1Mngelo wa Chauta adapita ku Bokimu kuchokera ku Giligala. Ndipo adauza Aisraele kuti, “Ndidakutulutsani ku Ejipito ndi kukuloŵetsani m'dziko limene ndidalumbira kuti ndidzapatsa makolo anu. Ndidati, ‘Ineyo sindidzaswa konse chipangano changa ndi inu.
2Eks. 34.12, 13; Deut. 7.2-5 Tsono inuyo musadzachite chipangano ndi nzika za dziko lino. Mudzaphwanye maguwa ao onse.’ Koma inu simudamvere lamulo langa. Zimenezi mwachitiranji?
3Choncho tsopano ndikukuuzani kuti sindidzapirikitsa nzikazo pamene inu mukufika. Koma zidzasanduka adani anu, ndipo milungu yao idzakhala ngati msampha kwa inu.”
4Pamene mngelo wa Chauta adalankhula mau ameneŵa kwa Aisraele onse, anthuwo adayamba kufuula ndi kulira.
5Malowo adaŵatcha Bokimu (ndiye kuti olira), ndipo adapereka nsembe kwa Chauta pomwepo.
Imfa ya Yoswa.6Yoswa atauza anthu kuti apite, Aisraele adapita aliyense ku dera la choloŵa chake, kuti akhazikike konko.
7Anthuwo ankatumikira Chauta masiku onse pamene Yoswa anali moyo, ndipo ngakhale atafa Yoswayo, anthu ankatumikirabe Chauta nthaŵi yonse ya moyo wa akuluakulu otsatira Yoswa aja, amene anali ataona ntchito zazikulu zimene Chauta adachitira Aisraele.
8Yoswa, mwana wa Nuni, mtumiki wa Chauta, adamwalira ali ndi zaka 110.
9Yos. 19.49, 50 Ndipo adamuika m'dziko lake limene adalandira ngati choloŵa chake ku Timnati-Heresi m'dziko lamapiri la Efuremu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.
10Mbadwo wonsewo udafa. Tsono padauka mbadwo wina pambuyo pake umene sudadziŵe Chauta kapenanso ntchito zija Chauta adaachitira Aisraelezi.
Aisraele aleka kupembedza Chauta.11Aisraele adayamba kuchita zinthu zoipira Chauta nkumatumikira Baala.
12Iwo adasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao, amene adaŵatulutsa m'dziko la Aejipito. Adatsata milungu ina ya anthu oŵazungulira, ndipo ankaipembedza. Pakutero adakwiyitsa Chauta.
13Iwo adasiya Chauta, nayamba kutumikira Abaala ndi Aasitaroti.
14Choncho Chauta adaŵapsera mtima Aisraelewo, ndipo adaŵapereka m'manja mwa anthu ofunkha amene adasakaza zinthu zao. Ndipo adalola kuti adani ao oŵazungulira aŵagonjetse, kotero kuti sadathenso kulimbana nawo adaniwo.
15Ankati akapita kukamenya nkhondo, Chauta ankalimbana nawo iwowo, monga momwe Iye adaanenera molumbira kuti adzaterodi. Choncho Aisraelewo anali pa mavuto oopsa.
16Tsono Chauta adautsa atsogoleri amene adaŵapulumutsa Aisraele kwa anthu osakaza aja amene ankaŵaonongera zinthu zao.
17Komabe iwo sadaŵamvere atsogoleri aowo, pakuti ankapembedza milungu ina namaigwadira. Makolo ao ankamvera malamulo a Chauta. Koma mbadwo watsopanowu udaleka mwamsanga kutsata njira imeneyo.
18Nthaŵi zonse Chauta akaŵautsira mtsogoleri, Chauta ankakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankaŵapulumutsa Aisraele kwa adani ao nthaŵi zonse mtsogoleriyo ali moyo. Zoonadi Chauta ankaŵamvera chisoni anthuwo, iwowo akamamdandaulira chifukwa cha amene ankaŵazunza ndi kuŵasautsa.
19Koma nthaŵi zonse mtsogoleri akafa, anthuwo ankayambanso kuchita zoipa, nkusanduka oipa kupambana makolo ao, namatsata milungu ina, kumaitumikira ndi kumaigwadira. Sankaleka kuchita zimene adaazoloŵera ndiponso sankaleka kukhala ouma mitu.
20Choncho Chauta adaŵapsera mtima Aisraele, nati, “Anthuŵa aphwanya chipangano changa chimene ndidaakhazikitsira makolo ao. Ndiye popeza kuti sadamvere mau anga,
21kuyambira tsopano sindidzapirikitsanso mtundu wina uliwonse umene Yoswa adasiya pamene ankamwalira.
22Motero ndidzaŵayesa Aisraele kuti ndiwone ngati adzasamala zoyenda m'njira ya Ine Chauta, monga adachitira makolo ao, kapena ai.”
23Choncho Chauta adaisiya mitundu imeneyo osaipirikitsa nthaŵi yomweyo, ndipo sadaipereke m'manja mwa Yoswa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.