Chifukwa chiyani mukungokhala osachitapo kanthu?

2Ntc. 7.12 Ndikumva kuti ku Ejipito aliko tirigu. Pitaniko kumeneko, mukatigulireko ife, kuti tingafe ndi njala.”

3Motero abale ake a Yosefe khumi adanyamuka kupita ku Ejipito kukagula tirigu.

4Yakobe sadamtume nawo Benjamini, mng'ono wake weniweni wa Yosefe uja, chifukwa ankaopa kuti angapeze tsoka.

5Ana a Israelewo adapita ku Ejipito kukagula chakudya pamodzi ndi anthu ena onse, chifukwa chakuti ku dziko la Kanani kunali njala.

6Tsono popeza kuti Yosefe anali nduna yaikulu yolamulira dziko lonse la Ejipito, ndiye amene ankagulitsa tirigu kwa anthu ochokera ku mbali zonse za dziko. Choncho abale ake a Yosefe nawonso adabwera, ndipo adamgwadira Yosefeyo, namuŵeramira.

7Yosefe ataŵaona abale akewo, adaŵazindikira, koma adangochita ngati sadaŵadziŵe. Adayamba kuŵalankhula mozaza, naŵafunsa kuti, “Kodi inu mukuchokera kuti?” Iwo adayankha kuti, “Tikuchokera ku Kanani, tadzagula chakudya kuno.”

8Yosefe adaŵazindikira abale ake aja, koma iwo sadamzindikire.

9Gen. 37.5-10 Adakumbukira maloto aja onena za iwo, ndipo adati, “Ndinu anthu ozonda dziko. Mwabwera kuno kudzazonda kuti muwone ngati dziko lathu ndi lofooka.”

10Iwo aja adayankha kuti, “Iyai mbuyathu, ife atumiki anu tabwera kuti tidzagule chakudya basi.

11Tonsefe tili pachibale. Sindife azondi, mbuyathu, koma ndife anthu okhulupirika ndithu.”

12Yosefe adati, “Iyai. Inu mwabwera kudzazonda dziko lathu kuti muwone ngati ndi lofooka.”

13Tsono iwowo adati, “Mbuyathu, ife tinalipo ana aamuna khumi ndi aŵiri pachibale pathu, bambo wathu mmodzi, ku dziko la kwathu ku Kanani. Wamng'ono ali ndi bambo wathu, ndipo wina adamwalira.”

14Koma Yosefe adaŵayankha kuti, “Paja ndanena kale kuti ndinu azondi basi.

15Tsono ndikuyesani motere; ndikulumbira kuti pali Farao! Inuyo simuchoka, mpaka mng'ono wanuyo atabwera kuno.

16Tumani mmodzi mwa inu kuti apite akamtenge. Ena nonse otsalanu mukhale m'ndende ndithu, mpaka mau anuŵa atsimikizike, tiwone ngati mukunena zoona. Apo ai, ndithu pali Farao, inuyo ndinu azondi basi.”

17Atanena mau ameneŵa, adakaŵatsekera m'ndende masiku atatu.

18Patapita masiku atatu, adaŵauza kuti, “Ine ndimaopa Mulungu. Choncho ndikupatsani mwai woupulumutsa moyo wanu mukachita izi.

19Ngati ndinu okhulupirika, mmodzi yekha atsalire m'ndendemu, ena nonsenu mungathe kupita, kuti mukapereke tirigu mwagulayu ku banja la kwanu kuli njalako.

20Mng'ono wanuyo mukabwere naye kuno, kutsimikiza kuti mukunenadi zoona, ndipo simudzaphedwa.” Iwo aja adavomereza zimenezo.

21Ndipo adayamba kuuzana kuti, “Ndithu, ife tidalakwa pamene mng'ono wathu ankatipempha kuti timchitire chifundo, koma ife osamumvera konse chifundo. Nchifukwa chake tili m'mavuto tsopano lino.”

22Gen. 37.21, 22 Apo Rubeni adati, “Ine paja ndinkakuuzani kuti mnyamatuyu musamchite kanthu, inu osandimvera. Mwaonatu, tsopano tikulandira malipiro a imfa yake ija.”

23Yosefe anali kumva zonse zimene ankakambiranazo, koma iwowo sadadziŵe, chifukwa choti ankalankhula naye kudzera mwa womasulira.

24Tsono Yosefe adapita payekha kukalira misozi. Kenaka adabwerako nayambanso kulankhula nawo. Adapatulapo Simeoni, nammanga pomwepo iwowo akuwona.

Abale a Yosefe abwerera ku Kanani

25Tsono Yosefe adalamula kuti matumba ao adzazidwe ndi tirigu, ndipo kuti ndalama za aliyense ziikidwe m'thumba mwake momwemo. Adalamulanso kuti aŵapatse kamba wapaulendo. Antchito a Yosefe adachitadi zonsezo.

26Abale akewo adasenzetsa abulu ao matumba a tirigu uja adagulayu, ndipo adanyamuka ulendo.

27Atafika pa chigono, mmodzi mwa iwo adamasula thumba lake kuti atengeko chakudya chodyetsa bulu wake. Atamasula, adangoona kuti pakamwa pa thumbalo pali ndalama.

28Adaitana abale ake naŵauza kuti, “Ha, wandibwezera ndalama zanga. Si izi zili m'thumbazi.” Pamenepo onsewo mitima yao idangoti phwii! Adachita mantha kwambiri nati, “Mulungu watichita zotani ife?”

29Atafika kwa bambo wao Yakobe, adamsimbira zonse zimene zidaŵagwera, adati,

30“Nduna yaikulu ya dzikolo idatilankhula mozaza, kuti ati ndife ozonda dziko laolo.

31Ife tidamuuza munthuyo kuti, ‘Ndife anthu okhulupirika, osati azondi.

32Ife tonse tinalipo ana aamuna khumi ndi aŵiri, koma mmodzi adamwalira, ndipo wamng'ono ali ndi bambo wathu ku Kanani.’

33Pamenepo iyeyo adati, ‘Kuti ndidziŵe kuti ndinu anthu okhulupirika, mmodzi mwa inu atsale ndi ine kuno, koma ena nonsenu mutenge tirigu, mupite naye ku banja la kwanu kuli njalako.

34Ndipo mbale wanu wamng'onoyo mudzabwere naye kuno. Pamenepo ndiye ndidzadziŵe kuti sindinu azondi, koma ndinu okhulupirika. Mbale wanuyo ndidzambwezera kwa inu. Mukadzatero mungathe kumadzachitabe malonda m'dziko muno.’ ”

35Atamasula matumba ao, aliyense adapeza kuti chikwama cha ndalama chinali momwe m'thumbamo. Ataona ndalamazo, iwowo pamodzi ndi bambo wao yemweyo adachita mantha kwambiri.

36Tsono Yakobe bambo wao adaŵauza kuti, “Mwandilanda ana anga. Yosefe adapita, ndipo nayenso Simeoni wapita, tsopano mufuna kutenganso Benjamini, zonse zandigwera ine!”

37Rubeni adauza atate ake kuti, “Mungathe kudzapha ana anga aŵiri, ngati Benjamini sindidzabwera naye kwa inu. Mundipatse kuti ndimsamale ndine, ndipo ndidzabwera naye.”

38Koma Yakobe adati, “Mwana wangayu sangapite nanu ai, paja mbale wake adamwalira, ndipo ndi yekhayu watsala. Mwina mwake angathe kuphedwa pa njira, ndipo ine m'mene ndakalambiramu, chisoni chotere chidzangonditsiriza.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help