1Ili ndi buku losimba za Tobiti, mwana wa Tobiele, mwana wa Ananiyele, mwana wa Aduwele, mwana wa Gabaele, mwana wa Rafaele, mwana wa Raguele, wa banja la Asiyele ndi wa fuko la Nafutali.
2 ndinkagulitsa chachikhumi chachiŵiri cha zinthu zanga, ndalama zake nkukazitula ku ntchito za ku Yerusalemu.
8Chachikhumi chachitatu ndinkachipereka kwa ana ndi kwa akazi amasiye, ndiponso kwa alendo amene ankakhala pakati pa Aisraele. Ndinkagaŵa zoperekazo chaka chachitatu chilichonse. Pakudya zimenezo tinkatsata malamulo a Mose ndi malangizo amene Debora, amai a Ananiyele, kholo lathu, adandisiyira, poti ine bambo wanga anali atamwalira, kundisiya wamasiye.
9Nditakula, ndidakwatira mkazi wa mtundu wanga, dzina lake Hana. Adandibalira mwana wamwamuna amene ndidamutcha dzina loti Tobiyasi.
Kukhulupirika kwa Tobiti ku dziko laukapolo10Titatengedwa ukapolo kupita ku Asiriya, tidafika ku Ninive. Abale anga onse ndi onse a mtundu wanga ankadya chakudya cha anthu akunjawo.
11Koma ine ndekha sindinkadya nawo chakudyacho.
12Tsono popeza kuti ndinali wokhulupirika kwa Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse,
13Wopambanazonse adandipezetsa kuyanja pamaso pa mfumu Salimanezere. Motero iye adandipatsa udindo wogula zonse zimene iyeyo ankafuna.
14Ndinkapitapita ku Mediya, ndipo kumeneko ndinkamugulira zonse mpaka nthaŵi ya kufa kwake. Tsiku lina Gabaele, mbale wa Gabriyasi, wa ku Ragesi, ku Mediya komweko, ndidamusungiza matumba a ndalama zasiliva zopitirira makilogramu 340.
15Salimanezere atafa, ndipo mwana wake Senakeribu ataloŵa ufumu, njira zopita ku Mediya zidatsekeka, choncho sindidathe kupitakonso.
16Pa nthaŵi ya Salimanezere, ndinkapereka ndalama zothandiza abale anga, anthu a mtundu wanga. Anthu anjala ndinkaŵapatsa chakudya, ndipo anthu ausiŵa ndinkaŵapatsa zovala.
17Yob. 31.16-20Tsono ndikaona kuti mmodzi mwa abale anga wafa, ndipo mtembo wake angouti chi kuseri kwa linga la Ninive, ndinkauika m'manda.
18Ndinkaŵaikanso, koma mobisa, onse amene Senakeribu ankaŵapha, pa nthaŵi imene iyeyo ankathaŵa ku Yudeya. Paja nthaŵi imeneyo Mulungu, Mfumu ya Kumwamba, adaamulanga chifukwa cha mau ake achipongwe omnyoza Iyeyo. Motero Senakeribu adaapsa mtima, napha Aisraele ambiri. Mitembo yao ine ndinkaiba nkumaikwirira. Pamene Senakeribu adaifunafuna, sadaipeze.
19Tsono munthu wina wa ku Ninive ndiye adapita kukaulula kwa mfumu kuti ndine amene ndinkaika malirowo mobisa. Ndiye ine nditadziŵa kuti mfumu yamva zonse za ine, ndipo ikundifunafuna kuti indiphe, ndidachita mantha nkuthaŵa kukabisala.
20Adandilanda katundu wanga yense, osandisiyira kanthu, ndipo zonse adakaziika m'nyumba ya chuma cha mfumu. Ndidangotsala ndi mkazi wanga Hana, ndi mwana wanga Tobiyasi.
21Patangopita pafupi masiku makumi anai, mfumu Senakeribu adaphedwa ndi ana ake aŵiri, iwowo nkuthaŵira ku mapiri a Ararati. Asaradoni, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Adasankha Ahikare, mwana wa mbale wanga Anaele, kuti akhale nduna yazachuma m'dzikolo, ndipo adampatsa udindo woyendetsa zinthu zonse.
22Tsono Ahikare adandinenerako kwa mfumu, ndipo ndidabwerera ku Ninive. Pa nthaŵi ya Senakeribu ija Ahikare anali kapitao wamkulu woyang'anira zopereka vinyo, analinso mlonda wosunga chidindo chosindikizira cha mfumu. Ankayang'anira zonse za boma, ndipo anali msungachuma wa mfumu ya ku Asiriya. Tsono Asaradoni adamsunga m'maudindo omwewo. Ahikareyo anali wa m'banja langa, mwana wa mbale wanga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.